GENESIS 49:24-25
GENESIS 49:24-25 BLPB2014
Koma uta wake unakhala wamphamvu, ndi mikono ya manja ake inalimbitsidwa. Ndi manja a Wamphamvu wa Yakobo. (Kuchokera kumeneko ndi mbusa, mwala wa Israele,) Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe, ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iwe. Ndi madalitso a Kumwamba, madalitso a madzi akuya akukhala pansi, madalitso a mawere, ndi a mimba.