Ndipo uganiza kodi, munthu iwe, amene umaweruza iwo akuchita zotere, ndipo uzichitanso iwe mwini, kuti udzapulumuka pa mlandu wa Mulungu? Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape?