LUKA 9
9
Yesu atuma ophunzira ake kukalalikira mau
(Mat. 10.1-14; Mrk. 6.7-13)
1Ndipo Iye anaitana pamodzi khumi ndi awiriwo nawapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse, ndi zakuchiritsa nthenda. 2#Mrk. 6.12Ndipo anawatuma kukalalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuchiritsa anthu odwala. 3#Mrk. 6.8Ndipo Iye anati kwa iwo, Musanyamule kanthu ka paulendo, kapena ndodo, kapena thumba, kapena mkate, kapena ndalama; ndipo musakhale nao malaya awiri. 4#Mrk. 6.10Ndipo m'nyumba iliyonse mukalowemo, khalani komweko, ndipo muzikachokera kumeneko. 5#Mac. 13.51Ndipo onse amene sakakulandireni inu, m'mene mutuluka m'mudzi womwewo, sansani fumbi la pa mapazi anu, likhale mboni ya paiwo. 6#Mrk. 6.12Ndipo iwo anatuluka, napita m'midzi yonse, ndi kulalikira Uthenga Wabwino, ndi kuchiritsa ponse.
Herode ndi Yohane Mbatizi
(Mat. 14.1-12; Mrk. 6.14-29; Luk. 3.19-20)
7Ndipo Herode chiwangacho anamva mbiri yake ya zonse zinachitika; ndipo inamthetsa nzeru, chifukwa ananena anthu ena, kuti Yohane anauka kwa akufa; 8koma ena, kuti Eliya anaoneka; ndipo ena, kuti mneneri wina wa akale aja anauka. 9#Luk. 23.8Ndipo Herode anati, Yohane ndinamdula mutu ine; koma uyu ndani ndikumva zotere za iye? Ndipo anafunafuna kumuona Iye.
Yesu achulukitsa mikate
(Mat. 14.13-21; Mrk. 6.30-44; Yoh. 6.1-14)
10Ndipo atabwera atumwi, anamfotokozera Iye zonse anazichita. Ndipo Iye anawatenga, napatuka nao pa okha kunka kumudzi dzina lake Betsaida. 11Koma unyinji wa anthu, pamene anadziwa, anamtsata Iye; ndipo Iye anawalandira, nalankhula nao za Ufumu wa Mulungu, nachiritsa amene anasowa kuchiritsidwa. 12#Yoh. 6.1, 5; Luk. 7.14Koma dzuwa lidapendeka; ndipo khumi ndi awiriwo anadza, nati kwa Iye, Tauzani makamu a anthu amuke, kuti apite kumidzi yoyandikira ndi kumilaga, kukafuna pogona, ndi kupeza zakudya; chifukwa tili kumalo achipululu kuno. 13Koma anati kwa iwo, Muwapatse kudya ndinu. Koma anati, Ife tilibe mikate, koma isanu yokha, ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya. 14Pakuti anali amuna ngati zikwi zisanu. Koma Iye anati kwa ophunzira ake, Khalitsani iwo pansi magulumagulu, ngati makumi asanuasanu. 15Ndipo anatero, nawakhalitsa pansi onsewo. 16Ndipo Iye, m'mene anatenga mikate isanu ija ndi nsomba ziwiri anayang'ana kumwamba, nazidalitsa, nanyema, napatsa ophunzira apereke kwa anthuwo. 17Ndipo anadya, nakhuta onsewo; natola makombo, madengu khumi ndi awiri.
Petro avomereza Khristu
(Mat. 16.13-23; Mrk. 8.27-33; Yoh. 6.66-69)
18Ndipo kunali, pamene Iye anali kupemphera padera, ophunzira anali naye; ndipo anawafunsa iwo, kuti, Makamuwo a anthu anena kuti Ine ndine yani? 19#Mat. 14.2Ndipo anayankha nati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndi ena, kuti anauka mmodzi wa aneneri akale. 20#Yoh. 6.69Ndipo anati kwa iwo, Koma inu munena kuti Ine ndine yani? Ndipo anayankha Petro, nati, Khristu wa Mulungu. 21Ndipo Iye anawauzitsa iwo, nalamulira kuti asanene ichi kwa munthu aliyense; 22nati, Kuyenera kuti Mwana wa Munthu amve zowawa zambiri, ndi kukanidwa ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi, ndi kuphedwa, ndi kuuka tsiku lachitatu.
Za kusenza mtanda
(Mat. 16.24-28; Mrk. 8.34—9.1; Yoh. 12.25)
23Ndipo Iye ananena kwa onse, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake tsiku ndi tsiku, nanditsate Ine. 24Pakuti amene aliyense akafuna kupulumutsa moyo wake, iye adzautaya; koma amene aliyense akataya moyo wake chifukwa cha Ine, iye adzaupulumutsa uwu. 25Pakuti munthu apindulanji, akadzilemezera dziko lonse lapansi nadzitayapo, kapena kulipapo moyo wake? 26#Mat. 10.33; 2Tim. 2.12Pakuti amene aliyense adzachita manyazi chifukwa cha Ine ndi mau anga, Mwana wa Munthu adzachita manyazi chifukwa cha iye, pamene adzafika ndi ulemerero wake ndi wa Atate, ndi wa angelo oyera. 27Koma Ine ndinena ndi inu zoonadi, Kuli ena a iwo akuimirira pano, amene sadzalawatu imfa, kufikira kuti adzaona Ufumu wa Mulungu.
Mawalitsidwe a Yesu paphiri
(Mat. 17.1-13; Mrk. 9.2-13)
28Ndipo pamene padatha ngati masiku asanu ndi atatu atanena mau amenewa, Iye anatenga Petro ndi Yohane ndi Yakobo apite naye, nakwera m'phiri kukapemphera. 29Ndipo m'kupemphera kwake, maonekedwe a nkhope yake anasandulika, ndi chovala chake chinayera ndi kunyezimira. 30Ndipo onani, analikulankhulana naye amuna awiri, ndiwo Mose ndi Eliya; 31amene anaonekera m'ulemerero, nanena za kumuka kwake kumene Iye ati adzatsiriza ku Yerusalemu. 32Koma Petro ndi iwo anali naye analemedwa ndi tulo; koma m'mene anayera m'maso ndithu, anaona ulemerero wake, ndi amuna awiriwo akuimirira ndi Iye. 33Ndipo panali polekana iwo aja ndi Iye, Petro anati kwa Yesu, Ambuye, nkwabwino kuti tili pano; ndipo timange misasa itatu, umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya; wosadziwa iye chimene alikunena. 34Ndipo akadalankhula izi, unadza mtambo, nuwaphimba iwo; ndipo anaopa pakulowa iwo mumtambo. 35#Mat. 3.17; Mac. 3.22Ndipo munatuluka mau mumtambo, nanena, Uyu ndiye Mwana wanga, wosankhidwayo; mverani Iye. 36Ndipo pakutero mauwo, Yesu anapezedwa ali yekha. Ndipo iwo anakhala chete, ndipo sanauze munthu aliyense masiku aja kanthu konse ka izo anaziona.
