GENESIS 19
19
Chionongeko cha Sodomu ndi Gomora
1Ndipo anadza ku Sodomu madzulo amithenga awiri; ndipo Loti anakhala pa chipata cha Sodomu, ndipo Loti anaona iwo, nauka kuti akakomane nao, ndipo anaweramitsa pansi nkhope yake. 2#Luk. 24.29; Aheb. 13.2Ndipo anati, Taonanitu, Ambuye anga, tembenukanitu, kulowa m'nyumba mwa kapolo wanu, mugone usiku wonse, mutsuke mapazi anu, ndipo mudzalawira m'mawa kunka ulendo wanu. Ndipo anati, Iai; koma tigone m'khwalalamu usiku wonse. 3Ndipo anawaumiriza iwo ndithu: ndipo anapatukira kwa iye, nalowa m'nyumba mwake; ndipo anawakonzera iwo madyerero, naphika mikate yopanda chotupitsa, ndipo anadya. 4Koma asanagone, anthu a m'mzindamo anthu a Sodomu, anazinga nyumba, anyamata ndi okalamba, anthu onse a m'mbali zonse; 5#Ower. 19.22; Aro. 1.24ndipo anamuitana Loti, nati kwa iye, Ali kuti anthu amene anadza kwa iwe madzulo ano, utitulutsire iwo kuti tiwadziwe. 6Ndipo Loti anatulukira kwa iwo pakhomo, natseka chambuyo pakhomo pake. 7Ndipo anati, Abale anga, musachitetu koipa kotere. 8Taonanitu, ndili ndi ana aakazi awiri, amene sanadziwe mwamuna; ndiwatulutsire iwo kwa inu, muchite nao chomwe chikomera inu; koma anthu awa musawachitire iwo kanthu; chifukwa kuti anadza iwo pansi pa mthunzi wa tsindwi langa. 9#Eks. 2.14Ndipo anati iwo, Baima; natinso, Uyu anadza kuno kukhala ngati mlendo, ndipo afuna kutilamulira; tsopano tidzakuchitira iwe koipa koposa iwo. Ndipo iwo anamkakamiza munthuyo Loti ndithu, nayandikira kuti aswe chitseko. 10Koma anthu aja anatulutsa dzanja lao, namlowetsa Loti momwe anali iwo m'nyumba, natseka pakhomo. 11#2Maf. 6.18Ndipo anachititsa khungu m'maso mwa anthu amene anali pakhomo pa nyumba, aang'ono ndi aakulu, ndipo anavutika kufufuza pakhomo. 12Ndipo anthu aja anati kwa Loti, Kodi muli nao ena pano? Mkamwini, ndi ana ako aamuna, ndi ana ako aakazi, ndi onse ali nao m'mzinda muno, utuluke nao m'malo muno: 13popeza ife tidzaononga malo ano, chifukwa kulira kwao kwakula pamaso pa Yehova, ndipo Yehova anatitumiza ife kuti tiuononge. 14#Yer. 51.6Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene amayenera kukwatira ana ake aakazi, nati, Taukani, tulukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mzindawu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka. 15Pamene kunacha, amithengawo anafulumiza Loti, nati, Uka, tenga mkazi wako, ndi ana ako aakazi awiri amene ali kunowa, kuti munganyeke m'mphulupulu ya mzinda. 16Koma anachedwa; ndipo anthuwo anamgwira dzanja lake, ndi dzanja la mkazi wake ndi dzanja la ana ake aakazi awiri; chifukwa cha kumchitira chifundo Yehova; ndipo anamtulutsa iye, namuika kunja kwa mzinda. 17#Mat. 24.16-18Ndipo panali pamene anawatulutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa paliponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke. 18Ndipo Loti anati kwa iwo, Iaitu, mfumu; 19taonanitu, kapolo wanu anapeza ufulu pamaso panu, ndipo munakuza chifundo chanu, chimene munandichitira ine, pakupulumutsa moyo wanga; ine sindikhoza kuthawira kuphiri kuti chingandipeze ine choipacho ndingafe; 20taonanitu, mzinda uwu uli pafupi pothawirapo, ndipo uli waung'ono; ndithawiretu kumeneko, suli waung'ono nanga? Ndipo ndidzakhala ndi moyo. 21Ndipo anati kwa iye, Taona, ndikuvomereza iwe pamenepanso kuti sindidzaononga mzinda uwu umene wandiuza. 22Fulumira, thawira kumeneko; pakuti sindithai kuchita kanthu usadafike kumeneko. Chifukwa chake anatcha dzina la mzindawo Zowari. 23Ndipo dzuwa lidakwera padziko pamene Loti anafika ku Zowari. 24#Yer. 50.40; Amo. 4.11; Luk. 17.29Ndipo Yehova anavumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulufure ndi moto kutuluka kwa Mulungu kumwamba; 25ndipo anaononga mizindayo, ndi chigwa chonse, ndi onse akukhala m'mizindamo, ndi zimene zimera panthaka. 26#Luk. 17.32Koma mkazi wake anacheuka ali pambuyo pake pa Loti, nasanduka mwala wamchere. 27Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa kunka kumalo kumene anaima pamaso pa Yehova: 28ndipo anayang'anira ku Sodomu ndi ku Gomora ndi ku dziko lonse la chigwa, ndipo anapenya, taonanitu, utsi wa dzikolo unakwera, monga utsi wa ng'anjo.
29 #
Gen. 8.1
Ndipo panali pamene Mulungu anaononga mizinda ya m'chigwa, Mulungu anakumbukira Abrahamu, natulutsa Loti pakati pa chionongeko, pamene anaononga mizinda m'mene anakhalamo Loti.
Gwero la Amoni ndi Mowabu
30Ndipo Loti anabwera kutuluka mu Zowari nakhala m'phiri ndi ana aakazi awiri pamodzi naye: chifukwa anaopa kukhala mu Zowari, ndipo anakhala m'phanga, iye ndi ana ake aakazi. 31Woyamba ndipo anati kwa wamng'ono, Atate wathu akalamba, ndipo palibe padziko lapansi mwamuna amene adzalowa kwa ife monga amachita padziko lonse lapansi: 32tiyeni, timwetse atate vinyo, tidzagona naye, kuti tisunge mbeu za atate wathu. 33Ndipo anamwetsa atate wao vinyo usiku womwewo; woyamba ndipo analowa nagona naye atate wake; ndipo sanadziwe pomwe anagona ndi pomwe anauka. 34Ndipo panali m'mamawa, woyamba anati kwa wamng'ono, Taona, ndinagona ine ndi atate wanga usiku walero: timwetsenso iye usikunso: udzalowe nugone naye kuti tisunge mbeu za atate wathu. 35Ndipo anamwetsa vinyo atate wao usiku womwenso; wamng'ono ndipo anauka nagona naye; ndipo iye sanadziwe pomwe anagona ndi pomwe anauka. 36Ndipo ana aakazi awiri a Loti anali ndi pakati pa atate wao. 37#Deut. 2.9Woyamba ndipo anabala mwana wamwamuna, namtcha dzina lake. Mowabu; yemweyo ndi atate wa Amowabu kufikira lero. 38#Deut. 2.19Wamng'ono ndipo anabala mwana wamwamuna, namtcha dzina lake Benami; yemweyo ndi atate wa Aamoni kufikira lero.
Currently Selected:
GENESIS 19: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi

: