EKSODO 2
2
Kubadwa kwa Mose
1 #
Eks. 6.20
Ndipo anamuka munthu wa banja la Levi, natenga mwana wamkazi wa Levi. 2#Aheb. 11.23Ndipo anaima mkaziyo, naona mwana wamwamuna; m'mene anamuona kuti ali wokoma, anambisa miyezi itatu. 3Koma pamene sanathe kumbisanso, anamtengera kabokosi kagumbwa, napakapo nkhunga ndi phula; naikamo mwanayo, nakaika pakati pa mabango m'mbali mwa nyanja. 4#Eks. 15.20Ndipo mlongo wake anaima patali, adziwe chomwe adzamchitira. 5Ndipo mwana wamkazi wa Farao anatsikira kukasamba m'nyanja; ndipo atsikana ake anayendayenda m'mbali mwa nyanja; ndipo iye anaona kabokosi pakati pa mabango, natuma mdzakazi wake akatenge. 6Pamene anakavundukula, anapenya mwanayo; ndipo taonani, khandalo lilikulira. Ndipo anamva naye chifundo, nati, Uyu ndiye wa ana a Ahebri. 7Pamenepo mlongo wake ananena ndi mwana wamkazi wa Farao, Ndipite ine kodi kukuitanirani woyamwitsa wa Ahebri, akuyamwitsireni mwanayo? 8Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita. Napita namwaliyo, nakaitana amake wa mwanayo. 9Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita naye mwana uyu, ndi kundiyamwitsira iye, ndidzakupatsa mphotho yako. Ndipo mkaziyo anatenga mwanayo, namyamwitsa. 10Ndipo atakula mwanayo, anapita naye kwa mwana wamkazi wa Farao, ndipo iye anakhala mwana wake. Ndipo anamutcha dzina lake Mose, nati, Chifukwa ndinamvuula m'madzi.
11 #
Mac. 7.23; Aheb. 11.24-26 Ndipo kunali masiku amenewo, atakula Mose, kuti anatulukira kukazonda abale ake, napenya akatundu ao; ndipo anaona munthu Mwejipito ali kukantha Muhebri, wa abale ake. 12Ndipo anaunguza kwina ndi kwina, ndipo pamene anaona kuti palibe munthu, anakantha Mwejipito, namfotsera mumchenga. 13M'mawa mwake anatulukanso, ndipo, taonani, anthu awiri Ahebri alikugwirana; ndipo ananena ndi wochimwayo, kuti, Umpandiranji mnzako? 14#Mac. 7.27Koma anati, Wakuika iwe ndani ukhale mkulu ndi woweruza wathu? Kuteroku ukuti undiphe, monga unamupha Mwejipito? Ndipo Mose anachita mantha, nanena, Ndithu chinthuchi chadziwika. 15#Aheb. 11.27Pamene Farao anachimva ichi, anafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa pankhope pa Farao, nakhala m'dziko la Midiyani; nakhala pansi pachitsime. 16#Gen. 24.11Ndipo wansembe wa Midiyani anali nao ana akazi asanu ndi awiri, amene anadza kudzatunga madzi; ndipo anadzaza mimwero kuti amwetse gulu la atate wao. 17Pamenepo anadza abusa nawapirikitsa; koma Mose anauka nawathandiza, namwetsa gulu lao. 18#Eks. 3.1M'mene anafika kwa Reuwele atate wao, iye anati, Mwabwera msanga bwanji lero? 19Ndipo anati iwo, Munthu Mwejipito anatilanditsa m'manja a abusa, natitungiranso madzi okwanira, namwetsa gululi. 20Ndipo anati kwa ana ake akazi, Ali kuti iye? Mwamsiyiranji munthuyo? Kamuitaneni, adzadye chakudya. 21Ndipo Mose anavomera kukhala naye munthuyo; ndipo anampatsa Mose mwana wake wamkazi Zipora. 22#Aheb. 11.13-14Ndipo anaona mwana, ndi Mose anamutcha dzina lake Geresomo; pakuti anati, Ndakhala mlendo m'dziko la eni.
23Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aejipito; ndi ana a Israele anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo. 24#Gen. 15.14Ndipo Mulungu anamva kubuula kwao, ndi Mulungu anakumbukira chipangano chake ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo. 25Ndipo Mulungu anapenya Aisraele, ndi Mulungu anadziwa.
Currently Selected:
EKSODO 2: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: