Gen. 6:1-4

Gen. 6:1-4 BLY-DC

Nthaŵi imeneyo anthu anali atayamba kuchuluka pa dziko lonse lapansi, ndipo adabereka ana aakazi. Ana aamuna a Mulungu adaona kuti ana aakazi a anthu anali okongola, nayamba kukwatira amene ankaŵakonda. Tsono Chauta adati, “Sindidzalola anthu kukhala ndi moyo mpaka muyaya, popeza kuti munthu ndi thupi limene limafa. Kuyambira tsopano adzangokhala zaka 120.” Pa masiku amenewo, ngakhale pambuyo pakenso, panali anthu amphamvu ataliatali pa dziko lapansi. Anthu ameneŵa ndi amene ankabadwa mwa akazi omwe adaakwatiwa ndi ana a Mulungu aja. Iwoŵa anali ngwazi zomveka ndiponso anthu otchuka pa masiku akalewo.

Чытаць Gen. 6