GENESIS 7
7
Nowa ndi banja lake alowa m'chingalawa
1Ndipo anati Yehova kwa Nowa, Talowani, iwe ndi akunyumba ako onse m'chingalawamo; chifukwa ndakuona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m'mbadwo uno. 2Nyama zonse zodyedwa udzitengereko wekha zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yamphongo ndi yaikazi yake; ndi nyama zosadyedwa ziwiriziwiri yamphongo ndi yaikazi yake. 3Ndiponso mbalame za kumlengalenga zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yaimuna ndi yaikazi, kuti mbeu ikhale ndi moyo pa dziko lonse lapansi. 4Pakuti akapita masiku asanu ndi awiri Ine ndidzavumbitsa mvula pa dziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku; ndi zinthu zamoyo zonse zomwe ndazipanga ndidzaziononga pa dziko lapansi. 5Ndipo anachita Nowa monga mwa zonse anamlamulira iye Yehova.
6Ndipo Nowa anali wa zaka mazana asanu ndi limodzi, pamene chigumula cha madzi chinali pa dziko lapansi. 7#Mat. 24.38Ndipo analowa Nowa ndi ana ake ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake m'chingalawamo, chifukwa cha madzi a chigumula. 8Nyama zodyedwa ndi nyama zosadyedwa, ndi mbalame, ndi zonse zokwawa pansi, 9zinalowa ziwiriziwiri kwa Nowa m'chingalawamo, yamphongo ndi yaikazi, monga momwe Mulungu anamlamulira Nowa. 10Ndipo panali pamene anapita masiku asanu ndi awiri, madzi a chigumula anali pa dziko lapansi. 11#Mala. 3.10Chaka cha mazana asanu ndi limodzi cha moyo wa Nowa, mwezi wachiwiri, tsiku la khumi ndi asanu ndi awiri la mwezi, tsiku lomwelo akasupe onse a madzi aakulu anasefuka, ndi mazenera a kumwamba anatseguka. 12Ndipo mvula inali pa dziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku. 13Tsiku lomwelo analowa m'chingalawamo Nowa, ndi Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti, ana a Nowa, ndi mkazi wake wa Nowa, ndi akazi atatu a ana ake pamodzi nao: 14iwo, ndi zamoyo zonse monga mwa mitundu yao, ndi zinyama zonse monga mwa mitundu yao, zokwawa zonse zokwawa pa dziko lapansi monga mwa mitundu yao, ndi zouluka zonse monga mwa mitundu yao, ndi mbalame zonse za mitundumitundu. 15Ndipo zinalowa kwa Nowa m'chingalawamo ziwiriziwiri zamoyo zonse, m'mene muli mpweya wa moyo. 16Zimene zinalowazo, zinalowa yamphongo ndi yaikazi zamoyo zonse, monga momwe Mulungu anamlamulira iye: ndipo Yehova anamtsekera iye. 17Ndipo chigumula chinali pa dziko lapansi masiku makumi anai: ndipo madzi anachuluka natukula chingalawa, ndipo chinakwera pamwamba pa dziko lapansi. 18Ndipo madzi anapambana, nachuluka ndithu pa dziko lapansi, ndipo chingalawa chinayandama pamadzi. 19Ndipo madzi anapambana ndithu pa dziko lapansi; anamizidwa mapiri aatali onse amene anali pansi pa thambo lonse. 20Madzi anapambana ndithu nakwera mikono khumi ndi isanu: namizidwa mapiri. 21#2Pet. 3.6Ndipo zinafa zamoyo zonse zoyenda pa dziko lapansi, zouluka, ndi nyama, ndi zamoyo, ndi zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi, ndi anthu onse: 22zonse zimene m'mphuno zao munali mpweya wa mzimu wa moyo, zonse zinali pamtunda, zinafa. 23#2Pet. 2.5Ndipo zinaonongedwa zamoyo zonse zimene zinali pa dziko lapansi, anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndipo zinaonongedwa pa dziko lapansi: anatsala Nowa yekha ndi amene anali pamodzi naye m'chingalawa. 24Ndipo anapambana madzi pa dziko lapansi masiku zana kudza makumi asanu.
Currently Selected:
GENESIS 7: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: