Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu; amene ife tikhoza kulowa naye ndi chikhulupiriro m'chisomo ichi m'mene tilikuimamo; ndipo tikondwera m'chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu.