YouVersion Logo
Search Icon

AROMA 5

5
Zipatso za chikhulupiriro
1 # Aro. 3.28, 30; Aef. 2.14 Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu; 2#Aef. 3.12amene ife tikhoza kulowa naye ndi chikhulupiriro m'chisomo ichi m'mene tilikuimamo; ndipo tikondwera m'chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu. 3#Mat. 5.11-12Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi; 4ndi chizolowezi chichita chiyembekezo: 5#Afi. 1.20ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife. 6#Aro. 5.8Pakuti pamene tinali chikhalire ofooka, pa nyengo yake Khristu anawafera osapembedza. 7Pakuti ndi chivuto munthu adzafera wina wolungama; pakuti kapena wina adzalimbika mtima kufera munthu wabwino. 8#Yoh. 3.16Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife. 9#Aheb. 9.14Ndipo tsono popeza tinayesedwa olungama ndi mwazi wake, makamaka ndithu tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa Iyeyo. 10#Akol. 1.20-21Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake. 11Ndipo si chotero chokha, koma ife tikondwera ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene talandira naye tsopano chiyanjanitso.
Uchimo unalowa ndi Adamu, chilungamo ndi Khristu
12 # Gen. 3.6 Chifukwa chake, monga uchimo unalowa m'dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa. 13#Aro. 4.15Pakuti kufikira nthawi ya lamulo uchimo unali m'dziko lapansi; koma uchimo suwerengedwa popanda lamulo. 14#1Ako. 15.21-22, 45Komatu imfa inachita ufumu kuyambira kwa Adamu kufikira kwa Mose, ngakhale pa iwonso amene sanachimwa monga machimwidwe ake a Adamu, ndiye fanizo la wakudzayo. 15Koma mphatso yaulere siilingana ndi kulakwa. Pakuti ngati ambiriwo anafa chifukwa cha kulakwa kwa mmodziyo, makamaka ndithu chisomo cha Mulungu, ndi mphatso yaulere zakuchokera ndi munthu mmodziyo Yesu Khristu, zinachulukira anthu ambiri. 16Ndipo mphatso siinadza monga mwa mmodzi wakuchimwa, pakuti mlandu ndithu unachokera kwa munthu mmodzi kufikira kutitsutsa, koma mphatso yaulere ichokera ku zolakwa zambiri kufikira kutiyesa olungama. 17Pakuti ngati, ndi kulakwa kwa mmodzi, imfa inachita ufumu mwa mmodziyo; makamaka ndithu amene akulandira kuchuluka kwake kwa chisomo ndi kwa mphatso ya chilungamo, adzachita ufumu m'moyo mwa mmodzi, ndiye Yesu Khristu. 18Chifukwa chake, monga mwa kulakwa kumodzi kutsutsa kunafikira anthu onse; chomwechonso mwa chilungamitso chimodzi chilungamo cha moyo chinafikira anthu onse. 19Pakuti monga ndi kusamvera kwa munthu mmodzi ambiri anayesedwa ochimwa, chomwecho ndi kumvera kwa mmodzi ambiri adzayesedwa olungama. 20#Yoh. 15.22; 1Tim. 1.14Ndipo lamulo linalowa moonjezera, kuti kulakwa kukachuluke; koma pamene uchimo unachuluka, pomwepo chisomo chinachuluka koposa; 21kuti, monga uchimo unachita ufumu muimfa, chomwechonso chisomo chikachite ufumu mwa chilungamo, kufikira moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.

Currently Selected:

AROMA 5: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in