Luka 21:25-27

Luka 21:25-27 CCL

“Padzakhala zizindikiro zodabwitsa pa dzuwa, mwezi ndi nyenyezi. Pa dziko lapansi, mitundu ya anthu idzakhala mʼmasautso ndipo idzathedwa nzeru pakumva mkokomo ndi mafunde a mʼnyanja. Anthu adzakomoka chifukwa cha mantha, akadzamva za zimene zikubwera pa dziko lapansi, pakuti zinthu zamlengalenga zidzagwedezeka. Nthawi imeneyo adzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu.