LUKA 20
20
Amfunsa Yesu za ulamuliro
(Mat. 21.23-27; Mrk. 11.27-33)
1Ndipo kunali lina la masiku ao m'mene Iye analikuphunzitsa anthu m'Kachisi, ndi kulalikira Uthenga Wabwino, adamdzera ansembe aakulu ndi alembi pamodzi ndi akulu; 2#Mac. 4.7; 7.27ndipo anati, nanena naye, Mutiuze muchita izi ndi ulamuliro wotani? Kapena ndani iye amene anakupatsani ulamuliro umene? 3Ndipo anayankha, nati kwa iwo, Ndidzakufunsani mau Inenso; mundiuze: 4Ubatizo wa Yohane unachokera Kumwamba kodi, kapena kwa anthu? 5Ndipo anatsutsana mwa okha, nanena, Ngati tinena uchokera Kumwamba; adzati, Simunamkhulupirira chifukwa ninji? 6#Mat. 14.5Ndiponso, tikanena, Uchokera kwa anthu; anthu onse adzatiponya miyala: pakuti akopeka mtima, kuti Yohane ali mneneri. 7Ndipo anayankha kuti sadziwa kumene uchokera. 8Ndipo Yesu anati kwa iwo Ndingakhale Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndichita nao zinthu izi.
Fanizo la olima munda wamphesa
(Mat. 21.33-46; Mrk. 12.1-12)
9Ndipo Iye anayamba kunena kwa anthu fanizo ili: Munthu analima munda wamphesa, naukongoletsa kwa olima munda, nanka kudziko lina, nagonerako nthawi yaikulu. 10Ndipo pa nyengo ya zipatso anatumiza kapolo wake kwa olima mundawo, kuti ampatseko chipatso cha mundawo; koma olimawo anampanda, nambweza wopanda kanthu. 11Ndipo anatumizanso kapolo wina; ndipo iyenso anampanda, namchitira chipongwe, nambweza, wopanda kanthu. 12Ndipo anatumizanso wina wachitatu; ndipo iyenso anamlasa, namtaya kunja. 13Ndipo mwini mundawo anati, Ndidzachita chiyani? Ndidzatuma mwana wanga amene ndikondana naye; kapena akamchitira iye ulemu. 14Koma olimawo, pamene anamuona, anauzana wina ndi mnzake, nati, Uyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe, kuti cholowa chake chikhale chathu. 15Ndipo anamponya kunja kwa mundawo, namupha. Pamenepo mwini munda wamphesawo adzawachitira chiyani? 16Iye adzafika nadzaononga olima munda aja, nadzapatsa munda kwa ena. Ndipo pamene iwo anamva, anati, Musatero iai! 17#Mas. 118.22Koma Iye anawapenyetsa iwo, nati, Nchiyani ichi chinalembedwa,
Mwala umene anaukana omanga nyumba,
womwewu unakhala mutu wa pangodya.
18Munthu yense wakugwa pa mwala uwu, adzaphwanyika; koma iye amene udzamgwera, udzamupha.
Za msonkho
(Mat. 22.15-22; Mrk. 12.13-17)
19Ndipo alembi ndi ansembe aakulu anafunafuna kumgwira ndi manja nthawi yomweyo; ndipo anaopa anthu; pakuti anazindikira kuti ananenera pa iwo fanizo ili. 20Ndipo anamyang'anira, natumiza ozonda, amene anadzionetsera ngati olungama mtima, kuti akamkole pa mau ake, kotero kuti akampereke Iye ku ukulu ndi ulamuliro wa kazembe. 21#Mrk. 12.14Ndipo anamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi, ife tidziwa kuti munena ndi kuphunzitsa kolunjika, ndi kusasamalira nkhope ya munthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu koonadi; 22kodi kuloledwa kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena iai? 23Koma Iye anazindikira chinyengo chao, nati kwa iwo, 24Tandionetsani Ine rupiya latheka. Chithunzithunzi ndi cholemba chake ncha yani? Anati iwo, Cha Kaisara. 25Ndipo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake perekani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu. 26Ndipo sanakhoze kugwira mauwo pamaso pa anthu; ndipo anazizwa ndi kuyankha kwake, nakhala chete.
Yesu ayankha Asaduki za kuuka kwa akufa
(Mat. 22.23-33; Mrk. 12.18-27)
27Ndipo anadza kwa Iye Asaduki ena, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; ndipo anamfunsa Iye, 28#Deut. 25.5nanena, Mphunzitsi, Mose anatilembera ife, kuti mbale wake wa munthu akafa, wokhala ndi mkazi, ndipo alibe mwana iye, mbale wake adzakwatira mkaziyo, nadzamuukitsira mbale wake mbeu. 29Tsono panali abale asanu ndi awiri; ndipo woyamba anakwatira mkazi, nafa wopanda mwana; 30ndipo wachiwiri, 31ndi wachitatu anamtenga mkaziyo; ndipo choteronso asanu ndi awiri onse, sanasiye mwana, namwalira. 32Pomalizira anamwaliranso mkaziyo. 33Potero m'kuuka iye adzakhala mkazi wa yani wa iwo? Pakuti asanu ndi awiriwo adamkwatira iye. 34Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ana a dziko lapansi akwatira nakwatiwa: 35koma iwo akuyesedwa oyenera kufikira dziko lijalo, ndi kuuka kwa akufa, sakwatira kapena kukwatiwa. 36#Aro. 8.23; 1Ako. 15.42, 49, 52; 1Yoh. 3.2Pakuti sangathe kufanso nthawi zonse; pakuti afanafana ndi angelo; ndipo ali ana a Mulungu, popeza akhala ana a kuuka kwa akufa. 37#Eks. 3.6Koma za kuti anthu akufa auka, anasonyeza ngakhale Mose, pa Chitsamba chija, pamene iye amtchulira Ambuye, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo. 38#Aro. 6.10-11Ndipo Iye sakhala Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: pakuti anthu onse akhala ndi moyo kwa Iye. 39Ndipo alembi ena anayankha nati, Mphunzitsi, mwanena bwino. 40Pakuti sanalimbenso mtima kumfunsa Iye kanthu kena.
Khristu mwana wa Davide
(Mat. 22.41-46; Mrk. 12.35-37)
41Koma Iye anati kwa iwo, Amanena bwanji kuti Khristuyo ndiye mwana wa Davide? 42#Mas. 110.1; Mac. 2.34-35Pakuti Davide yekha anena m'buku la Masalmo,
Ambuye ananena kwa Ambuye wanga,
ukhale pa dzanja langa lamanja,
43kufikira Ine ndikaika adani ako pansi pa mapazi ako.
44Chotero Davide anamtchula Iye Ambuye, ndipo nanga ali mwana wake bwanji?
Ophunzira achenjere nao alembi
(Mat. 23.1-39; Mrk. 12.38-40)
45Ndipo pamene anthu onse analinkumva Iye, anati kwa ophunzira, 46#Luk. 11.43Chenjerani nao alembi, amene afuna kuyendayenda ovala miinjiro, nakonda kupatsidwa moni m'misika, ndi mipando yaulemu m'sunagoge, ndi malo aulemu pamaphwando; 47amene aononga nyumba za akazi amasiye, ndipo monyenga achita mapemphero atali; amenewo adzalandira kulanga koposa.
Currently Selected:
LUKA 20: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: