YouVersion Logo
Search Icon

AROMA 3

3
Kuposa kwake kwa Myuda. Mulungu ali wolungama
1Ndipo potero Myuda aposa ninji? Kapena mdulidwe upindulanji? 2#Deut. 4.7-8Zambiri monsemonse: choyamba, kuti mau a Mulungu anaperekedwa kwa iwo. 3#Num. 23.19Nanga bwanji ngati ena sanakhulupirira? Kodi kusakhulupirira kwao kuyesa chabe chikhulupiriko cha Mulungu? 4#Mas. 51.4Msatero ai. Koma Mulungu akhale woona, ndimo anthu onse akhale onama; monga kwalembedwa,
Kuti Inu mukayesedwe wolungama m'maneno anu,
ndi kuti mukalakike m'mene muweruzidwa.
5Koma ngati chosalungama chathu chitsimikiza chilungamo cha Mulungu, tidzatani ife? Kodi ali wosalungama Mulungu, amene afikitsa mkwiyo? (Ndilankhula umo anenera munthu). 6Msatero ai. Ngati kotero, Mulungu adzaweruza bwanji mlandu wa dziko lapansi? 7Pakuti ngati choonadi cha Mulungu chichulukitsa ulemerero wake chifukwa cha bodza langa, nanga inenso ndiweruzidwa bwanji monga wochimwa? 8Ndipo tilekerenji kunena, Tichite zoipa kuti zabwino zikadze (monganso ena atinamiza ndi kuti timanena)? Kulanga kwa amenewo kuli kolungama.
Anthu onse agwidwa ndi zoipa
9 # Aro. 3.23; Agal. 3.22 Ndipo chiyani tsono? Kodi tiposa ife? Iai ndithu; pakuti tidawaneneza kale Ayuda ndi Agriki omwe, kuti onsewa agwidwa ndi uchimo; 10#Mas. 14.1-3; 53.1-3monga kwalembedwa,
Palibe mmodzi wolungama, inde palibe mmodzi;
11palibe mmodzi wakudziwitsa,
palibe mmodzi wakulondola Mulungu;
12onsewa apatuka, pamodzi akhala opanda pake;
palibe mmodzi wakuchita zabwino,
inde, palibe mmodzi ndithu.
13 # Mas. 5.9 M'mero mwao muli manda apululu;
ndi lilime lao amanyenga;
ululu wa mamba uli pansi pa milomo yao;
14 # Mas. 10.7 m'kamwa mwao mudzala ndi zotemberera ndi zowawa;
15 # Yes. 59.7-8 miyendo yao ichita liwiro kukhetsa mwazi;
16kusakaza ndi kusauka kuli m'njira zao;
17ndipo njira ya mtendere sanaidziwa;
18 # Mas. 36.1 kumuopa Mulungu kulibe pamaso pao.
19 # Ezk. 16.63 Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu; 20#Mas. 143.2; Aro. 7.7; Agal. 2.16chifukwa kuti pamaso pake palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo; pakuti uchimo udziwika ndi lamulo.
Tilungamitsidwa mwa kukhulupirira Yesu Khristu
21 # Mac. 15.11; Afi. 3.9 Koma tsopano chilungamo cha Mulungu chaoneka chopanda lamulo, chilamulo ndi aneneri achitira ichi umboni; 22#Aro. 4ndicho chilungamo cha Mulungu chimene chichokera mwa chikhulupiriro cha pa Yesu Khristu kwa onse amene akhulupirira; pakuti palibe kusiyana; 23#Aro. 3.9; Agal. 3.22pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu; 24#Mat. 20.28; Aef. 2.8; Akol. 1.14; Aheb. 9.12ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi chisomo chake, mwa chiombolo cha mwa Khristu Yesu; 25#1Yoh. 2.2; Akol. 1.20amene Mulungu anamuika poyera akhale chotetezera mwa chikhulupiriro cha m'mwazi wake, kuti aonetse chilungamo chake, popeza Mulungu m'kulekerera kwake analekerera machimo ochitidwa kale lomwe; 26kuti aonetse chilungamo chake m'nyengo yatsopano; kuti Iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu. 27#1Ako. 1.29, 31Pamenepo kudzitama kuli kuti? Kwaletsedwa. Ndi lamulo lotani? La ntchito kodi? Iai; koma ndi lamulo la chikhulupiriro. 28#Mac. 13.38-39; Agal. 2.16Pakuti timuyesa munthu wolungama chifukwa cha chikhulupiriro, wopanda ntchito za lamulo. 29Kapena Mulungu ndiye wa Ayuda okhaokha kodi? Si wao wa amitundunso kodi? Eya, wa amitundunso: 30#Agal. 3.8, 20, 28ngatitu ndiye Mulungu mmodzi, amene adzawayesa amdulidwe olungama ndi chikhulupiriro, ndi akusadulidwa mwa chikhulupiriro. 31Potero kodi lamulo tiyesa chabe mwa chikhulupiriro? Msatero ai; koma tikhazikitsa lamulo.

Currently Selected:

AROMA 3: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in