Yohane 11:43-44

Yohane 11:43-44 CCL

Yesu atanena izi, Iye anayitana ndi mawu ofuwula kuti, “Lazaro, tuluka!” Munthu womwalirayo anatuluka, womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za ku manda, ndi nkhope yake yokulungidwa nsalu. Yesu anawawuza kuti, “Mʼmasuleni, ndipo muloleni apite.”