Achiritsa mwana wodwala khunyu
(Mat. 17.14-23; Mrk. 9.14-32)
37Ndipo panali, m'mawa mwake, atatsika m'phiri, khamu lalikulu la anthu linakomana naye. 38Ndipo onani, anafuula munthu wa m'khamulo, nanena, nati, Mphunzitsi, ndikupemphani, yang'anirani mwana wanga; chifukwa ndiye mmodzi yekha wa ine: 39ndipo onani, umamgwira iye mzimu, nafuula modzidzimuka; ndipo umamng'amba iye ndi kumchititsa thovu pakamwa, nuchoka pa iye mwa unyenzi, numgola iye. 40Ndipo ndinapempha ophunzira anu kuti autulutse; koma sanathe. 41Ndipo Yesu anayankha, nati, Ha! Obadwa inu osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji, ndi kulekerera inu? Idza naye kuno mwana wako. 42Ndipo akadadza iye, chiwandacho chinamgwetsa, ndi kumng'ambitsa. Koma Yesu anadzudzula mzimu wonyansawo, nachiritsa mnyamata, nambwezera iye kwa atate wake. 43Ndipo onse anadabwa pa ukulu wake wa Mulungu. Koma pamene onse analikuzizwa ndi zonse anazichita, Iye anati kwa ophunzira ake, 44Alowe mau amenewa m'makutu anu; pakuti Mwana wa Munthu adzaperekedwa m'manja a anthu. 45#Mrk. 9.32Koma iwo sanadziwitse mau awa, ndipo anabisidwa kwa iwo, kuti asawadziwe; ndipo anaopa kumfunsa za mau awa.
Wamkulu m'Ufumu wa Kumwamba
(Mat. 18.1-5; Mrk. 9.33-37)
46Ndipo anayamba kutsutsana kuti wamkulu mwa iwo ndani. 47Koma Yesu pakuona kutsutsana kwa mitima yao, anatenga kamwana, nakaimika pambali pake, nati kwa iwo, 48#Mat. 10.40; 23.11-12; Mrk. 9.37Amene aliyense akalandire kamwana aka m'dzina langa alandira Ine; ndipo amene andilandira Ine alandira Iye amene anandituma Ine; pakuti iye wakukhala wamng'onong'ono wa inu nonse, yemweyu ndiye wamkulu.
Osatsutsana nafe athandizana nafe
(Mrk. 9.38-40)
49Ndipo Yohane anayankha nati, Ambuye, tinaona wina alikutulutsa ziwanda m'dzina lanu; ndipo tinamletsa, chifukwa satsatana nafe. 50Koma Yesu anati kwa iye, Musamletse, pakuti iye amene satsutsana nanu athandizana nanu.
Asamariya amkaniza Yesu
51 #
Mrk. 16.19; Mac. 1.2 Ndipo panali, pamene anayamba kukwanira masiku akuti alandiridwe Iye kumwamba, Yesu anatsimikiza kuloza nkhope yake kunka ku Yerusalemu, 52natumiza amithenga patsogolo pake; ndipo ananka, nalowa m'mudzi wa Asamariya, kukamkonzera Iye malo. 53Ndipo iwo sanamlandire Iye, chifukwa nkhope yake inali yoloza kunka ku Yerusalemu. 54Ndipo pamene ophunzira ake Yakobo ndi Yohane anaona, anati, Ambuye, Kodi mufuna kuti ife tiuze moto utsike kumwamba ndi kuwanyeketsa iwo? 55Koma Iye anapotoloka nawadzudzula. 56Ndipo anapita kumudzi kwina.
Matsatidwe a Yesu
(Mat. 8.18-22)
57Ndipo m'mene iwo analikuyenda m'njira, munthu anati kwa Iye, Ine ndidzakutsatani kumene kulikonse mukapitako. 58Ndipo Yesu anati kwa iye, Nkhandwe zili nazo nkhwimba, ndi mbalame za kumwamba zisa, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu. 59#Mat. 8.21Ndipo anati kwa munthu wina, Unditsate Ine. Koma iye anati, Mundilole ine, Ambuye, ndithange ndamuka kuika maliro a atate wanga. 60Koma anati kwa iye, Leka akufa aike akufa a eni okha; koma muka iwe nubukitse mbiri yake ya Ufumu wa Mulungu. 61#1Maf. 19.20Ndipo winanso anati, Ambuye ndidzakutsatani Inu; koma muthange mwandilola kulawirana nao a kunyumba kwanga. 62#Afi. 3.13Koma Yesu anati kwa iye, Palibe munthu wakugwira chikhasu, nayang'ana za kumbuyo, ayenera Ufumu wa Mulungu.
Currently Selected:
LUKA 9: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: