1
GENESIS 32:28
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.
Compare
Explore GENESIS 32:28
2
GENESIS 32:26
Ndipo iye anati Ndileke ndimuke, chifukwa kulinkucha. Ndipo Yakobo anati, Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine.
Explore GENESIS 32:26
3
GENESIS 32:24
Ndipo anatsala Yakobo yekha; ndipo analimbana naye munthu kufikira mbandakucha.
Explore GENESIS 32:24
4
GENESIS 32:30
Ndipo Yakobo anatcha dzina la malo amenewo, Penuwele: chifukwa ndaonana ndi Mulungu nkhope ndi nkhope, ndipo wapulumuka moyo wanga.
Explore GENESIS 32:30
5
GENESIS 32:25
Ndipo pamene anaona kuti sanamgonjetsa, anakhudza nsukunyu ya ntchafu yake; ndipo nsukunyu ya ntchafu yake ya Yakobo inaguluka, pakulimbana naye.
Explore GENESIS 32:25
6
GENESIS 32:27
Ndipo iye anati kwa Yakobo, Dzina lako ndani? Nati iye, Yakobo.
Explore GENESIS 32:27
7
GENESIS 32:29
Yakobo ndipo anafunsa iye, nati, Undiuze ine dzina lako. Ndipo iye anati, Undifunsa dzina chifukwa ninji? Ndipo anamdalitsa iye pamenepo.
Explore GENESIS 32:29
8
GENESIS 32:10
sindiyenera zazing'ono za zifundo zonse, ndi zoona zonse, zimene mwamchitira kapolo wanu: chifukwa ndindodo yanga ndinaoloka pa Yordani uyu; ndipo tsopano ndili makamu awiri.
Explore GENESIS 32:10
9
GENESIS 32:32
Chifukwa chake ana a Israele samadya mtsempha ya thako ili pa nsukunyu ya ntchafu kufikira lero: chifukwa anakhudza nsukunyu ya ntchafu ya Yakobo pa mtsempha ya thako.
Explore GENESIS 32:32
10
GENESIS 32:9
Ndipo Yakobo anati, Mulungu wa atate wanga Abrahamu, Mulungu wa atate wanga Isaki, Yehova, amene munati kwa ine, Bwera ku dziko lako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakuchitira iwe bwino
Explore GENESIS 32:9
11
GENESIS 32:11
Mundipulumutsetu ine m'dzanja la mkulu wanga, m'dzanja la Esau; chifukwa ine ndimuopa iye, kapena adzadza kudzandikantha ine, ndi amai pamodzi ndi ana.
Explore GENESIS 32:11
Home
Bible
Plans
Videos