YouVersion Logo
Search Icon

GENESIS 43

43
Abale a Yosefe atsikiranso ku Ejipito
1Ndipo njala inakula m'dzikomo. 2Ndipo panali pamene atatha kudya tirigu yense anatengayo ku Ejipito atate wao anati kwa iwo, Pitaninso, mukatigulire ife chakudya pang'ono. 3Ndipo Yuda ananena ndi iye kuti, Munthu uja anatilimbitsira mau kuti, simudzaonanso nkhope yanga, koma mphwanu akhale ndi inu ndiko. 4Ngati mudzatuma mphwathu pamodzi ndi ife, tidzatsikira ndi kugulira inu chakudya. 5#Gen. 42.20Koma mukapanda kumtuma iye sititsika; pakuti munthu uja anati kwa ife, Simudzaona nkhope yanga, ngati mphwanu sali ndi inu. 6Ndipo Israele anati, Chifukwa ninji munandichitira ine choipa chotero kuti munamuuza munthuyo muli ndi mphwanu? 7Ndipo iwo anati, Munthuyo anafunsitsa za ife, ndi za abale athu, kuti, Atate wanu alipo? Kodi muli ndi mphwanu? Ndipo tinamfotokozera iye monga mwa mau amenewo: ngati tinadziwa kuti iye adzati, Idzani naye mphwanu? 8Ndipo Yuda anati kwa atate wake Israele, Mumtume mnyamata pamodzi ndi ine ndipo ife tidzanyamuka ndi kupita; kuti tikhale ndi moyo tisafe, ife ndi inu ndi ana athu ang'ono. 9#Gen. 44.32Ine ndidzakhala chikole, pa manja anga mudzamfunsa: ndikapanda kumbwezera kwa inu ndi kumuimitsa pamaso panu, chifukwa chake chidzakhala pa ine masiku onse: 10pakuti tikadaleka kuchedwa mwenzi tsopano titabwera kawiri. 11Ndipo Israele atate wao anati kwa iwo, Ngati chomwecho tsopano chitani ichi: tengani zipatso za m'dziko muno m'zotengera zanu, mumtengere munthu uja mphatso, mafuta amankhwala pang'ono, ndi uchi pang'ono, zonunkhira ndi mure, ndi mfula, ndi katungurume; 12nimutenge ndalama zowirikiza m'manja mwanu; ndipo ndalama zimene zinabwezedwa kukamwa kwa matumba anu mutengenso m'manja mwanu; kapena sanachite dala; 13mutengenso mphwanu, nimunyamuke, mupitenso kwa munthu uja: 14Mulungu Wamphamvuyonse adzakupatsani inu chifundo pamaso pa munthu uja, kuti akumasulireni inu mbale wanu wina ndi Benjamini. Ndipo ine, ngati ndikhala wopanda ana, ndikhalatu.
Abalewo m'nyumba ya Yosefe
15Amunawo ndipo anatenga mphatso natenga ndalama zowirikiza m'manja mwao, ndi Benjamini; ndipo ananyamuka ndi kutsikira ku Ejipito, naima pamaso pa Yosefe. 16Ndipo pamene Yosefe anaona Benjamini pamodzi nao, anati kwa tsanyumba wake, Lowa nao anthuwo m'nyumba, kaphere iwo, kakonzere, chifukwa anthuwo adzadya ndi ine usana uno. 17Munthuyo anachita monga anamuuza Yosefe, ndipo munthuyo analowa nao anthuwo m'nyumba ya Yosefe. 18Anthuwo ndipo anaopa, chifukwa analowezedwa m'nyumba ya Yosefe; nati, Chifukwa cha ndalama zija zinabwezedwa m'matumba athu nthawi yoyamba ija, ife tilowezedwa, kuti aone chifukwa ndi ife, atigwere ife, atiyese ife akapolo, ndi abulu athu. 19Ndipo anayandikira kwa tsanyumba wa Yosefe, ndipo ananena ndi iye pa khomo la nyumba, nati, 20#Gen. 42.3Mfumu, tinatsikira ndithu nthawi yoyamba kudzagula chakudya: 21ndipo panali pamene ife tinafika pachigono, tinamasula matumba athu, ndipo taonani ndalama za yense zinali kukamwa kwa thumba lake, ndalama zathu mkulemera kwake; ndipo tabwera nazo m'manja mwathu. 22Ndalama zina tatenga m'manja mwathu kuti tigule chakudya: sitimdziwa amene anaika ndalama zathu m'matumba athu. 23Ndipo iye anati, Mtendere ukhale ndi inu, musaope; Mulungu wanu ndi Mulungu wa atate wanu anakupatsani inu chuma m'matumba anu; ine ndinali nazo ndalama zanu. Pamenepo anawatulutsira Simeoni. 24#Gen. 18.4Ndipo munthuyo analowetsa anthu m'nyumba ya Yosefe, nawapatsa iwo madzi, natsuka mapazi ao, napatsa abulu ao chakudya. 25Ndipo anakonzeratu mphatso asanafike Yosefe usana; chifukwa anamva kuti adzadya chakudya pamenepo. 26#Gen. 42.6Pamene Yosefe anadza kunyumba kwake, analowa nazo m'nyumba mphatso zinali m'manja mwao, namweramira iye pansi. 27Ndipo anafunsa iwo za ubwino wao, nati, Kodi atate wanu ali ndi moyo? Wokalamba uja amene munanena uja: kodi alipo? 28Ndipo iwo anati, Kapolo wanu atate wathu ali bwino, alipo. Ndipo anawerama, namgwadira iye. 29#Gen. 42.13Ndipo iye anatukula maso ake naona Benjamini mphwake, mwana wa amake, nati, Kodi uyu ndi mphwanu wamng'ono uja, amene munanena ndi ine uja? Ndipo iye anati, Mulungu akuchitire iwe ufulu, mwana wanga. 30#Gen. 45.2Yosefe ndipo anafulumira, chifukwa mtima wake unakhumbitsa mphwake, ndipo anafuna polirira; nalowa m'chipinda chake naliramo. 31Ndipo anasamba nkhope yake, natuluka; ndipo anadziletsa, nati, Ikani chakudya. 32Ndipo anamuikira iye chake pa yekha, ndi iwo chao pa okha, ndi Aejipito akudya naye chao pa okha; chifukwa Aejipito sanathei kudya chakudya pamodzi ndi Ahebri: chifukwa kuchita chomwecho nkunyansira Aejipito. 33Ndipo anakhala pamaso pake, woyamba monga ukulu wake, ndi wamng'ono monga ung'ono wake; ndipo anazizwa wina ndi wina. 34Ndipo anawagawira mitanda ya patsogolo pake; koma mtanda wa Benjamini unaposa mitanda ya onsewo kasanu. Ndipo anamwa, nasekera pamodzi ndi iye.

Currently Selected:

GENESIS 43: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in