YouVersion Logo
Search Icon

MARKO 14

14
Ansembe akulu achita chiwembu pa Yesu
(Mat. 26.1-5; Luk. 21.34-36)
1 # Yoh. 11.55 Ndipo popita masiku awiri kuli phwando la Paska ndi mikate yopanda chotupitsa; ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna momchitira chiwembu, ndi kumupha: 2pakuti anati, Pachikondwerero ai, kuti pangakhale phokoso la anthu.
Phwando la ku Betaniya
(Mat. 26.6-13; Yoh. 12.1-8)
3 # Luk. 7.37 Ndipo pakukhala Iye ku Betaniya m'nyumba ya Simoni wakhate, m'mene anaseama kudya, anadzapo mkazi ali nayo nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino a narido weniweni a mtengo wapatali; naswa nsupayo, nawatsanulira pamutu pake. 4Koma anakhalako ena anavutika mtima mwa iwo okha, ndi kuti, Mafutawo atayidwa chifukwa ninji? 5Pakuti mafuta amene akadagula marupiya atheka mazana atatu ndi mphamvu zake, ndi kupatsa aumphawi. Ndipo anadandaulira mkaziyo. 6Koma Yesu anati, Mlekeni, mumvutiranji? Wandichitira Ine ntchito yabwino. 7#Deut. 15.11Pakuti muli nao aumphawi pamodzi ndi inu masiku onse, ndipo paliponse pamene mukafuna mukhoza kuwachitira zabwino; koma Ine simuli nane masiku onse. 8Iye wachita chimene wakhoza; anandidzozeratu thupi langa ku kuikidwa m'manda. 9Ndipo ndithu ndinena ndi inu, Ponse pamene padzalalikidwa Uthenga Wabwino kudziko lonse lapansi, ichinso chimene anachita mkazi uyu chidzanenedwa, chikhale chonkumbukira nacho.
Yudasi apangana ndi ansembe aakulu
(Mat. 26.14-16; Luk. 22.3-6)
10Ndipo Yudasi Iskariote, ndiye mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anachoka napita kwa ansembe aakulu, kuti akampereke Iye kwa iwo. 11Ndipo pamene iwo anamva, anasekera, nalonjezana naye kuti adzampatsa ndalama. Ndipo iye anafunafuna pompereka Iye bwino.
Paska wotsiriza
(Mat. 26.17-25; Luk. 22.7-14; Yoh. 13.21-30)
12Ndipo tsiku loyamba la mikate yopanda chotupitsa, pamene amapha Paska, ophunzira ananena naye, Mufuna tinke kuti, tikakonze mkadyereko Paska? 13Ndipo anatuma awiri a ophunzira ake, nanena nao, Lowani m'mzinda, ndipo adzakomana nanu munthu wakusenza mtsuko wa madzi; mumtsate iye; 14ndipo kumene akalowako iye, munene naye mwini nyumba, Mphunzitsi anena, Chilikuti chipinda cha alendo changa, m'menemo ndikadye Paska ndi ophunzira anga? 15Ndipo iye yekha adzakusonyezani chipinda chapamwamba chachikulu choyalamo ndi chokonzedwa; ndipo m'menemo mutikonzere. 16Ndipo ophunzira anatuluka, nafika m'mzinda, napeza monga anati kwa iwo; ndipo anakonza Paska.
17Ndipo pofika madzulo anadza Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo. 18Ndipo pamene anaseama iwo kudya, Yesu anati, Ndithu ndinena ndi inu, Mmodzi wa inu adzandipereka Ine, ndiye wakudya ndi Ine pamodzi. 19Anayamba iwo kukhala ndi chisoni, ndi kunena naye mmodzimmodzi, kuti, Ndine kodi? 20Ndipo anati kwa iwo, Mmodzi wa khumi ndi awiriwo, ndiye wakusunsa pamodzi ndi Ine m'mbale. 21#Luk. 22.22Pakuti Mwana wa Munthu amukadi, monga kwalembedwa za Iye; koma tsoka munthuyo amene apereka Mwana wa Munthu! Kukadakhala bwino kwa munthu ameneyo ngati sakadabadwa iye.
