YouVersion Logo
Search Icon

GENESIS 38

38
Yuda ndi Tamara
1Ndipo panali nthawi yomweyo, kuti Yuda anatsikira kwa abale ake nalowa kwa Mwadulamu, dzina lake Hira. 2Ndipo Yuda anaona kumeneko mwana wamkazi wa Mkanani dzina lake Suwa: ndipo anamtenga, nalowa kwa iye. 3Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Eri. 4Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Onani. 5Ndipo anabalanso mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Sela: ndipo iye anali pa Kezibu pamene mkazi anambala iye. 6Ndipo Yuda anamtengera Eri mwana wake woyamba mkazi, ndipo dzina lake ndilo Tamara. 7Koma Eri mwana wake woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova: ndipo Yehova anamupha iye. 8#Deut. 25.5-6; Mat. 22.24Ndipo Yuda anati kwa Onani, Lowani naye mkazi wa mbale wako, ndi kumchitira mkazi zoyenera mphwake wa mwamuna wake, ndi kumuukitsira mkulu wako mbeu. 9Ndipo Onani anadziwa kuti mbeu siidzakhala yake: ndipo panali pamene iye analowana naye mkazi wa mbale wake, kuti anaitaya pansi, kuti angampatse mbeu kwa mkulu wake. 10Koma chimene iye anachita chinali choipa pamaso pa Yehova, ndipo anamupha iyenso. 11#Rut. 1.12Ndipo Yuda anati kwa Tamara mpongozi wake, Khala wamasiye m'nyumba ya atate wako, kufikira akakula msinkhu Sela mwana wanga wamwamuna: chifukwa anati kuti, Angafe iyenso monga abale ake. Ndipo Tamara ananka nakhala m'nyumba ya atate wake. 12Atachuluka masiku mwana wamkazi wa Suwa, mkazi wake wa Yuda anafa; ndipo Yuda anatonthola mtima, nakwera kunka kwa akusenga nkhosa zake ku Timna, iye ndi bwenzi lake Hira, Mwadulamu. 13Ndipo anamuuza Tamara, kuti, Taona, mpongozi wako akwera kunka ku Timna kuti akasenge nkhosa zake. 14Pamenepo anavula zovala zake zamasiye, nadzifunda ndi chofunda chake, navala nakhala pa chipata cha Enaimu, chifukwa chili pa njira ya ku Timna; pakuti anaona kuti Sela anakula msinkhu, ndipo sanampatse iye kuti akhale mkazi wake. 15Pamene Yuda anamuona iye, anaganizira kuti ali mkazi wadama: chifukwa iye anabisa nkhope yake. 16Ndipo iye anapatukira kwa mkazi panjira, nati, Tiyetu, ndilowane nawe; chifukwa sanamdziwe kuti ndiye mpongozi wake. Ndipo anati, Kodi udzandipatsa ine chiyani kuti ulowane ndi ine. 17Ndipo iye anati, Ndidzatumiza kwa iwe kamwana ka mbuzi ka m'ziweto. Ndipo mkazi nati, Kodi udzandipatsa ine chikole mpaka ukatumiza? 18Ndipo iye anati, Chikole chanji ndidzakupatsa iwe? Ndipo mkazi anati, Mphete yako, ndi chingwe chako, ndi ndodo ili m'dzanja lako. Ndipo anampatsa izo, nalowana naye, ndipo mkazi anatenga pakati ndi iye. 19Ndipo mkazi anauka nachoka, navula chofunda chake, navala zovala zamasiye zake. 20Ndipo Yuda anatumiza kamwana kambuzi ndi dzanja la bwenzi lake Mwadulamu, kuti alandire chikole pa dzanja la mkazi; koma sanampeze iye. 21Ndipo anafunsa amuna a pamenepo kuti, Ali kuti wadama uja anali pambali pa njira pa Enaimu? Ndipo iwo anati, Panalibe wadama pano. 22Ndipo iye anabwera kwa Yuda nati, Sitinampeza mkazi; ndiponso amuna a pamenepo anati, Panalibe wadama pano. 23Ndipo Yuda anati, Azilandire kuti tingachitidwe manyazi: taona, ndinatumiza mwana uyu wa mbuzi, ndipo sunampeza iye. 24#Lev. 21.9Ndipo panali itapita miyezi itatu, anamuuza Yuda kuti, Tamara mpongozi wako wachita chigololo, ndiponso taonani, ali ndi pakati ndi chigololocho. Ndipo Yuda anati, Mtulutse iye kuti amponye pamoto. 25Pamene anamtulutsa iye, mkazi anatumiza kwa mpongozi wake kuti, Ndi mwamuna mwini izi ndatenga pakati; ndipo mkazi anati, Tayang'anatu, za yani zimenezi, mphete, ndi chingwe, ndi ndodo? 26#1Sam. 24.17Ndipo Yuda anavomereza nati, Akhale wolungama wopambana ine, chifukwa ine sindinampatsa iye Sela mwana wanga wamwamuna. Ndipo iye sanamdziwenso mkaziyo. 27Ndipo panali nthawi ya kubala kwake, taonani, amapasa anali m'mimba mwake. 28Ndipo panali pamene anabala kuti mmodzi anatulutsa dzanja; ndipo namwino anatenga chingwe chofiira namanga pa dzanja lake, kuti, Uyu anayamba kubadwa. 29#Mat. 1.3Ndipo panali pamene iye anabweza dzanja lake, kuti, taona, mbale wake anabadwa, ndipo namwino anati, Wadziposolera wekha bwanji? Chifukwa chake dzina lake linatchedwa Perezi. 30Ndipo pambuyo pake anabadwa mbale wake, amene anali ndi chingwe chofiira pamkono pake, dzina lake linatchedwa Zera.

Currently Selected:

GENESIS 38: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in