LUKA 22
22
Yudasi apangana kupereka Yesu
(Mat. 26.1-5, 14-16; Mrk. 14.10-11; Yoh. 11.45-53)
1Ndipo chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa chinayandikira, ndicho chotchedwa Paska. 2#Yoh. 11.47, 53Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna maphedwe ake pakuti anaopa anthuwo.
3 #
Mrk. 14.10; Yoh. 13.2, 27 Ndipo Satana analowa mwa Yudasi wonenedwa Iskariote, amene anawerengedwa mmodzi wa khumi ndi awiriwo. 4Ndipo iye anachoka, nalankhulana ndi ansembe aakulu ndi akazembe mompereka Iye kwa iwo. 5#Zek. 11.12Ndipo anakondwera, napangana naye kumpatsa ndalama. 6Ndipo iye anavomera, nafunafuna nthawi yabwino yakumpereka Iye kwa iwo, pakalibe khamu la anthu.
Paska lotsiriza. Mgonero
(Mat. 26.17-30; Mrk. 14.12-26; Yoh. 13.21-30; 1Ako. 11.23-29)
7Ndipo tsiku la mikate yopanda chotupitsa linafika, limene inayenera kuphedwa nsembe ya Paska. 8Ndipo Iye anatumiza Petro ndi Yohane, nati, Pitani mutikonzere ife Paska, kuti tidye. 9Ndipo iwo ananena naye, Mufuna tikakonzere kuti? 10Ndipo Iye anati kwa iwo, Onani, mutalowa m'mzinda, adzakomana ndinu munthu alikusenza mtsuko wa madzi; mumtsate ameneyo kunyumba kumene akalowako iye. 11Ndipo mukanene kwa mwini nyumbayo, Mphunzitsi anena nawe, Chipinda cha alendo chili kuti, m'mene ndikadye Paska pamodzi ndi ophunzira anga? 12Ndipo iyeyo adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokonzeka; mukakonzere kumeneko. 13Ndipo anapita iwo, napeza monga adatero nao; ndipo anakonza Paska.
14 #
Mrk. 14.17
Ndipo itadza nthawi yake, Iye anakhala pachakudya, ndi ophunzira pamodzi ndi Iye. 15Ndipo anati kwa iwo, Ndinalakalaka ndithu kudya Paska uwu pamodzi ndinu, ndisanayambe kusautsidwa; 16pakuti ndinena ndi inu, sindidzadya kufikira udzakwaniridwa mu Ufumu wa Mulungu. 17Ndipo analandira chikho, ndipo pamene adayamika, anati, Landirani ichi, muchigawane mwa inu nokha; 18#Mrk. 14.25pakuti ndinena kwa inu, kuyambira tsopano Ine sindidzamwako chipatso cha mpesa, kufikira Ufumu wa Mulungu udzafika. 19#Mrk. 14.22Ndipo m'mene adatenga mkate, nayamika, anaunyema, nawapatsa, nanena, Ichi ndi thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikumbukiro changa. 20#1Ako. 10.16Ndipo choteronso chikho, atatha mgonero, nanena, Chikho ichi ndi pangano latsopano m'mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu. 21#Mas. 41.9; Mrk. 14.18; Yoh. 13.21, 26Koma onani, dzanja lake la iye amene adzandipereka ali pagome pano pamodzi ndi Ine. 22#Mac. 2.23; 4.27-28Pakuti Mwana wa Munthu amukatu, monga kunaikidwiratu; koma tsoka munthuyo amene ampereka! 23#Yoh. 13.22, 25Ndipo anayamba kufunsana mwa iwo okha, ndiye yani mwa iwo amene adzachita ichi.
Kutsutsana kwakuti wamkulu ndani?
