YouVersion Logo
Search Icon

LUKA 1

1
1Popeza ambiri anayesa kulongosola nkhani ya zinthu zinachitika pakati pa ife, 2#Yoh. 15.27; Aheb. 2.3monga anazipereka kwa ife iwo amene anakhala mboni ndi atumiki a mau, 3#Mac. 1.1kuyambira pachiyambi, ndinayesa nkokoma inenso, amene ndinalondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira pachiyambi, kulembera kwa iwe tsatanetsatane, Teofilo wabwinotu iwe; 4#Yoh. 20.31kuti udziwitse zoona zake za mau amene unaphunzira.
Aneneratu za kubadwa kwa Yohane
5 # 1Mbi. 24.10; Mat. 2.1 Masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali munthu wansembe, dzina lake Zekariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wake wa ana akazi a fuko la Aroni, dzina lake Elizabeti. 6Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa. 7Ndipo analibe mwana, popeza Elizabeti anali wouma, ndipo onse awiri anakalamba.
8 # 1Mbi. 24.19 Ndipo panali, pakuchita iye ntchito yakupereka nsembe m'dongosolo la gulu lake, pamaso pa Mulungu, 9monga mwa machitidwe a kupereka nsembe, adamgwera maere akufukiza zonunkhira polowa iye m'Kachisi wa Ambuye. 10#Lev. 16.17Ndipo khamu lonse la anthu linalikupemphera kunja nthawi ya zonunkhira. 11Ndipo anamuonekera iye mngelo wa Ambuye, naimirira kudzanja lamanja la guwa la nsembe la zonunkhira. 12Ndipo Zekariya anadabwa pamene anamuona, ndipo mantha anamgwira. 13#Luk. 1.60, 63Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zekariya, chifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane. 14#Luk. 1.58Ndipo udzakhala nako kukondwera ndi msangalalo; ndipo anthu ambiri adzakondwera pa kubadwa kwake. 15#Yer. 1.5; Agal. 1.15Pakuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena kachasu; nadzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, kuyambira asanabadwe. 16Ndipo iye adzatembenuzira ana a Israele ambiri kwa Ambuye Mulungu wao. 17#Mala. 4.5-6Ndipo adzamtsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka. 18#Gen. 17.17Ndipo Zekariya anati kwa mngelo, Ndidzadziwitsa ichi ndi chiyani? Pakuti ndine nkhalamba, ndipo zaka zake za mkazi wanga zachuluka. 19Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Ine ndine Gabriele, woimirira pamaso pa Mulungu; ndipo ndinatumidwa kwa iwe kudzalankhula nawe, ndi kuuza iwe uthenga uwu wabwino. 20Ndipo taona, udzakhala wotonthola ndi wosakhoza kulankhula, kufikira tsiku limene zidzachitika izi, popeza kuti sunakhulupirira mau anga, amene adzakwanitsidwa pa nyengo yake. 21Ndipo anthu analikulindira Zekariya, nazizwa ndi kuchedwa kwake m'Kachisimo. 22Koma m'mene iye anatulukamo, sanatha kulankhula nao; ndipo anazindikira kuti iye adaona masomphenya m'Kachisimo. Ndipo iye analinkukodola iwo, nakhalabe wosalankhula. 23Ndipo kunali, pamene masiku a utumiki wake anamalizidwa, anamuka kunyumba kwake.
24Ndipo atatha masiku awa, Elizabeti mkazi wake anaima; nadzibisa miyezi isanu, nati, 25#Gen. 30.23Ambuye wandichitira chotero m'masiku omwe Iye anandipenyera, kuchotsa manyazi anga pakati pa anthu.
Aneneratu za kubadwa kwa Yesu
26Ndipo mwezi wachisanu ndi chimodzi mngelo Gabriele anatumidwa ndi Mulungu kunka kumudzi wa ku Galileya dzina lake Nazarete, 27#Mat. 1.18kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la Davide; ndipo dzina lake la namwaliyo ndilo Maria. 28#Ower. 6.12Ndipo pakulowa mngelo anati kwa iye, Tikuoneni, wochitidwa chisomo, Ambuye ali ndi iwe. 29Koma iye ananthunthumira ndi mau awa, nasinkhasinkha kulonjera uku nkutani. 30Ndipo mngelo anati kwa iye, Usaope, Maria; pakuti wapeza chisomo ndi Mulungu. 31#Yes. 7.14; Luk. 2.21Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu. 32#Yes. 9.6-7; Mrk. 5.7Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake: 33#Yes. 9.6-7ndipo Iye adzachita ufumu pa banja la Yakobo kunthawi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha. 34Koma Maria anati kwa mngelo, Ichi chidzachitika bwanji, popeza ine sindidziwa mwamuna? 35#Mat. 1.20; 14.33; Yoh. 1.34, 49; Aro. 1.3-4Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu. 36Ndipo taona, Elizabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna m'ukalamba wake; ndipo mwezi uno uli wachisanu ndi chimodzi wa iye amene ananenedwa wouma. 37#Gen. 18.14; Mat. 19.26; Aro. 4.21Chifukwa palibe mau amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu. 38Ndipo Maria anati, Onani, mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa mau anu. Ndipo mngelo anachoka kwa iye.
Maria acheza kwa Elizabeti
39Ndipo Maria ananyamuka masiku amenewa, namuka ndi changu kudziko la mapiri kumudzi wa Yuda; 40nalowa m'nyumba ya Zekariya, nalonjera Elizabeti. 41Ndipo panali pamene Elizabeti anamva kulonjera kwake kwa Maria, mwana wosabadwayo anatsalima m'mimba mwake; ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera; 42#Luk. 1.28nakweza mau ndi mfuu waukulu, nati, Wodalitsika iwe mwa akazi, ndipo chodalitsika chipatso cha mimba yako. 43Ndipo ichi chichokera kuti kudza kwa ine, kuti adze kwa ine amake wa Ambuye wanga? 44Pakuti ona, pamene mau a moni wako analowa m'makutu anga, mwana anatsalima ndi msangalalo m'mimba mwanga. 45Ndipo wodala ali iye amene anakhulupirira; chifukwa zidzachitidwa zinthu zimene Ambuye analankhula naye.
Nyimbo ya Maria
46 # 1Sam. 2.1 Ndipo Maria anati,
Moyo wanga ulemekeza Ambuye,
47ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,
48chifukwa Iye anayang'anira umphawi wa mdzakazi wake;
pakuti taonani, kuyambira tsopano,
anthu a mibadwo yonse adzanditchula ine wodala.
49 # Mas. 111.9 Chifukwa Iye Wamphamvuyo anandichitira ine zazikulu;
ndipo dzina lake lili loyera.
50 # Mas. 103.17-18 Ndipo chifundo chake chifikira anthu a mibadwomibadwo
pa iwo amene amuopa Iye.
51 # Mas. 33.10 Iye anachita zamphamvu ndi mkono wake;
Iye anabalalitsa odzitama ndi mlingaliro wa mtima wao.
52Iye anatsitsa mafumu pa mipando yao yachifumu,
ndipo anakweza aumphawi.
53 # Mas. 107.9 Anawakhutitsa anjala ndi zinthu zabwino,
ndipo eni chuma anawachotsa opanda kanthu.
54Anathangatira Israele mnyamata wake,
kuti akakumbukire chifundo,
55 # Gen. 17.19 (Monga analankhula kwa makolo athu)
kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake kunthawi yonse.
56Ndipo Maria anakhala ndi iye ngati miyezi itatu, nabweranso kunyumba kwake.
Kubadwa kwa Yohane Mbatizi
57Ndipo inakwanira nthawi ya Elizabeti, ya kubala kwake, ndipo anabala mwana wamwamuna. 58#Luk. 1.14Ndipo anansi ake ndi abale ake anamva kuti Ambuye anakulitsa chifundo chake pa iye; nakondwera naye pamodzi. 59#Gen. 17.12Ndipo panali tsiku lachisanu ndi chitatu iwo anadza kudzadula kamwanako; ndipo akati amutche dzina la atate wake Zekariya. 60#Luk. 1.13Ndipo amake anayankha, kuti, Iai; koma adzatchedwa Yohane. 61Ndipo iwo anati kwa iye, Palibe wina wa abale ako amene atchedwa dzina ili. 62Ndipo anakodola atate wake, afuna amutche dzina liti? 63Ndipo iye anafunsa cholemberapo, nalemba, kuti, Dzina lake ndi Yohane. Ndipo anazizwa onse. 64#Luk. 1.20Ndipo pomwepo panatseguka pakamwa pake, ndi lilime lake linamasuka, ndipo iye analankhula, nalemekeza Mulungu. 65Ndipo panagwa mantha pa iwo onse akukhala oyandikana nao; ndipo analankhulalankhula nkhani izi zonse m'dziko lonse la mapiri a Yudeya. 66#Mas. 89.20-21Ndipo onse amene anazimva anazisunga m'mtima mwao, nanena, Nanga mwana uyu adzakhala wotani? Pakuti dzanja la Ambuye linakhala pamodzi ndi iye.
Nyimbo ya Zekariya
67Ndipo atate wake Zekariya anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nanenera za Mulungu, nati,
68 # Eks. 3.16-17 Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israele;
chifukwa Iye anayang'ana, nachitira anthu ake chiombolo.
69Ndipo Iye anatikwezera ife nyanga ya chipulumutso,
mwa fuko la Davide mwana wake.
70 # Yer. 23.5-6 Monga Iye analankhula ndi m'kamwa
mwa aneneri ake oyera mtima, akale lomwe,
71chipulumutso cha adani athu,
ndi pa dzanja la anthu onse amene atida ife.
72 # Mas. 105.8-9 Kuchitira atate athu chifundo,
ndi kukumbukira pangano lake lopatulika;
73chilumbiro chimene Iye anachilumbira
kwa Abrahamu atate wathu.
74 # Aro. 6.18, 22 Kutipatsa ife kuti titalanditsidwa kudzanja la adani athu,
tidzamtumikira Iye, opanda mantha,
75 # Aro. 6.18, 22 m'chiyero ndi chilungamo pamaso pake, masiku athu onse.
76 # Mat. 3.1-3; 11.9 Eya, ndipo iwetu kamwanawe,
udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu;
pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake.
77 # Mrk. 1.4 Kuwapatsa anthu ake adziwitse chipulumutso,
ndi makhululukidwe a machimo ao,
78chifukwa cha mtima wachifundo wa Mulungu wathu.
M'menemo mbandakucha wa kumwamba udzatichezera ife.
79 # Yes. 9.2; Mat. 4.16 Kuwalitsira iwo okhala mumdima ndi mthunzi wa imfa;
kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere.
80 # Mat. 4.16 Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israele.

Currently Selected:

LUKA 1: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in