GENESIS 21
21
Kubadwa kwa Isaki
1 #
Gen. 17.19
Ndipo Yehova anayang'anira Sara monga momwe anati, ndipo Yehova anamchitira iye monga ananena. 2#Gen. 18.10; Aheb. 11.11Ndipo Sara anatenga pakati, nambalira Abrahamu m'ukalamba wake mwana wamwamuna, nthawi yomweyo Mulungu anamuuza iye. 3Ndipo Abrahamu anamutcha dzina lake la mwana wake wamwamuna amene anabala iye, amene anambalira iye Sara, Isaki. 4#Gen. 17.10Ndipo Abrahamu anamdula mwana wake wamwamuna Isaki pamene anali wa masiku ake asanu ndi atatu, monga Mulungu anamlamulira iye. 5#Aro. 4.19Ndipo Abrahamu anali wa zaka zana limodzi pamene anambadwira iye Isaki mwana wake. 6Ndipo Sara anati, Mulungu anandisekeretsa ine; onse akumva adzasekera pamodzi ndi ine. 7Ndipo anati, Akadatero ndani kwa Abrahamu kuti Sara adzayamwitsa ana? Pakuti ndambalira iye mwana wamwamuna m'ukalamba wake.
Abrahamu achotsa Hagara
8Ndipo anakula mwanayo naletsedwa kuyamwa: ndipo Abrahamu anakonza madyerero akulu tsiku lomwe analetsedwa Isaki kuyamwa. 9Ndipo Sara anaona mwana wake wamwamuna wa Hagara Mwejipito, amene anambalira Abrahamu, alinkuseka. 10#Agal. 4.30Chifukwa chake anati kwa Abrahamu, Chotsa mdzakazi uyo, ndi mwana wake wamwamuna; chifukwa mwana wa mdzakazi uyo sadzalowa m'nyumba pamodzi naye mwana wanga Isaki. 11Ndipo mauwo anaipira Abrahamu chifukwa cha mwana wake. 12#Aro. 9.7; Aheb. 11.18Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Usaipidwe nao, chifukwa cha mnyamatayo, ndi chifukwa cha mdzakazi wako; momwe monse akunenera iwe Sara umvere iwe mau ake; chifukwa kuti mwa Isaki zidzaitanidwa mbeu zako. 13Ndipo mwana wamwamuna wa mdzakazi uyo ndidzayesa mtundu, chifukwa iye ndiye mbeu yako. 14Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi mchenje wa madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba. 15Ndipo anatha madzi a m'mchenje ndipo anaika mwana pansi pa chitsamba. 16Ndipo ananka nakhala pansi popenyana naye patali, monga pakugwa muvi: chifukwa anati, Ndisaone kufa kwa mwana. Ndipo anakhala popenyana naye, nakweza mau ake nalira. 17Ndipo Mulungu anamva mau a mnyamatayo, ndi mthenga wa Mulungu anamuitana Hagara, ndi mau odzera kumwamba, nati kwa iye, Watani Hagara? Usaope; chifukwa Mulungu anamva mau a mnyamata kumene ali. 18#Gen. 16.10Tauka, nuukitse mnyamatayo, ndi kumgwira m'dzanja lako; chifukwa ndidzamuyesa iye mtundu waukulu. 19#Num. 22.31; 2Maf. 6.17; Luk. 24.16, 31Ndipo Mulungu anamtsegula m'maso mwake, ndipo anaona chitsime cha madzi; namuka nadzaza mchenje ndi madzi, nampatsa mnyamata kuti amwe. 20Ndipo Mulungu anakhala ndi mnyamata, ndipo anakula iye; nakhala m'chipululu, nakhala wauta. 21Ndipo anakhala m'chipululu cha Parani; ndipo amake anamtengera iye mkazi wa ku dziko la Ejipito.
Abrahamu apangana ndi Abimeleki
22 #
Gen. 26.28
Ndipo panali nthawi yomweyo, Abimeleki ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yake anati kwa Abrahamu, kuti, Mulungu ali pamodzi ndi iwe m'zonse uzichita iwe; 23tsopano iwe undilumbirire ine pano pa Mulungu kuti sudzandinyenga ine, kapena mwana wanga, kapena mdzukulu wanga: koma monga ufulu ndakuchitira iwe udzandichitire ine, ndi dziko lomwe wakhalamo, ngati mlendo. 24Ndipo Abrahamu anati, Ine ndidzalumbira. 25Ndipo Abrahamu anamdzudzula Abimeleki chifukwa cha chitsime cha madzi, anyamata ake a Abimeleki anachilanda. 26Ndipo anati Abimeleki, Sindinadziwe amene anachita icho; ndipo iwe sunandiuze ine, ndiponso sindinamve koma lero lino. 27#Gen. 26.31Ndipo Abrahamu anatenga nkhosa ndi ng'ombe, nampatsa Abimeleki, ndipo anapangana pangano onse awiriwo. 28Ndipo Abrahamu anapatula anaankhosa akazi asanu ndi awiri pa okha. 29Ndipo Abimeleki anati kwa Abrahamu, Nanga anaankhosa akazi asanu ndi awiri amene wapatula pa okha? 30Ndipo anati, Anaankhosa akazi asanu ndi awiriwa uwalandire pa dzanja langa, kuti akhale mboni zanga, kuti ndakumba ine chitsime chimenechi. 31Chifukwa chake anatcha malowo Beereseba: chifukwa pamenepo analumbira onse awiri. 32Ndipo anapangana pangano pa Beereseba: ndipo anauka Abimeleki ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yake, nabwera kunka ku dziko la Afilisti. 33#Gen. 4.26; Yes. 40.28Ndipo Abrahamu anaoka mtengo wa bwemba pa Beereseba, naitanira pamenepo dzina la Yehova, Mulungu wa nthawi zonse. 34Ndipo Abrahamu anakhala ngati mlendo masiku ambiri m'dziko la Afilisti.
Currently Selected:
GENESIS 21: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: