1
AROMA 3:23-24
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu; ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi chisomo chake, mwa chiombolo cha mwa Khristu Yesu
Compare
Explore AROMA 3:23-24
2
AROMA 3:22
ndicho chilungamo cha Mulungu chimene chichokera mwa chikhulupiriro cha pa Yesu Khristu kwa onse amene akhulupirira; pakuti palibe kusiyana
Explore AROMA 3:22
3
AROMA 3:25-26
amene Mulungu anamuika poyera akhale chotetezera mwa chikhulupiriro cha m'mwazi wake, kuti aonetse chilungamo chake, popeza Mulungu m'kulekerera kwake analekerera machimo ochitidwa kale lomwe; kuti aonetse chilungamo chake m'nyengo yatsopano; kuti Iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu.
Explore AROMA 3:25-26
4
AROMA 3:20
chifukwa kuti pamaso pake palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo; pakuti uchimo udziwika ndi lamulo.
Explore AROMA 3:20
5
AROMA 3:10-12
monga kwalembedwa, Palibe mmodzi wolungama, inde palibe mmodzi; palibe mmodzi wakudziwitsa, palibe mmodzi wakulondola Mulungu; onsewa apatuka, pamodzi akhala opanda pake; palibe mmodzi wakuchita zabwino, inde, palibe mmodzi ndithu.
Explore AROMA 3:10-12
6
AROMA 3:28
Pakuti timuyesa munthu wolungama chifukwa cha chikhulupiriro, wopanda ntchito za lamulo.
Explore AROMA 3:28
7
AROMA 3:4
Msatero ai. Koma Mulungu akhale woona, ndimo anthu onse akhale onama; monga kwalembedwa, Kuti Inu mukayesedwe wolungama m'maneno anu, ndi kuti mukalakike m'mene muweruzidwa.
Explore AROMA 3:4
Home
Bible
Plans
Videos