1
Yohane 8:12
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Yesu atayankhulanso kwa anthu, anati, “Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi. Aliyense amene anditsata Ine sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuwala kotsogolera anthu ku moyo.”
Compare
Explore Yohane 8:12
2
Yohane 8:32
Tsono mudzadziwa choonadi, ndipo choonadicho chidzakumasulani.”
Explore Yohane 8:32
3
Yohane 8:31
Kwa Ayuda amene anamukhulupirira, Yesu anati, “Ngati inu mutsatira chiphunzitso changa, ndithu ndinu ophunzira anga.
Explore Yohane 8:31
4
Yohane 8:36
Nʼchifukwa chake ngati Mwana adzakumasulani, mudzakhala mfulu ndithu.
Explore Yohane 8:36
5
Yohane 8:7
Pamene iwo anapitirira kumufunsa, Iye anaweramuka ndipo anawawuza kuti, “Ngati wina wa inu alipo wopanda tchimo, ayambe iyeyo kumugenda ndi miyala mkaziyu.”
Explore Yohane 8:7
6
Yohane 8:34
Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimolo.
Explore Yohane 8:34
7
Yohane 8:10-11
Yesu anaweramuka ndipo anamufunsa iye kuti, “Akuluakulu aja ali kuti? Kodi palibe amene wakutsutsa?” Iye anati, “Ambuye, palibe ndi mmodzi yemwe.” “Inenso sindikukutsutsa iwe. Pita kuyambira tsopano usakachimwenso.”
Explore Yohane 8:10-11
Home
Bible
Plans
Videos