GENESIS 39
39
Yosefe ayesedwa ndi mkazi wa Potifara
1Ndipo anatsika naye Yosefe kunka ku Ejipito; ndipo Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda, Mwejipito, anamgula iye m'manja mwa Aismaele amene anatsika naye kunka kumeneko. 2#Mac. 7.9Ndipo Yehova anali ndi Yosefe; ndipo iye anali wolemeralemera; nakhala m'nyumba ya mbuyake Mwejipito. 3#Mas. 1.2Ndipo mbuyake anaona kuti Yehova anali ndi iye, ndi kuti Yehova anamlemereza m'dzanja lake zonse anazichita. 4Ndipo Yosefe anapeza ufulu pamaso pake, ndipo anamtumikira iye; ndipo anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yake, naika m'manja mwake zonse anali nazo. 5Ndipo panali chiyambire anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yake, ndi pa zake zonse, Yehova anadalitsa nyumba ya Mwejipito chifukwa cha Yosefe; ndipo mdalitso wa Yehova unali pa zake zonse, m'nyumba ndi m'munda. 6#1Sam. 16.12Ndipo iye anasiya zake zonse m'manja a Yosefe: osadziwa chomwe anali nacho, koma chakudya chimene anadya. Ndipo Yosefe anali wokoma thupi ndi wokongola. 7Ndipo panali zitapita izi, kuti mkazi wa mbuyake anamyang'anira maso Yosefe: ndipo mkaziyo anati, Gona ndi ine. 8Koma iye anakana, nati kwa mkazi wa mbuyake, Taonani, mbuyanga sadziwa chimene chili ndi ine m'nyumbamu, ndipo anaika zake zonse m'manja anga; 9#2Sam. 12.13; Mas. 51.4mulibe wina m'nyumba wamkulu ndine; ndipo sanandikanize ine kanthu, koma iwe, chifukwa kuti uli mkazi wake: nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu? 10#Miy. 1.10Ndipo pali pakunenanena ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, iye sanamvere mkazi kugona naye kapena kukhala naye. 11Ndipo panali, nthawi yomweyo, iye analowa m'nyumba kuti agwire ntchito yake; ndipo munalibe amuna a m'nyumba m'katimo. 12Ndipo mkazi anagwira iye chofunda chake, nati, Gona ndi ine; ndipo anasiya chofunda chake m'dzanja lake nathawa, natulukira kubwalo. 13Ndipo panali pamene mkazi anaona kuti anasiya chofunda chake m'dzanja lake, nathawira kubwalo, 14anaitana aamuna a m'nyumba yake, nanena ndi iwo kuti, Taonani, walowetsa kwa ife Muhebri kuti atiseke ife, analowa kwa ine kugona ndi ine, ndipo ndinafuula ndi mau aakulu: 15ndipo panali pamene iye anamva kuti ndinakweza mau anga ndi kufuula, iye anasiya chofunda chake kwa ine nathawira kubwalo. 16Ndipo anasunga chofunda chake chikhale ndi iye kufikira atabwera kwao mbuyake. 17Ndipo ananena kwa iye monga mau awa, anati, Analowa kwa ine kapolo wa Chihebri uja, munabwera naye kwathu, kundipunza ine: 18ndipo panali pamene ndinakweza mau anga ndi kufuula, iye anasiya chovala chake kwa ine, nathawira kunja. 19Ndipo panali pamene mbuyake anamva mau a mkazi wake, amene ananena kwa iye, kuti, Choterochi anandichitira ine kapolo wako; kuti iye anapsa mtima. 20#Mas. 105.18Ndipo mbuyake wa Yosefe anamtenga iye namuika m'kaidi, umo anamangidwa akaidi a mfumu: ndipo iye anali m'mwemo m'kaidimo. 21#Gen. 39.2; Eks. 3.21Koma Yehova anali ndi Yosefe namchitira iye zokoma, nampatsa ufulu pamaso pa woyang'anira kaidi. 22#Gen. 40.4Ndipo woyang'anira kaidi anapereka m'manja a Yosefe akaidi onse okhala m'kaidimo, ndipo zonse iwo anazichita m'menemo, iye ndiye wozichita. 23#Gen. 39.2-3Woyang'anira m'kaidi sanayang'anire kanthu kalikonse kamene kanali m'manja a Yosefe, chifukwa Yehova anali ndi iye; ndipo zimene anazichita, Yehova anazipindulitsa.
Currently Selected:
GENESIS 39: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi

: