1
AROMA 6:23
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
Compare
Explore AROMA 6:23
2
AROMA 6:14
Pakuti uchimo sudzachita ufumu pa inu; popeza simuli a lamulo koma a chisomo.
Explore AROMA 6:14
3
AROMA 6:4
Chifukwa chake tinaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Khristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m'moyo watsopano.
Explore AROMA 6:4
4
AROMA 6:13
ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.
Explore AROMA 6:13
5
AROMA 6:6
podziwa ichi, kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye, kuti thupilo la uchimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a uchimo
Explore AROMA 6:6
6
AROMA 6:11
Chotero inunso mudziwerengere inu nokha ofafa ku uchimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.
Explore AROMA 6:11
7
AROMA 6:1-2
Chifukwa chake tidzatani? Tidzakhalabe m'uchimo kodi, kuti chisomo chichuluke? Msatero ai. Ife amene tili akufa ku uchimo, tidzakhala bwanji chikhalire m'menemo?
Explore AROMA 6:1-2
8
AROMA 6:16
Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye; kapena a uchimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kuchilungamo?
Explore AROMA 6:16
9
AROMA 6:17-18
Koma ayamikidwe Mulungu, kuti ngakhale mudakhala akapolo a uchimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe aja a chiphunzitso chimene munaperekedweracho; ndipo pamene munamasulidwa kuuchimo, munakhala akapolo a chilungamo.
Explore AROMA 6:17-18
Home
Bible
Plans
Videos