GENESIS 49
49
Yakobo adalitsa ana ake namwalira
1Ndipo Yakobo anaitana ana ake amuna, nati, Sonkhanani inu, kuti ndikuuzeni inu chimene chidzakugwerani inu masiku akudzawo.
2Sonkhanani, tamvani, ana amuna a Yakobo;
tamverani Israele atate wanu.
3Rubeni, ndiwe woyamba wanga,
mphamvu yanga ndi chiyambi cha mphamvu yanga;
ulemu wopambana, ndi mphamvu yopambana.
4Wobwabwada ngati madzi; sudzapambana;
chifukwa unakwera pa kama wa atate wako;
pamenepo unaipitsapo; anakwera paja ndigonapo.
5Simeoni ndi Levi ndiwo abale;
zida za mphulupulu ndizo malupanga ao.
6 #
Gen. 34.25
Mtima wangawe, usalowe mu chiungwe chao;
ulemerero wanga, usadziphatike pa masonkhano ao;
chifukwa m'kukwiya kwao anapha munthu.
M'kufuna kwao anapundula ng'ombe.
7 #
Yos. 19.1; 21.3 Kutembereredwe kukwiya kwao,
chifukwa kunali koopsa;
ndi kupsa mtima kwao, chifukwa kunali kwankhalwe.
Ndidzawagawanitsa m'Yakobo.
Ndidzabalalitsa iwo m'Israele.
8Yuda, abale ako adzakuyamika iwe;
dzanja lako lidzakhala pa khosi la adani ako;
ana amuna a atate wako adzakuweramira.
9 #
Chiv. 5.5
Yuda ndi mwana wa mkango,
kuchokera kuzomotola, mwananga, wakwera;
anawerama pansi, anabwatama ngati mkango,
ndipo ngati mkango waukazi; ndani adzamukitsa iye?
10 #
Mat. 2.6
Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda,
kapena wolamulira pakati pa mapazi ake,
kufikira atadza Silo;
ndipo anthu adzamvera iye.
11Adamanga mwana wa kavalo wake pampesa,
ndi mwana wa bulu wake pa mpesa wosankhika;
natsuka malaya ake m'vinyo,
ndi chofunda chake m'mwazi wa mphesa.
12Maso ake adzafiira ndi vinyo,
ndipo mano ake adzayera ndi mkaka.
13Zebuloni adzakhala m'mphepete mwa nyanja;
ndipo iye adzakhala dooko la ngalawa;
ndipo malire ake adakhala pa Sidoni.
14Isakara ndiye bulu wolimba,
alinkugona pakati pa makola.
15Ndipo anaona popumulapo kuti panali pabwino,
ndi dziko kuti linali lokondweretsa;
ndipo anaweramitsa phewa lake kuti anyamule,
nakhala kapolo wakugwira ntchito ya msonkho.
16Dani adzaweruza anthu ake,
monga limodzi la mafuko a Israele.
17Dani adzakhala njoka m'khwalala,
songo panjira,
imene iluma zitende za kavalo,
kuti womkwera wake agwe chambuyo.
18Ndadikira chipulumutso chanu, Yehova.
19Ndi Gadi, achifwamba adzampsinja iye;
koma iye adzapsinja pa chitende chao.
20Ndi Asere, chakudya chake ndicho mafuta,
ndipo adzapereka zolongosoka zachifumu.
21Nafutali ndi mbawala yomasuka;
apatsa mau abwino.
22 #
Yos. 17.14, 18 Yosefe ndi nthambi yobala,
nthambi yobala pambali pa kasupe;
nthambi zake ziyangayanga palinga.
23Eni uta anavutitsa iye kwambiri,
namponyera iye, namzunza.
24Koma uta wake unakhala wamphamvu,
ndi mikono ya manja ake inalimbitsidwa.
Ndi manja a Wamphamvu wa Yakobo.
(Kuchokera kumeneko ndi mbusa, mwala wa Israele,)
25Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe,
ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iwe.
Ndi madalitso a Kumwamba,
madalitso a madzi akuya akukhala pansi,
madalitso a mawere, ndi a mimba.
26Madalitso a atate wako
apambana mphamvu ndi madalitso a makolo anga,
aufikira ku malekezero a patali a mapiri a chikhalire.
Adzakhala pa mutu wa Yosefe,
ndi pakati pa mutu wa iye amene ali wolekanitsidwa
ndi abale ake.
27Benjamini ndiye mmbulu wakulusalusa;
m'mamawa adzadya chomotola,
madzulo adzagawa zofunkha.
28Awa onse ndiwo mafuko khumi ndi awiri a Israele: izo ndizo zomwe ananena kwa iwo atate wao nawadalitsa; yense monga mdalitso wake anawadalitsa. 29#Gen. 25.8; 47.30; 49.33; 50.13Ndipo analangiza iwo nati kwa iwo, Ine nditi ndisonkhanizidwe kwa anthu a mtundu wanga; mundiike ine pamodzi ndi makolo anga m'phanga lili m'munda wa Efuroni Muhiti, 30m'phanga lili m'munda wa Makipela, umene uli patsogolo pa Mamure, m'dziko la Kanani, limene Abrahamu analigula kwa Efuroni Muhiti pamodzi ndi munda, likhale poikira pake: 31#Gen. 23.19; 25.9; Mac. 7.16pamenepo anaika Abrahamu ndi Sara mkazi wake; pamenepo anaika Isaki ndi Rebeka mkazi wake: pamenepo ndinaika Leya: 32munda ndi phanga lili m'menemo, zinagulidwa kwa ana a Hiti 33Pamene Yakobo anatha kulangiza ana ake amuna, anafunya mapazi ake pakama, natsirizika, nasonkhanizidwa kwa anthu a mtundu wake.
Currently Selected:
GENESIS 49: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

:
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi