ndipo ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, ndipo ndidzapatsa mbeu zako maiko onsewa; m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa; chifukwa kuti Abrahamu anamvera mau anga, nasunga chilangizo changa, ndi maweruziro anga, ndi malemba anga ndi malamulo anga.