GENESIS 41
41
Yosefe ammasulira Farao maloto ake
1Ndipo panali zitapita zaka ziwiri zamphumphu, Farao analota; ndipo, taonani, anaima panyanja. 2Ndipo, taonani, zinatuluka m'nyanja ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe okoma ndi zonenepa; ndipo zinadya mabango. 3Ndipo, taonani ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zinatuluka m'nyanjamo pambuyo pao, za maonekedwe oipa ndi zoonda; ndipo zinaima pa ng'ombe zinazo m'mphete mwa nyanja. 4Ndipo ng'ombe zazikazi za maonekedwe oipa ndi zoonda zinadya ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe abwino ndi zonenepazo. Ndipo Farao anauka. 5Ndipo anagona nalotanso kachiwiri; ndipo taonani, ngala zisanu ndi ziwiri za tirigu zinamera pa mbuwa imodzi, zonenepa ndi zabwino. 6Ndipo, taonani, ngala zisanu ndi ziwiri, zoonda zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pao. 7Ndipo ngala zoondazo zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zonenepa ndi zodzalazo. Ndipo Farao anauka, ndipo, taonani, analota. 8#Dan. 2.2Ndipo panali m'mamawa mtima wake unavutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a m'Ejipito, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lake; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao. 9Pamenepo wopereka chikho wamkulu anati kwa Farao, kuti, Ine ndidzakumbukira zochimwa zanga lero. 10Farao anakwiya ndi anyamata ake, nandiika ine ndisungidwe m'nyumba ya kazembe wa alonda, ine ndi wophika mkate wamkulu: 11ndipo tinalota loto usiku umodzi ine ndi iye; tinalota munthu yense monga mwa kumasulira kwa loto lake. 12Ndipo panali ndi ife mnyamata Muhebri, kapolo wa kazembe wa alonda, ndipo ife tinafotokozera iye, ndipo iye anatimasulira ife maloto athu; kwa munthu yense monga loto lake anatimasulira. 13Ndipo panali monga momwe iye anatimasulira, momwemo mudachitika; ine anandibwezera mu utumiki wanga, mnzanga anampachika. 14#Mas. 105.20; Dan. 2.25Ndipo Farao anatumiza nakaitana Yosefe; ndipo anamtulutsa iye msanga m'dzenjemo: ndipo iye anameta, napindula malaya ake, nalowa kwa Farao. 15#Dan. 5.16Farao ndipo anati kwa Yosefe, Ine ndalota loto, koma palibe wondimasulira; ndipo ndamva alikunena za iwe kuti, ukamva loto udziwa kumasulira. 16#Dan. 2.20-30Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere. 17Ndipo Farao ananena kwa Yosefe, M'loto langa taona, ndinaima m'mphepete mwa nyanja; 18ndipo taona, zinatuluka m'nyanjamo ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri, zonenepa ndi za maonekedwe abwino; ndipo zinadya m'mabango; 19ndipo taona, ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zina zinatuluka pambuyo pao zosauka ndi za maonekedwe oipa ndi zoonda, zoipa zotere sindinazione m'dziko la Ejipito; 20ndipo ng'ombe zazikazi zoonda ndi za maonekedwe oipa zinadya ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zonenepa. 21Ndipo pamene zinadya sizinadziwika kuti zinadya; koma zinaipabe m'maonekedwe ao monga poyamba. 22Pamenepo ndinauka. Ndipo ndinaona m'kulota kwanga, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zinamera pa mbuwa imodzi zodzala ndi zabwino; 23ndipo, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zina zofota, zoonda, zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pao; 24ndipo ngala zoonda zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zabwino; ndipo ndinafotokozera amatsenga: koma panalibe wondimasulira ine. 25#Dan. 2.28Ndipo Yosefe anati kwa Farao, Loto la Farao lili limodzi: chimene Mulungu ati achite wam'masulira Farao. 26Ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zabwino ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndi ngala zisanu ndi ziwiri zabwino ndizo zaka zisanu ndi ziwiri: loto lili limodzi. 27Ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zoonda ndi za maonekedwe oipa zinatuluka pambuyo pao ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zopanda kanthu zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, ndizo zaka zisanu ndi ziwiri za njala. 28Ichi ndi chinthu chimene ndinena kwa Farao: chimene Mulungu ati achite wasonyeza kwa Farao. 29Taonani, zidzafika zaka zisanu ndi ziwiri zakuchuluka chakudya m'dziko lonse la Ejipito; 30ndipo pambuyo pao zidzauka zaka zisanu ndi ziwiri za njala; ndipo anthu adzaiwala zochuluka zonsezo m'dziko la Ejipito; ndipo njala idzapululutsa dziko; 31ndipo zochuluka sizidzazindikirika chifukwa cha njala ikudza m'mbuyoyo, pakuti idzavuta. 32#Yes. 14.24Ndipo lotolo linabwezedwa kawiri kwa Farao, chifukwa chinthu chili chokhazikika ndi Mulungu, ndipo Mulungu afulumira kuchichita. 33Tsopano, Farao afunefune munthu wakuzindikira ndi wanzeru, amkhazike iye ayang'anire dziko la Ejipito. 34Farao achite chotere, alembe woyang'anira dziko wosonkhetsa limodzi la magawo asanu la dziko la Ejipito m'zaka zisanu ndi ziwiri zakuchuluka dzinthu. 35Iwo asonkhanitse chakudya chonse cha zaka zabwino izo zilinkudzazo, aunjike tirigu m'manja a Farao akhale chakudya m'midzi, namsunge. 36Ndipo chakudyacho chidzakhala m'dziko chosonkhera zaka zisanu ndi ziwiri za njala imene idzakhala m'dziko la Ejipito; kuti dziko lisaonongedwe ndi njala.
