11
Nsanja ya Babeli
1Nthawi imeneyo anthu onse a pa dziko lapansi ankayankhula chiyankhulo chimodzi ndipo mawu amene ankayankhula anali amodzi. 2Pamene anthu amapita chakummawa anapeza chigwa ku dziko la Sinara nakhazikikako.
3Tsono anawuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuziwotcha bwinobwino.” Tsono mʼmalo mwa miyala anagwiritsa ntchito njerwa zowotcha, ndipo mʼmalo mwa matope anagwiritsa ntchito phula. 4Kenaka anati, “Tiyeni tidzimangire mzinda wokhala ndi nsanja yoti ikafike kumwamba kuti titchuke. Kupanda kutero tibalalikana pa dziko lonse lapansi.”
5Koma Yehova anatsika kudzaona mzindawo ndi nsanja imene anthu aja ankayimanga. 6Yehova anati, “Anthuwa ndi amodzi, ndipo ali ndi chiyankhulo chimodzi. Izi akuchitazi nʼchiyambi chabe cha zomwe akufuna kukwaniritsa kuchita. 7Tiyeni titsikireko tikasokoneze chiyankhulo chawo kuti asamamvetsetsane.”
8Choncho Yehova anabalalitsa anthu aja pa dziko lonse lapansi ndipo analeka kumanga mzindawo. 9Nʼchifukwa chake mzindawo unatchedwa Babeli, popeza Yehova anasokoneza chiyankhulo cha anthu onse. Powachotsa kumeneko, Yehova anawabalalitsira pa dziko lonse lapansi.
Mibado Kuyambira pa Semu Mpaka Abramu
10Nayi mibado yochokera kwa Semu.
Patapita zaka ziwiri chitatha chigumula, Semu ali ndi zaka 100, anabereka Aripakisadi. 11Atabereka Aripakisadi, Semu anakhala ndi moyo zaka 500 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
12Pamene Aripakisadi anali ndi zaka 35, anabereka Sela. 13Atabereka Sela, Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
14Pamene Sela anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Eberi. 15Atabereka Eberi, Sela anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
16Pamene Eberi anali ndi zaka 34 anabereka Pelegi. 17Atabereka Pelegi, Eberi anakhala ndi moyo zaka zina 430 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
18Pamene Pelegi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Reu. 19Atabereka Reu, Pelegi anakhala zaka zina 209 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
20Pamene Reu anali ndi zaka 32, anabereka Serugi. 21Atabereka Serugi, Reu anakhala ndi moyo zaka zina 207 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
22Pamene Serugi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Nahori. 23Atabereka Nahori, Serugi anakhala ndi moyo zaka zina 200 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
24Pamene Nahori anali ndi zaka 29, anabereka Tera. 25Atabereka Tera, Nahori anakhala ndi moyo zaka zina 119 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
26Pamene Tera anali ndi zaka 70, anabereka Abramu, Nahori ndi Harani.
Mibado Yochokera mwa Tera
27Nayi mibado yochokera mwa Tera.
Tera anabereka Abramu, Nahori ndi Harani. Ndipo Harani anabereka Loti. 28Abambo ake a Tera akanali ndi moyo, Harani anamwalira ku Uri wa ku Akaldeya kumene anabadwira. 29Abramu ndi Nahori onse anakwatira. Dzina la mkazi wa Abramu linali Sarai, ndipo la mkazi wa Nahori linali Milika. Iyeyu ndi Isika abambo awo anali Harani. 30Sarai analibe ana chifukwa anali wosabereka.
31Tera anatenga mwana wake Abramu, mdzukulu wake Loti, ndi mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu natuluka mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kupita ku Kanaani. Pamene anafika ku Harani, anakhazikika kumeneko.
32Tera anamwalira ku Harani ali ndi zaka 205.