1
AROMA 4:20-21
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
ndipo poyang'anira lonjezo la Mulungu sanagwedezeka chifukwa cha kusakhulupirira, koma analimbika m'chikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemu, nakhazikikanso mumtima kuti, chimene Iye analonjeza, anali nayonso mphamvu yakuchichita.
Compare
Explore AROMA 4:20-21
2
AROMA 4:17
monga kwalembedwa: Ndinakukhazika iwe kholo la mitundu yambiri ya anthu pamaso pa Mulungu amene iye anamkhulupirira, amene apatsa akufa moyo, ndi kuitana zinthu zoti palibe, monga ngati zilipo.
Explore AROMA 4:17
3
AROMA 4:25
amene anaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu, naukitsidwa chifukwa cha kutiyesa ife olungama.
Explore AROMA 4:25
4
AROMA 4:18
Amene anakhulupirira nayembekeza zosayembekezeka, kuti iye akakhale kholo la mitundu yambiri ya anthu, monga mwa chonenedwachi, Mbeu yako idzakhala yotere.
Explore AROMA 4:18
5
AROMA 4:16
Chifukwa chake chilungamo chichokera m'chikhulupiriro, kuti chikhale monga mwa chisomo; kuti lonjezo likhale lokhazikika kwa mbeu zonse; si kwa iwo a chilamulo okhaokha, koma kwa iwonso a chikhulupiriro cha Abrahamu; ndiye kholo la ife tonse
Explore AROMA 4:16
6
AROMA 4:7-8
ndi kuti, Odala iwo amene akhululukidwa kusaweruzika kwao, nakwiriridwa machimo ao. Wodala munthu amene Mulungu samwerengera uchimo.
Explore AROMA 4:7-8
7
AROMA 4:3
Pakuti lembo litani? Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo chinawerengedwa kwa iye chilungamo.
Explore AROMA 4:3
Home
Bible
Plans
Videos