Yosefe wolamulira dziko la Ejipito
37Ndipo chinthucho chinali chabwino m'maso mwa Farao, ndi m'maso mwa anyamata ake. 38#Dan. 4.8, 18Ndipo Farao anati kwa anyamata ake, Kodi ife tidzaone munthu ngati uyu, mzimu wa Mulungu uli m'mtima mwake? 39Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Popeza Mulungu wakuonetsa iwe zonsezo palibe wina wakuzindikira ndi wanzeru ngati iwe. 40#Mas. 105.21; Mac. 7.10Uziyang'anira pa nyumba yanga, ndipo anthu anga onse adzalamulidwa mwa mau ako; pa mpando wachifumu pokha ine ndidzakuposa iwe. 41Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Taona, ndakhazika iwe wolamulira dziko lonse la Ejipito. 42#Est. 3.10; 8.15Ndipo Farao anachotsa mphete yosindikizira yake pa dzanja lake, naiveka pa dzanja la Yosefe, namveka iye ndi zovalira zabafuta, naika unyolo wagolide pakhosi pake; 43#Est. 6.9ndipo anamkweza iye m'galeta wake wachiwiri amene anali naye: ndipo anafuula patsogolo pa iye, Gwadani; ndipo anamkhazika iye wolamulira dziko lonse la Ejipito. 44Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Ine ndine Farao, ndipo popanda iwe palibe munthu aliyense adzatukula dzanja lake kapena mwendo wake m'dziko lonse la Ejipito. 45Ndipo Farao anamutcha dzina la Yosefe Zafenati-Panea; ndipo anampatsa akwatire Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni. Ndipo Yosefe anatuluka wolamulira, nayendayenda m'dziko la Ejipito. 46Ndipo Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene iye anaima pamaso pa Farao mfumu ya Aejipito. Ndipo Yosefe anatuluka pamaso pa Farao, napitapita pa dziko lonse la Ejipito. 47Ndipo zaka zisanu ndi ziwiri zakuchuluka dzinthu nthaka inabala zambirimbiri. 48Ndipo anasonkhanitsa chakudya chonse cha zaka zisanu ndi ziwiri chimene chinali m'dziko la Ejipito, nasunga chakudyacho m'midzi; chakudya cha m'minda, yozinga midzi yonse, anachisunga m'menemo. 49Ndipo Yosefe anasunga tirigu ngati mchenga wa panyanja, wambirimbiri kufikira analeka kuwerenga; chifukwa anali wosawerengeka. 50#Gen. 46.20; 48.5Ndipo kwa Yosefe anabadwa ana amuna awiri, chisanafike chaka cha njala, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye. 51Ndipo Yosefe anamutcha dzina la woyamba Manase, chifukwa anati iye, Mulungu wandiiwalitsa ine zovuta zanga zonse, ndi nyumba yonse ya atate wanga. 52Ndipo dzina la wachiwiri anamutcha Efuremu: chifukwa Mulungu anandibalitsa ine m'dziko la kusauka kwanga. 53Ndipo zaka zakuchuluka dzinthu zisanu ndi ziwiri za m'dziko la Ejipito, zinatha. 54#Mas. 106.16; Mac. 7.10Ndipo zinayamba kufika zaka zisanu ndi ziwiri za njala, monga ananena Yosefe; ndipo munali njala m'maiko monse; koma m'dziko lonse la Ejipito munali chakudya. 55Ndipo pamene dziko lonse la Ejipito linali ndi njala, anthu anafuulira Farao awapatse chakudya; ndipo Farao anati kwa Aejipito onse, Pitani kwa Yosefe: chimene iye anena kwa inu chitani. 56Ndipo njala inali pa dziko lonse lapansi; ndipo Yosefe anatsegula nkhokwe zonse nagulitsa Aejipito: ndipo njala inakula m'dziko la Ejipito. 57Ndipo maiko onse anafika ku Ejipito kudzagula tirigu kwa Yosefe: chifukwa njala inakula m'dziko lonse lapansi.
Currently Selected:
GENESIS 41: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: