GENESIS 42
42
Abale a Yosefe afika ku Ejipito
1Ndipo anaona Yakobo kuti mu Ejipito munali tirigu, nati Yakobo kwa ana ake aamuna, Chifukwa chanji mulinkuyang'anana? 2#Mac. 7.12Ndipo iye anati, Taonani, ndamva kuti mu Ejipito muli tirigu, mutsikireko mutigulire kumeneko; kuti tikhale ndi moyo, tisafe. 3Ndipo abale ake a Yosefe khumi anatsikira kukagula tirigu mu Ejipito. 4Koma Yakobo sanamtume Benjamini mphwake wa Yosefe, pamodzi ndi abale ake, chifukwa anati, Choipa chingam'gwere iye. 5Ndipo ana aamuna a Israele anadza kudzagula mwa iwo amene anadzako, pakuti m'dziko la Kanani munali njala. 6#Gen. 37.7Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m'dziko; ndipo anafika abale ake a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi. 7Ndipo Yosefe anaona abale ake, ndipo anazindikira iwo, koma anadziyesetsa kwa iwo ngati mlendo, nanena kwa iwo mwankhanza: ndipo anati kwa iwo, Mufuma kuti inu? Nati iwo, Ku dziko la Kanani kudzagula chakudya. 8Ndipo Yosefe anazindikira abale ake, koma iwo sanamzindikire iye. 9#Gen. 37.5Ndipo Yosefe anakumbukira maloto amene analota za iwo, ndipo anati kwa iwo, Ozonda inu; mwadzera kudzaona usiwa wa dziko. 10Ndipo iwo anati kwa iye, Iai, mbuyanga, koma akapolo anu adzera kudzagula chakudya. 11Tonse tili ana aamuna a munthu mmodzi; tili oona, akapolo anu, sitili ozonda. 12Ndipo iye anati kwa iwo, Iai, koma mwadzera kuti muone usiwa wa dziko. 13#Gen. 42.32Nati iwo, Akapolo anu ndife abale khumi, ana aamuna a munthu mmodzi m'dziko la Kanani; ndipo, taonani, wamng'ono ali ndi atate wathu lero; ndipo palibe mmodzi. 14Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Ndicho chimene ndinakunenani inu, kuti, Ndinu ozonda. 15Mudzayesedwa ndi ichi, pali moyo wa Farao, simudzatuluka muno, koma akadze kuno mphwanu ndiko. 16Tumizani mmodzi wa inu akatenge, adze naye mphwanu: ndipo inu mudzamangidwa kuti mau anu ayesedwe, ngati zoona zili mwa inu: penatu, pali moyo wa Farao, muli ozonda ndithu. 17Ndipo anaika onse m'kaidi masiku atatu. 18Ndipo Yosefe anati kwa iwo tsiku lachitatu, Chitani ichi, kuti mukhale ndi moyo; ine ndiopa Mulungu; 19ngati muli oona, mmodzi wa abale anu amangidwe m'kaidi momwemo; mukani inu, mupite naye tirigu wa njala ya mabanja anu; 20#Gen. 43.5koma mukatenge mphwanu kudza naye kwa ine, kuti atsimikizidwe mau anu ndipo simudzafa. Ndipo anachita chomwecho. 21#Yob. 35.8-9Ndipo iwo anati wina ndi mnzake, Tachimwiratu mbale wathu, pamene tinaona kuvutidwa kwa mtima wake, potipembedzera ife, koma ife tinakana kumvera, chifukwa chake kuvutidwa kumene kwatifikira. 22#1Maf. 2.32; Mas. 9.12; Luk. 11.50Ndipo Rubeni anayankha nati kwa iwo, Kodi sindinanene kwa inu kuti, Musachimwire mwanayu; ndipo inu munakana kumvera? Chifukwa chakenso, taonani mwazi wake ufunidwa. 23Ndipo sanadziwe kuti Yosefe anamva; chifukwa anali ndi womasulira. 24Ndipo anawafotokozera iwo nalira, nawatembenukiranso, nanena nao, nampatula Simeoni mwa iwo, nammanga iye pamaso pao. 25Ndipo Yosefe analamulira kuti adzaze zotengera zao ndi tirigu, ndi kubweza ndalama zao, aliyense m'thumba mwake, ndi kuwapatsa phoso la panjira; ndipo anatero nao.
Abale a Yosefe apita kwao
26Ndipo anasenzetsa abulu ao tirigu wao nachokapo. 27Ndipo pamene wina wa iwo anamasula thumba lake kuti adyetse bulu wake pachigono, anapeza ndalama zake; taonani, zinali kukamwa kwa thumba lake. 28Ndipo iye anati kwa abale ake, Wandibwezera ine ndalama zanga, taonani, zili kukamwa kwa thumba langa; ndipo mitima yao inawadera iwo, nanthunthumira, natembenukirana wina ndi mnzake kuti, Nchiyani ichi Mulungu watichitira ife? 29Ndipo anadza kwa Yakobo atate wao ku dziko la Kanani, namfotokozera iye zonse zinaonekera kwa iwo; 30kuti, Munthu mwini dziko, ananena ndi ife mwankhalwe, natiyesa ife ozonda dziko. 31Koma ife tinati kwa iye, Tili anthu oona; sitili ozonda; 32tili abale khumi ndi awiri, ana a atate wathu; wina palibe, ndipo lero wamng'ono ali ndi atate wathu m'dziko la Kanani. 33Ndipo munthuyo mwini dziko anati kwa ife, Momwemu ndidzadziwa kuti muli anthu oona; siyani mmodzi wa abale anu pamodzi ndi ine, tengani tirigu wa njala ya kwanu, mukani; 34idzani naye mphwanu kwa ine, ndipo ndidzadziwa kuti simuli ozonda koma anthu oona: chomwecho ndidzakubwezerani inu mbale wanu, ndipo mudzachita malonda m'dziko muno. 35Ndipo panali pamene analikukhuthula matumba ao, taonani, phukusi la ndalama la yense linali m'thumba lake; ndipo pamene iwo ndi atate ao anaona mapukusi a ndalama anaopa. 36Ndipo Yakobo atate wao anati kwa iwo, Munandilanda ine ana; Yosefe palibe, Simeoni palibe, ndipo mudzachotsa Benjamini: zonse zimene zandigwera. 37Ndipo Rubeni anati kwa atate wake, kuti, Muwaphe ana anga aamuna awiri ndikapanda kumbweza iye kwa inu; mumpereke iye m'manja mwanga, ndipo ine ndidzambwezanso kwa inu. 38#Gen. 44.29Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, chifukwa kuti mkulu wake wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati choipa chikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.
Currently Selected:
GENESIS 42: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi

: