YouVersion Logo
Search Icon

Yohane 14

14
Yesu Atonthoza Ophunzira Ake
1 “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu; khulupirirani Inenso. 2Mʼnyumba mwa Atate anga muli zipinda zambiri. Kukanakhala kuti mulibemo ndikanakuwuzani. Ine ndikupita kumeneko kukakukonzerani malo. 3Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti kumene kuli Ineko, inunso mukakhale komweko. 4Inu mukudziwa njira ya kumene Ine ndikupita.”
Yesu Njira ya kwa Atate
5Tomasi anati kwa Iye, “Ambuye ife sitikudziwa kumene Inu mukupita, nanga tingadziwe bwanji njirayo?”
6Yesu anayankha kuti, “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine. 7Mukanandidziwadi Ine, mukanadziwanso Atate anga. Kuyambira tsopano, mukuwadziwa ndipo mwawaona.”
8Filipo anati, “Ambuye, tionetseni Atatewo ndipo ife tikhutitsidwa.”
9Yesu anayankha kuti, “Kodi iwe Filipo, ndakhala pakati panu nthawi yonseyi ndipo iwe sukundidziwabe? Aliyense amene waona Ine, waonanso Atate. Tsono ukunena bwanji kuti, ‘Tionetseni Atate?’ 10Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndili mwa Atate, ndipo Atate ali mwa Ine? Mawu amene Ine ndiyankhula kwa inu si mawu anga okha koma ndi mawu Atate wokhala mwa Ine, amene akugwira ntchito yake. 11Khulupirirani Ine pamene ndi kuti Ine ndili mwa Atate ndipo Atate ali mwa Ine. Koma ngati si chomwecho, khulupiriranitu Ine chifukwa cha ntchito zanga zodabwitsa. 12Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene akhulupirira Ine adzachita zimene Ine ndakhala ndikuchita. Iye adzachita ngakhale zinthu zazikulu kuposa zimenezi, chifukwa ndikupita kwa Atate. 13Ndipo Ine ndidzachita chilichonse chimene inu mudzapempha mʼdzina langa kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana. 14Ngati mudzapempha kanthu kalikonse mʼdzina langa, Ine ndidzachita.
Lonjezo la Mzimu Woyera
15 “Ngati mundikonda Ine, sungani malamulo anga. 16Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthawi zonse. 17Nkhosweyo ndiye Mzimu wachoonadi. Dziko lapansi silingalandire Nkhosweyi chifukwa samuona kapena kumudziwa. Koma inu mumamudziwa pakuti amakhala nanu ndipo adzakhala mwa inu. 18Ine sindikusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ine ndidzabweranso kwa inu. 19Patsala nthawi yochepa dziko lapansi silidzandionanso koma inu mudzandiona. Popeza kuti Ine ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo. 20Tsiku limenelo inu mudzazindikira kuti Ine ndili mwa Atate, ndipo inu muli mwa Ine, ndipo Ine ndili mwa inu. 21Iye amene amadziwa malamulo anga ndi kuwasunga ndiye amene amandikonda. Wokonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga ndipo Inenso ndidzamukonda ndikudzionetsa ndekha kwa iye.”
22Kenaka Yudasi (osati Yudasi Isikarioti) anati, “Koma Ambuye, nʼchifukwa chiyani mukufuna kudzionetsa nokha kwa ife, osati ku dziko lapansi?”
23Yesu anamuyankha kuti, “Ngati wina aliyense andikonda Ine, adzasunga mawu anga. Atate wanga adzamukonda, ndipo Ife tidzabwera ndi kukhala naye. 24Iye amene sandikonda Ine sasunga mawu anga. Mawu awa amene mukumva si anga ndi a Atate amene anandituma Ine.
25 “Ndayankhula zonsezi ndikanali nanu. 26Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamutumiza mʼdzina langa adzakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndinakuwuzani. 27Ine ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Ine sindikukupatsani monga dziko lapansi limaperekera. Mtima wanu usavutike ndipo musachite mantha.
28 “Inu munamva Ine ndikunena kuti, ‘Ine ndikupita ndipo ndidzabweranso kwa inu.’ Mukanandikonda, mukanasangalala kuti Ine ndikupita kwa Atate, pakuti Atate ndi wamkulu kuposa Ine. 29Ine ndakuwuzani tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika mudzakhulupirire. 30Ine sindiyankhulanso nanu zambiri nthawi yayitali popeza wolamulira dziko lapansi akubwera. Iye alibe mphamvu pa Ine, 31koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti Ine ndimakonda Atate ndi kuti ndimachita zokhazokha zimene Atate wandilamulira Ine.
“Nyamukani; tizipita.”

Currently Selected:

Yohane 14: CCL

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in