Mgonero wa Ambuye
(Mat. 26.26-30; Luk. 22.15-20; 1Ako. 11.23-25)
22 # Luk. 22.19; 1Ako. 11.23-26 Ndipo pamene iwo analikudya, Iye anatenga mkate, ndipo pamene anadalitsa, ananyema, napereka kwa iwo, kuti, Tengani; thupi langa ndi ili. 23Ndipo anatenga chikho, ndipo pamene adayamika, anapereka kwa iwo; ndipo iwo onse anamweramo. 24Ndipo Iye anati kwa iwo, Ichi ndi mwazi wanga wa chipangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri. 25Ndipo ndinena nanu, Sindidzamwanso chipatso cha mpesa, kufikira tsiku lijalo, limene ndidzamwa icho chatsopano mu Ufumu wa Mulungu. 26Ndipo ataimba nyimbo, anatuluka, namuka kuphiri la Azitona.
Yesu achenjeza Petro
(Mat. 26.31-35; Luk. 22.31-34; Yoh. 13.36, 38)
27 # Zek. 13.7 Ndipo Yesu ananena nao, Mudzakhumudwa nonsenu; pakuti kwalembedwa,
Ndidzakantha mbusa, ndi nkhosa zidzamwazika.
28 # Mrk. 16.7 Komatu nditadzauka ndidzatsogolera inu ku Galileya. 29#Yoh. 13.37-38Koma Petro ananena naye, Angakhale adzakhumudwa onse, komatu ine iai. 30Ndipo Yesu ananena naye, Ndithu ndinena ndi iwe, kuti lero, usiku uno, tambala asanalire kawiri, udzandikana Ine katatu. 31Koma iye analimbitsa mau chilimbitsire, kuti, Ngakhale ndidzafa nanu, sindidzakana Inu. Ndipo onsewo anatero.
Getsemani
(Mat. 26.36-46; Luk. 22.39-46; Yoh. 18.1)
32Ndipo iwo anadza kumalo dzina lake Getsemani; ndipo ananena kwa ophunzira ake, Bakhalani pano, kufikira ndikapemphera. 33Ndipo anatenga pamodzi ndi Iye Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nayamba kudabwa kwambiri, ndi kusauka mtima ndithu. 34#Yoh. 12.27Ndipo ananena nao, Moyo wanga uli wa chisoni chambiri, kufikira imfa. Bakhalani pano, nimundikire. 35Ndipo Iye anapita m'tsogolo pang'ono, nagwa pansi, napemphera kuti ngati nkutheka nthawi imene impitirire. 36#Yoh. 5.30; 6.38; Aro. 8.15Ndipo ananena, Abba, Atate, zinthu zonse zitheka ndi Inu; mundichotsere chikho ichi; komatu si chimene ndifuna Ine, koma chimene mufuna Inu. 37Ndipo anadza nawapeza iwo ali m'tulo, nanena ndi Petro, Simoni, ugona kodi? Unalibe mphamvu yakudikira ora limodzi kodi? 38#Aro. 7.23; Agal. 5.17Dikirani, pempherani, kuti mungalowe m'kuyesedwa; mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka. 39Ndipo anachokanso, napemphera, nanena mau omwewo. 40Ndipo anadzanso nawapeza ali m'tulo, pakuti maso ao analemeradi; ndipo sanadziwe chomyankha Iye. 41#Yoh. 13.1Ndipo anadza kachitatu, nanena nao, Gonani tsopano, nimupumule; chakwanira; yafika nthawi; onani Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja a anthu ochimwa. 42Ukani, tizimuka; onani wakundiperekayo ali pafupi.
Amgwira Yesu
(Mat. 26.47-56; Luk. 22.47-53; Yoh. 18.2-11)
43Ndipo pomwepo, Iye ali chilankhulire, anadza Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, ndipo pamodzi naye khamu la anthu, ali nao malupanga ndi mikunkhu, ochokera kwa ansembe aakulu ndi alembi ndi akulu. 44Ndipo wakumpereka Iye anawapatsa chizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsompsona, ndiyetu; mgwireni munke naye chisungire. 45Ndipo atafika, pomwepo anadza kwa Iye, nanena, Rabi; nampsompsonetsa. 46Ndipo anamthira manja, namgwira. 47Koma mmodzi wina wa iwo akuimirirapo, anasolola lupanga lake, nakantha kapolo wake wa mkulu wa ansembe, namdula khutu lake. 48#Luk. 22.52Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi mwatuluka ndi malupanga ndi mikunkhu kundigwira Ine monga wachifwamba? 49#Yes. 53.7; Luk. 22.37Masiku onse ndinali nanu m'Kachisi ndilikuphunzitsa, ndipo simunandigwira Ine; koma ichi chachitika kuti malembo akwanitsidwe. 50Ndipo iwo onse anamsiya Iye, nathawa.