(Mat. 20.25-28; Mrk. 10.42-45)
24Ndipo kunakhala kutsutsana mwa iwo, ndani wa iwo ayesedwe wamkulu. 25Ndipo anati kwa iwo, Mafumu a anthu a mitundu awachitira ufumu; ndipo iwo amene awachitira ulamuliro anenedwa, Ochitira zabwino. 26#Luk. 9.46, 48Koma sipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkulu mwa inu, akhale ngati wamng'ono; ndi iye ali woyamba, akhale ngati wotumikira. 27#Luk. 12.37; Yoh. 13.13-14Pakuti wamkulu ndani, iye wakuseama pachakudya kapena wakutumikirapo? Si ndiye wakuseama pachakudya kodi? Koma Ine ndili pakati pa inu monga ngati wotumikira. 28#Aheb. 4.15Koma inu ndinu amene munakhala ndi Ine chikhalire m'mayesero anga; 29ndipo Ine ndikuikirani ufumu, monganso Atate wanga anandiikira Ine, kuti mukadye ndi kumwa kugome kwanga mu Ufumu wanga; 30#Mat. 19.28ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele.
Yesu achenjeza Petro
(Mat. 26.33-35; Mrk. 14.27-31; Yoh. 13.36-38)
31 #
1Pet. 5.8
Simoni, Simoni, taona, Satana anafunsa akutengeni kuti akupeteni ngati tirigu; 32#Yoh. 17.9, 11, 15; 21.15-17koma ndinakupempherera kuti chikhulupiriro chako chingazime; ndipo iwe, pamene watembenuka ukhazikitse abale ako. 33Ndipo anati kwa Iye, Ambuye, ndilipo ndikapite ndi Inu kundende ndi kuimfa. 34#Mrk. 14.30Ndipo Iye anati, Ndikuuza iwe, Petro, sadzalira tambala lero lino kufikira udzakana katatu kuti sundidziwa Ine. 35#Mat. 10.9Ndipo anati kwa iwo, Pamene ndinakutumizani opanda thumba la ndalama, ndi thumba la kamba, ndi nsapato, munasowa kanthu kodi? Anati iwo, Iai. 36Ndipo anati kwa iwo, Koma tsopano, iye amene ali ndi thumba la ndalama, alitenge, ndi thumba la kamba lomwe; ndipo amene alibe, agulitse chofunda chake, nagule lupanga. 37#Yes. 53.12Pakuti ndinena ndi inu, chimene chidalembedwa chiyenera kukwanitsidwa mwa Ine, Ndipo anawerengedwa ndi anthu opanda lamulo; pakuti izi za kwa Ine zili nacho chimaliziro. 38Ndipo iwo anati, Ambuye, taonani, malupanga awiri siwa. Ndipo anati kwa iwo, Chakwanira.
Yesu mu Getsemani
(Mat. 26.36-46; Mrk. 14.32-42; Yoh. 18.1)
39Ndipo Iye anatuluka, napita monga ankachitira, kuphiri la Azitona; ndi ophunzira anamtsata Iye. 40#Mat. 6.13; Mrk. 14.38Ndipo pofika pomwepo, anati kwa iwo, Pempherani kuti mungalowe m'kuyesedwa. 41#Mrk. 14.35Ndipo anapatukana nao kutalika kwake ngati kuponya mwala, nagwada pansi napemphera, 42#Yoh. 5.30nati, Atate, mukafuna Inu, chotsani chikho ichi pa Ine; koma si kufuna kwanga ai, komatu kwanu kuchitike. 43#Mat. 4.11Ndipo anamuonekera Iye mngelo wa Kumwamba namlimbitsa Iye. 44#Yoh. 12.27; Aheb. 5.7Ndipo pokhala Iye m'chipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lake linakhala ngati madontho aakulu a mwazi alinkugwa pansi. 45Ndipo pamene ananyamuka pakupemphera anadza kwa ophunzira, nawapeza ali m'tulo ndi chisoni, 46#Mat. 6.13; Mrk. 14.38ndipo anati kwa iwo, Mugoneranji? Ukani, pempherani kuti mungalowe m'kuyesedwa.
Amgwira Yesu
(Mat. 26.47-56; Mrk. 14.43-50; Yoh. 18.2-11)
47Pamene Iye anali chilankhulire, taonani, khamu la anthu, ndipo iye wotchedwa Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anawatsogolera; nayandikira Yesu kumpsompsona Iye. 48Koma Yesu anati kwa iye, Yudasi, ulikupereka Mwana wa Munthu ndi chimpsompsono kodi? 49Ndipo m'mene iwo akumzinga Iye anaona chimene chiti chichitike, anati, Ambuye, tidzakantha ndi lupanga kodi? 50#Mrk. 14.47Ndipo wina wa iwo anakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, namdula khutu lake lamanja. 51Koma Yesu anayankha nati, Lolani kufikira kumene. Ndipo anakhudza khutu lake, namchiritsa. 52#Mrk. 14.48Ndipo Yesu anati kwa ansembe aakulu ndi akapitao a Kachisi, ndi akulu, amene anadza kumgwira Iye, Munatuluka ndi malupanga ndi mikunkhu kodi monga ngati kugwira wachifwamba? 53#Yoh. 12.27; Aheb. 5.7Masiku onse, pamene ndinali ndi inu mu Kachisi, simunatanse manja anu kundigwira: koma nyengo ino ndi yanu, ndipo ulamuliro wa mdima ndi wanu.
Petro akana Yesu
(Mat. 26.66-75; Mrk. 14.66-72; Yoh. 18.15-18)
54 #
Mat. 26.57-58
Ndipo pamenepo anamgwira Iye, napita naye, nalowa m'nyumba ya mkulu wa ansembe. Koma Petro anatsata kutali. 55#Mrk. 14.66Ndipo pamene adasonkha moto m'kati mwa bwalo, nakhala pansi pamodzi, Petro anakhala pakati pao. 56Ndipo mdzakazi anamuona iye alikukhala m'kuwala kwake kwa moto, nampenyetsa iye, nati, Munthu uyunso anali naye. 57Koma anakana, nati, Mkaziwe, sindimdziwa Iye. 58#Mrk. 14.69-70Ndipo popita kamphindi, anamuona wina, nati, Iwenso uli mmodzi wa awo. Koma Petro anati, Munthu iwe, sindine. 59#Mrk. 14.69-70Ndipo patapita ngati ora limodzi, wina ananenetsa, kuti, Zoonadi, munthu uyunso anali naye, pakuti ndiye Mgalileya 60Koma Petro anati, Munthu iwe, sindidziwa chimene uchinena. Ndipo pomwepo, iye ali chilankhulire, tambala analira. 61#Mat. 26.34; Mrk. 14.72; Yoh. 13.38Ndipo Ambuye anapotoloka, nayang'ana Petro. Ndipo Petro anakumbukira mau a Ambuye, kuti anati kwa iye, Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu. 62Ndipo anatuluka, nalira misozi ndi kuwawa mtima.
Yesu pa bwalo la akulu a Ayuda
(Mat. 26.57-68; Mrk. 14.53-65; Yoh. 18.27)
63Ndipo amuna amene analikusunga Yesu anamnyoza Iye, nampanda. 64Ndipo anamkulunga Iye m'maso, namfunsa, nati, Talota; anakupanda Iwe ndani? 65Ndipo zambiri zina anamnenera Iye, namchitira mwano.
66 #
Mat. 27.1; Mrk. 14.61 Ndipo pamene kunacha, bungwe la akulu a anthu linasonkhana, ndiwo ansembe aakulu ndi alembi; ndipo anapita naye kubwalo lao, 67nanena, Ngati uli Khristu, utiuze. Ndipo anati kwa iwo, Ndikakuuzani, simudzavomereza; 68ndipo ndikakufunsani kanthu, simudzayankha. 69#Mrk. 14.62Koma kuyambira tsopano Mwana wa Munthu adzakhala padzanja lamanja la mphamvu ya Mulungu. 70#Mrk. 14.62Ndipo onse anati, Umo mtero, muli Mwana wa Mulungu kodi? Ndipo Iye anati kwa iwo, Munena kuti ndine. 71#Mrk. 14.63Ndipo iwo anati, Tifuniranjinso mboni? Pakuti ife tokha tinamva m'kamwa mwa Iye mwini.
Currently Selected:
LUKA 22: BLP-2018
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi

: