Ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo nayang'ana kumwamba, nadalitsa, nagawa mikate; napatsa kwa ophunzira kuti apereke kwa iwo; ndi nsomba ziwiri anagawira onsewo. Ndipo anadya iwo onse, nakhuta. Ndipo anatola makombo, madengu khumi ndi iwiri, ndiponso za nsomba.