51Ndipo mnyamata wina anamtsata Iye, atafundira pathupi bafuta yekha; ndipo anamgwira; 52koma iye anasiya bafutayo, nathawa wamaliseche.
Yesu aweruzidwa ndi akulu a Ayuda
(Mat. 26.57-68; Luk. 22.63-71; Yoh. 18.12-27)
53 # Luk. 22.54 Ndipo ananka naye Yesu kwa mkulu wa ansembe; ndipo anasonkhana kwa iye ansembe aakulu onse ndi akulu a anthu, ndi alembi. 54Ndipo Petro adamtsata Iye kutali, kufikira kulowa m'bwalo la mkulu wa ansembe; ndipo anali kukhala pansi pamodzi ndi anyamata, ndi kuotha moto. 55Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a milandu onse anafunafuna umboni wakutsutsa nao Yesu kuti amuphe Iye; koma sanaupeze. 56Pakuti ambiri anamchitira umboni wonama, ndipo umboni wao sunalingana. 57Ndipo ananyamukapo ena, namchitira umboni wakunama, nanena kuti, 58#Yoh. 2.19Ife tinamva Iye alikunena, kuti, Ine ndidzaononga Kachisi uyu wopangidwa ndi manja, ndi masiku atatu ndidzamanga wina wosapangidwa ndi manja. 59Ndipo ngakhale momwemo umboni wao sunalingana. 60Ndipo mkulu wa ansembe ananyamuka pakati, namfunsa Yesu, nanena, Suyankha kanthu kodi? Nchiyani ichi chimene awa alikuchitira mboni? 61#Yes. 53.7Koma anakhala chete, osayankha kanthu. Mkulu wa ansembe anamfunsanso, nanena naye, Kodi Iwe ndiwe Khristu, Mwana wake wa Wolemekezeka? 62#Luk. 22.69Ndipo Yesu anati, Ndine amene; ndipo mudzaona Mwana wa Munthu alikukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kudza ndi mitambo ya kumwamba. 63Ndipo mkulu wa ansembe anang'amba malaya ake, nanena, Tifuniranjinso mboni zina? 64Mwamva mwano wake; muyesa bwanji? Ndipo onse anamtsutsa Iye kuti ayenera kufa. 65Ndipo ena anayamba kumthira malovu Iye, ndi kuphimba nkhope yake, ndi kumbwanyula, ndi kunena naye, Lota; ndipo anyamatawo anampanda Iye khofu.
Petro akana kuti sadziwa Yesu
(Mat. 26.69-75; Luk. 22.54-62; Yoh. 18.15-18, 25-27)
66Ndipo pamene Petro anali pansi m'bwalo, anadzapo mmodzi wa adzakazi a mkulu wa ansembe; 67ndipo anaona Petro alikuotha moto, namyang'ana iye, nanena, Iwenso unali naye Mnazarene, Yesu. 68Koma anakana, nanena, Sindidziwa kapena kumvetsa chimene uchinena iwe; ndipo anatuluka kunka kuchipata; ndipo tambala analira. 69#Luk. 22.58-59Ndipo anamuona mdzakaziyo, nayambanso kunena ndi iwo akuimirirapo, Uyu ngwa awo. 70#Mac. 2.7Koma anakananso. Ndipo patapita kamphindi, akuimirirapo ananenanso ndi Petro, Zedi uli wa awo; pakutinso uli Mgalileya. 71Koma iye anayamba kutemberera, ndi kulumbira, Sindimdziwa munthuyu mulikunena. 72Ndipo pomwepo tambala analira kachiwiri. Ndipo Petro anakumbukira umo Yesu anati kwa iye, kuti, Tambala asanalire kawiri udzandikana katatu. Ndipo pakuganizira ichi analira misozi.

Currently Selected:

MARKO 14: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in