MARKO 16
16
Yesu auka kwa akufa
(Mat. 28.1-10; Luk. 24.1-12; Yoh. 20.1-18)
1 #
Luk. 23.56
Ndipo litapita Sabata, Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi Salome, anagula zonunkhira, kuti akadze kumdzoza Iye. 2Ndipo anadza kumanda mamawa tsiku loyamba la Sabata, litatuluka dzuwa. 3Ndipo analikunena mwa okha, Adzatikunkhunizira ndani mwalawo, pakhomo la manda? 4Ndipo pamene anakweza maso anaona kuti mwala wakunkhunizidwa, pakuti unali waukulu ndithu. 5#Luk. 24.3Ndipo pamene analowa m'manda, anaona mnyamata alikukhala kumbali ya kudzanja lamanja, wovala mwinjiro woyera; ndipo iwo anadabwa. 6Ndipo iye ananena nao, Musadabwe: mulikufuna Yesu Mnazarene amene anapachikidwa; anauka; sali pano; taonani, mbuto m'mene anaikamo Iye! 7#Mat. 26.32; Mrk. 14.28Koma mukani, uzani ophunzira ake, ndi Petro, kuti akutsogolerani inu ku Galileya; kumeneko mudzamuona Iye, monga ananena ndi inu. 8#Luk. 24.9Ndipo anatuluka iwo, nathawa kumanda; pakuti kunthunthumira ndi kudabwa kwakukulu kudawagwira; ndipo sanauze kanthu kwa munthu aliyense; pakuti anachita mantha.
Yesu aonekera kwa ophunzira ake
9 #
Luk. 8.2; Yoh. 20.14 Ndipo pamene Iye adauka mamawa tsiku loyamba la sabata, anayamba kuonekera kwa Maria wa Magadala, amene Iye adamtulutsira ziwanda zisanu ndi ziwiri. 10#Luk. 24.10; Yoh. 20.18Iyeyu anapita kuwauza iwo amene ankakhala naye, ali ndi chisoni ndi kulira misozi. 11#Luk. 24.11Ndipo iwowo, pamene anamva kuti ali moyo, ndi kuti adapenyeka kwa iye, sanamvere.
12 #
Luk. 24.13-35
Ndipo zitatha izi, anaonekanso Iye m'maonekedwe ena kwa awiri a iwo alikuyenda kupita kumilaga. 13Ndipo iwowa anachoka nawauza otsala; koma iwo omwe sanawavomereze.
14 #
Luk. 24.36-43
Ndipo chitatha icho anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pachakudya; ndipo anawadzudzula chifukwa cha kusavomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanavomereza iwo amene adamuona, atauka Iye. 15#Mat. 28.19Ndipo ananena nao, Mukani kudziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse. 16#Yoh. 3.18, 36; Aro. 10.9Amene akhulupirira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupirira adzalangidwa. 17#Luk. 10.17; Mac. 2.4; 5.16Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupirira: m'dzina langa adzatulutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano; 18#Mac. 28.5, 8adzatola njoka, ndipo ngakhale akamwa kanthu kakufa nako, sikadzawapweteka; adzaika manja ao pa odwala, ndipo adzachira.
19 #
Mas. 110.1; Luk. 24.51 Pamenepo Ambuye Yesu, atatha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala pa dzanja lamanja la Mulungu. 20#Mac. 5.12; 1Ako. 2.4-5Ndipo iwowa anatuluka, nalalikira ponseponse, ndipo Ambuye anachita nao pamodzi, natsimikiza mau ndi zizindikiro zakutsatapo. Amen.
Currently Selected:
MARKO 16: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: