MARKO 5
5
Yesu achiritsa wogwidwa ndi mzimu wonyansa ku Gerasa
1Ndipo anafika tsidya lina la nyanja, kudziko la Agerasa. 2Ndipo pamene adatuluka mungalawa, pomwepo anakomana naye munthu wotuluka kumanda wa mzimu wonyansa, 3amene anayesa nyumba yake kumanda; ndipo palibe munthu anakhoza kummanganso, inde ngakhale ndi unyolo; 4pakuti ankamangidwa kawirikawiri ndi matangadza ndi maunyolo, ndipo anamwetula maunyolo, naduladula matangadza; ndipo palibe munthu anali ndi mphamvu yakumfuya. 5Ndipo masiku onse, usiku ndi usana, anakhala m'manda ndi m'mapiri, nafuula, nadzitematema ndi miyala. 6Ndipo pakuona Yesu kutali, anathamanga, namgwadira Iye; 7ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Ndili ndi chiyani ine ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikulumbirirani pa Mulungu, msandizunze. 8Pakuti ananena kwa iye, Tuluka iwe, mzimu wonyansa, kwa munthuyu. 9Ndipo anamfunsa, Dzina lako ndani? Ndipo ananena kwa Iye, Dzina langa ndine Legio; chifukwa tili ambiri. 10Ndipo anampempha Iye kwambiri kuti asaitulutsire kunja kwake kwa dziko. 11Ndipo panali pamenepo gulu lalikulu la nkhumba zilinkudya kuphiri. 12Ndipo inampempha Iye, kuti, Titumizeni ife mu nkhumbazo, kuti tilowe mu izo. 13Ndipo anailola. Ndipo mizimu yonyansa inatuluka, nilowa mu nkhumba; ndipo gulu linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanja, ndizo ngati zikwi ziwiri; ndipo zinatsamwa m'nyanja. 14Ndipo akuziweta anathawa, nauza m'mudzi, ndi kuminda. Ndipo anadza kudzaona chochitikacho. 15Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo alikukhala pansi, wovala ndi wa nzeru zake zabwino, ndiye amene anali ndi legio; ndipo anaopa iwo. 16Ndipo adapenyawo adawafotokozera umo anachitira ndi wogwidwa ziwandayo, ndi za nkhumbazo. 17#Mac. 16.39Ndipo anayamba kumpempha Iye kuti achoke m'malire ao. 18#Luk. 8.38Ndipo m'mene Iye analikulowa mungalawa, anampempha waziwanda uja kuti akhale ndi Iye. 19Ndipo sanamlole, koma ananena naye, Muka kwanu kwa abale ako, nuwauze zinthu zazikulu anakuchitira Ambuye, ndi kuti anakuchitira chifundo. 20Ndipo anamuka nayamba kulalikira ku Dekapoli zinthu zazikulu Yesu adamchitira iye; ndipo anthu onse anazizwa.
Mwana wa Yairo. Mkazi wokhudza chofunda cha Yesu
21Ndipo pamene Yesu anaolokanso mungalawa tsidya lina, khamu lalikulu linasonkhana kwa Iye; ndipo Iye anali pambali pa nyanja. 22#Luk. 8.41Ndipo anadzako mmodzi wa akulu a sunagoge, dzina lake Yairo; ndipo pakuona Iye, anagwada pa mapazi ake, nampempha kwambiri, 23nanena, kuti, Kamwana kanga kabuthu kalinkutsirizika; ndikupemphani Inu mufikeko, muike manja anu pa iko, kuti kapulumuke, ndi kukhala ndi moyo. 24Ndipo ananka naye pamodzi; ndipo khamu lalikulu linamtsata Iye, ndi kumkanikiza Iye.
25Ndipo munthu wamkazi amene anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, 26ndipo anamva zowawa zambiri ndi asing'anga ambiri, nalipira zonse anali nazo osachira pang'ono ponse, koma makamaka nthenda yake idakula, 27m'mene iye anamva mbiri yake ya Yesu, anadza m'khamu kumbuyo kwake, nakhudza chovala chake. 28Pakuti ananena iye, Ngati ndikakhudza ngakhale zovala zake ndidzapulumutsidwa. 29Ndipo pomwepo kasupe wa nthenda yake adaphwa; ndipo anazindikira m'thupi kuti anachiritsidwa chivutiko chake. 30#Luk. 6.19; 8.46Ndipo pomwepo Yesu, pamene anazindikira mwa Iye yekha kuti mphamvu idatuluka mwa Iye, anapotoloka m'khamu, nanena, Ndani anakhudza zovala zanga? 31Ndipo ophunzira ake ananena kwa Iye, Muona kuti khamu lilikukanikiza Inu, ndipo munena kodi, Wandikhudza ndani? 32Ndipo Iye anaunguzaunguza kumuona iye amene adachita ichi. 33Koma mkaziyo anachita mantha, ndi kunthunthumira, podziwa chimene anamchitira iye, nadza, namgwadira, namuuza choona chonse. 34#Mrk. 10.52; Mac. 14.9Ndipo anati kwa iye, Mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakupulumutsa; muka mumtendere, nukhale wochira chivutiko chako.
35 #
Luk. 8.49
M'mene iye ali chilankhulire, anafika a kunyumba ya mkulu wa sunagoge, nanena, kuti, Mwana wako wafa; uvutiranjinso Mphunzitsi? 36Koma Yesu wosasamala mau olankhulidwawo, ananena kwa mkulu wa sunagoge, Usaope, khulupirira kokha. 37Ndipo sanalole munthu yense kutsagana naye, koma Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wake wa Yakobo. 38Ndipo anafika kunyumba kwake kwa mkulu wa sunagoge; ndipo anaona chipiringu, ndi ochita maliro, ndi akukuwa ambiri. 39#Yoh. 11.11Ndipo m'mene atalowa, ananena nao, Mubuma ndi kulira bwanji? Mwana sanafe, koma ali m'tulo. 40#Mac. 9.40Ndipo anamseka Iye pwepwete. Koma Iye anawatulutsa onse, natenga atate wa mwana, ndi amake, ndi ajawo anali naye, nalowa m'mene munali mwanayo. 41Ndipo anagwira dzanja lake la mwana, nanena kwa iye, Talita koumi, ndiko kunena posandulika, Buthu, ndinena ndi iwe, Uka. 42Ndipo pomwepo buthulo linauka, niliyenda; pakuti linali la zaka khumi ndi ziwiri. Ndipo anadabwa pomwepo ndi kudabwa kwakukulu. 43#Mat. 8.4; Luk. 5.14Ndipo anawalamulira kwambiri kuti asadziwe ichi munthu mmodzi, nawauza kuti ampatse iye kudya.
Currently Selected:
MARKO 5: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: