YouVersion Logo
Search Icon

AROMA 7

7
Okhulupirira akwatiwa ndi Khristu
1Nanga kodi simudziwa, abale, pakuti ndilankhula ndi anthu akudziwa lamulo, kuti lamulolo lichita ufumu pa munthu nthawi zonse iye ali wamoyo? 2#1Ako. 7.39Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wake wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo. 3#Mat. 5.32Ndipo chifukwa chake, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wake wamoyo, adzanenedwa mkazi wachigololo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamuloli; chotero sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.
4 # Aro. 8.2; Agal. 5.22 Chotero, abale anga, inunso munayesedwa akufa ku chilamulo ndi thupi la Khristu; kuti mukakhale ake a wina, ndiye amene anaukitsidwa kwa akufa, kuti ife timbalire Mulungu zipatso. 5#Yak. 1.15Pakuti pamene tinali m'thupi, zilakolako za machimo, zimene zinali mwa chilamulo, zinalikuchita m'ziwalo zathu, kuti zibalire imfa zipatso. 6#2Ako. 3.6Koma tsopano tinamasulidwa kuchilamulo, popeza tinafa kwa ichi chimene tinagwidwa nacho kale; chotero kuti titumikire mu mzimu watsopano, si m'chilembo chakale ai.
Malamulo aonetsa zoipa
7 # Aro. 3.20; Eks. 20.17 Pamenepo tidzatani? Kodi chilamulo chili uchimo? Msatero ai. Koma ine sindikadazindikira uchimo, koma mwa lamulo ndimo; pakuti sindikadazindikira chilakolako sichikadati chilamulo, Usasirire; 8#Aro. 5.20koma uchimo, pamene unapeza chifukwa, unachita m'kati mwanga zilakolako zonse mwa lamulo; pakuti popanda lamulo uchimo uli wakufa. 9Ndipo kale ine ndinali wamoyo popanda lamulo; koma pamene lamulo linadza, uchimo unatsitsimuka, ndipo ine ndinafa. 10#Lev. 18.5Ndipo lamulo, limene linali lakupatsa moyo, ndinalipeza lakupatsa imfa. 11Pakuti uchimo, pamene unapeza chifukwa mwa lamulo, unandinyenga ine, ndi kundipha nalo. 12#Mas. 19.8Chotero chilamulo chili choyera, ndi chilangizo chake nchoyera, ndi cholungama, ndi chabwino.
Kulimbana m'kati mwanga
13Ndipo tsopano chabwino chija chinandikhalira imfa kodi? Msatero ai. Koma uchimo, kuti uoneke kuti uli uchimo, wandichitira imfa mwa chabwino chija; kuti uchimo ukakhale wochimwitsa ndithu mwa lamulo. 14#1Maf. 21.20Pakuti tidziwa kuti chilamulo chili chauzimu; koma ine ndili wathupi, wogulitsidwa kapolo wa uchimo. 15#Agal. 5.17Pakuti chimene ndichita sindichidziwa; pakuti sindichita chimene ndifuna, koma chimene ndidana nacho, ndichita ichi. 16Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, ndivomerezana nacho chilamulo kuti chili chabwino. 17Ndipo tsopano si ine ndichichita, koma uchimo wakukhalabe m'kati mwanga ndiwo. 18#Gen. 6.5; 8.21Pakuti ndidziwa kuti m'kati mwanga, ndiko m'thupi langa, simukhala chinthu chabwino; pakuti kufuna ndili nako, koma kuchita chabwino sindikupeza. 19Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita. 20Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, si ndinenso amene ndichichita, koma uchimo wakukhalabe m'kati mwanga ndiwo. 21Ndipo chotero ndipeza lamulo ili, kuti, pamene ndifuna chabwino, choipa chiliko. 22#Mas. 1.2Pakuti monga mwa munthu wa m'kati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: 23#Agal. 5.17koma ndiona lamulo lina m'ziwalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la uchimo m'ziwalo zanga. 24Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m'thupi la imfa iyi? 25#1Ako. 15.57Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. Ndipo chotero ine ndekha ndi mtimatu nditumikira chilamulo cha Mulungu; koma ndi thupi nditumikira lamulo la uchimo.

Currently Selected:

AROMA 7: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in