GENESIS 45
45
Yosefe adziulula kwa abale ake
1Ndipo Yosefe sanakhoze kudziletsa pamaso pa onse amene anaima naye: nati, Tulutsa anthu onse pamaso panga. Ndipo panalibe munthu pamodzi ndi iye pamene Yosefe anadziululira yekha kwa abale ake. 2#Gen. 43.30Ndipo analira momveka, ndipo anamva Aejipito, ndipo anamva a m'nyumba ya Farao. 3#Mac. 7.13Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, Ine ndine Yosefe; kodi akali ndi moyo atate wanga? Ndipo abale ake sanakhoze kumyankha iye; pakuti anavutidwa pakumuona iye. 4#Gen. 37.28Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, Muyandikiretu kwa ine; nayandikira. Ndipo iye anati, Ine ndine Yosefe mbale wanu, ine ndemwe munandigulitsa ndilowe mu Ejipito. 5#Gen. 50.20; Mas. 105.16-17Tsopano musapwetekwe mtima, musadzikwiyira inu nokha, kuti munandigulitsa ine kuno, pakuti Mulungu ananditumiza ine patsogolo panu kuti ndisunge moyo. 6Zaka ziwirizi muli njala m'dziko muno; ndipo zatsala zaka zisanu, zopanda kulima kapena kusenga. 7Ndipo Mulungu anatumiza ine patsogolo panu kuti ndikhazike inu mutsale m'dziko lapansi, ndi kusunga inu amoyo ndi chipulumutso chachikulu. 8Ndipo tsopano sindinu amene munanditumiza ine ndifike kuno, koma Mulungu, ndipo anandiyesa ine atate wa Farao, ndi mwini banja lake lonse, ndi wolamulira dziko lonse la Ejipito. 9Fulumirani. Kwerani kunka kwa atate wanga, muti kwa iye, Chotere ati Yosefe mwana wanu, Mulungu wandiyesa ine mwini Ejipito lonse: tsikirani kwa ine, musachedwe. 10#Eks. 8.22Ndipo mudzakhala m'dziko la Goseni, mudzakhala pafupi ndi ine, inu ndi ana anu, ndi ana a ana anu, ndi nkhosa zanu, ndi zoweta zanu, ndi zonse muli nazo; 11ndipo ndidzachereza inu komweko; pakuti zatsala zaka zisanu za njala; kuti mungafikire umphawi, inu ndi banja lanu, ndi onse muli nao. 12Taonani, maso anu aona, ndi maso a mphwanga Benjamini, kuti ndi m'kamwa mwanga ndilikulankhula ndi inu. 13#Mac. 7.14Ndipo mudzafotokozera atate wanga za ulemerero wanga wonse mu Ejipito, ndi zonse mwaziona; ndipo muzifulumira ndi kutsitsira kuno atate wanga. 14Ndipo anagwa pakhosi pake pa Benjamini, nalira; ndipo Benjamini nalira pakhosi pake. 15Ndipo anampsompsona abale ake onse, nalirira iwo; ndipo pambuyo pake abale ake onse anacheza naye.
16Ndipo mbiri yake inamveka m'nyumba ya Farao, kuti abale ake a Yosefe afika; ndipo inamkomera Farao, ndi anyamata ake. 17Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Nena ndi abale ako, Chitani ichi; senzetsani nyama zanu, ndi kupita kunka ku dziko la Kanani; 18katengeni atate wanu ndi mabanja anu, nimudze kwa ine; ndipo ndidzakupatsani inu zabwino za dziko la Ejipito, ndipo mudzadya zonenepa za dzikoli. 19Tsopano mwalamulidwa chitani ichi; muwatengere ana anu ndi akazi magaleta a m'dziko la Ejipito; nimubwere naye atate wanu. 20Musasamalire chuma chanu; popeza zabwino za dziko lonse la Ejipito ndi zanu. 21Ndipo ana a Israele anachita chotero: ndipo Yosefe anawapatsa iwo magaleta monga analamulira Farao, nawapatsa phoso la panjira. 22Onse anawapatsa yense zovala zopindula; koma Benjamini anampatsa masekeli a siliva mazana atatu ndi zovala zopindula zisanu. 23Kwa atate wake anatumiza zotere: abulu khumi osenza zinthu zabwino za mu Ejipito, ndi abulu aakazi khumi osenza tirigu, ndi chakudya, ndi phoso la atate la panjira. 24Ndipo anamukitsa abale ake, ndipo anachoka; ndipo anati kwa iwo, Musakangane panjira. 25Ndipo anakwera kutuluka mu Ejipito, nafika ku dziko la Kanani kwa Yakobo atate wao. 26Ndipo anamfotokozera iye kuti, Yosefe akali ndi moyo, ndipo alamulira m'dziko lonse la Ejipito. Pamenepo mtima wake unakomoka, pakuti sanawakhulupirire iwo. 27Ndipo anamfotokozera iye mau onse a Yosefe amene ananena ndi iwo; ndipo pamene anaona magaleta amene Yosefe anatumiza kuti amtengeremo, mtima wa Yakobo atate wao unatsitsimuka; 28ndipo Israele anati, Chakwana; Yosefe mwana wanga akali ndi moyo; ndidzamuka ndikamuone iye ndisanafe.
Currently Selected:
GENESIS 45: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi

: