LUKA 15
15
Fanizo la nkhosa yosokera
(Mat. 18.12-14)
1 #
Mat. 9.10
Koma amisonkho onse ndi anthu ochimwa analikumyandikira kudzamva Iye. 2#Mac. 11.3Ndipo Afarisi ndi alembi anadandaula nati, Uyu alandira anthu ochimwa, nadya nao.
3Koma anati kwa iwo fanizo ili, nanena, 4#Mat. 18.12Munthu ndani wa inu ali nazo nkhosa makumikhumi, ndipo pakutayika imodzi ya izo, sasiya nanga m'chipululu zinazo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai, nalondola yotayikayo kufikira aipeza? 5Ndipo pamene adaipeza, aisenza pa mapewa ake wokondwera. 6Ndipo pakufika kunyumba kwake amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena nao, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza nkhosa yanga yotayikayo. 7#Luk. 5.32Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala chimwemwe Kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.
Fanizo la ndalama yotayika
8Kapena mkazi wanji ali nazo ndalama zasiliva khumi, ngati itayika imodzi, sayatsa nyali, nasesa m'nyumba yake, nafunafuna chisamalire kufikira akaipeza? 9Ndipo m'mene aipeza amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza ndalama ndidatayayo. 10Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.
Fanizo la mwana wolowerera
11Ndipo Iye anati, Munthu wina anali ndi ana amuna awiri; 12ndipo wamng'onoyo anati kwa atate wake, Atate, ndigawirenitu zanga za pa chuma chanu. Ndipo iye anawagawira za moyo wake. 13Ndipo pakupita masiku owerengeka mwana wamng'onoyo anasonkhanitsa zonse, napita ulendo wake kudziko lakutali; ndipo komweko anamwaza chuma chake ndi makhalidwe a chitayiko. 14Ndipo pamene anatha zake zonse, panakhala njala yaikulu m'dziko muja, ndipo iye anayamba kusowa. 15Ndipo anamuka nadziphatikiza kwa mfumu imodzi ya dziko lija; ndipo uyu anamtumiza kubusa kwake kukaweta nkhumba. 16Ndipo analakalaka kukhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumba zimadya, ndipo palibe munthu anamninkha kanthu. 17Koma m'mene anakumbukira mumtima, anati, Antchito olipidwa ambiri a atate wanga ali nacho chakudya chochuluka, ndipo ine ndionongeke kuno ndi njala? 18Ndidzanyamuka ndipite kwa atate wanga, ndipo ndidzanena naye, Atate, ndinachimwira Kumwamba ndi pamaso panu; 19sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu; mundiyese ine ngati mmodzi wa antchito anu. 20Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wake. Koma pakudza iye kutali atate wake anamuona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsompsonetsa. 21#Mas. 51.4Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinachimwira Kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu. 22Koma atateyo ananena kwa akapolo ake, Tulutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumveke; ndipo mpatseni mphete kudzanja lake ndi nsapato kumapazi ake; 23ndipo idzani naye mwanawang'ombe wonenepa, mumuphe, ndipo tidye, tisekere; 24#Aef. 2.1; 5.14chifukwa mwana wanga uyu anali wakufa, ndipo akhalanso wamoyo; anali wotayika, ndipo wapezedwa. Ndipo anayamba kusekera.
25Koma mwana wake wamkulu anali kumunda. Ndipo pakubwera iye ndi kuyandikira kunyumba, anamva kuimba ndi kuvina. 26Ndipo anaitana mmodzi wa anyamata, namfunsa, Zinthu izi nzotani? 27Ndipo uyu anati kwa iye, Mng'ono wako wafika; ndipo atate wako anapha mwanawang'ombe wonenepa, chifukwa anamlandira iye wamoyo. 28Koma anakwiya, ndipo sanafune kulowamo. Ndipo atate wake anatuluka namdandaulira. 29Koma anayankha nati kwa atate wake, Onani, ine ndinakhala kapolo wanu zaka zambiri zotere, ndipo sindinalakwira lamulo lanu nthawi iliyonse; ndipo simunandipatsa ine kamodzi konse mwanawambuzi, kuti ndisekere ndi abwenzi anga. 30Koma pamene anadza mwana wanu uyu, wakutha zamoyo zanu ndi akazi achiwerewere, munamphera iye mwanawang'ombe wonenepa. 31Koma iye ananena naye, Mwana wanga, iwe uli ndine nthawi zonse, ndipo zanga zonse zili zako. 32#Luk. 15.24Koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwerera: chifukwa mng'ono wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyo; anatayika, ndipo wapezeka.
Currently Selected:
LUKA 15: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: