Yoh. 1
1
Mau asanduka munthu, munthuyo ndi Khristu
1Pachiyambi pa zonse Iye amene amatchedwa dzina loti Mau, anali alipo kale. Anali kwa Mulungu, ndipo anali Mulungu. 2Anali kwa Mulungu chikhalire. 3Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo palibe chilichonse chimene chidalengedwa popanda Iye. 4Mwa Iyeyo munali moyo, ndipo moyowo unali kuŵala kounikira anthu. 5Kuŵalako kukuunikabe mu mdima, ndipo mdima sudathe kugonjetsa kuŵalako.
6 #
Mt. 3.1; Mk. 1.4; Lk. 3.1, 2 Mulungu adaatuma munthu wina, dzina lake Yohane. 7Iyeyu adaabwera ngati mboni, kudzachitira umboni kuŵala kuja, kuti anthu onse akhulupirire chifukwa cha umboni wakewo. 8Sikuti iyeyo ndiye anali kuŵalako ai, koma adangobwera kudzachitira umboni kuŵalako. 9Kuŵala kwenikweni, kounikira anthu onse, kunkadza pansi pano. 10Wotchedwa Mauyo anali m'dziko lapansi, ndipo Mulungu adalenga dziko lapansilo kudzera mwa Iye, komabe anthu apansipano sadamzindikire. 11Adaabwera kwao ndithu, koma anthu ake omwe sadamlandire. 12Komabe ena adaamlandira nakhulupirira dzina lake, ndipo ameneŵa Iye adaŵapatsa mphamvu zoti akhale ana a Mulungu. 13Kukhala ana a Mulungu kumeneku sikudachokere m'kubadwa kwao, kapena ku chifuniro cha thupi, kapena ku chifuniro cha munthu ai, koma kudachokera kwa Mulungu.
14Wotchedwa Mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu. Anali wokoma mtima ndi wokhulupirika kwabasi. Ndipotu tidaona ulemerero wake, ndiye kuti ulemerero womwe Iye amalandira kwa Atate pokhala Mwana wao mmodzi yekha uja.
15Yohaneyo adaamchitira umboni. Ankauza anthu mwamphamvu kuti, “Uyu ndiye uja ndinkanenayu kuti amene akubwera pambuyo panga ngwoposa ine; pakuti ine ndisanabadwe, Iye alipo.”
16Kuchokera m'kukoma mtima kwake kwathunthu ife tonse tidalandira madalitso, madalitso ake otsatanatsatana. 17Paja Mulungu adatipatsa Malamulo ake kudzera mwa Mose, koma kudzera mwa Yesu Khristu adatizindikiritsa kukoma mtima ndi kukhulupirika kwake. 18Chikhalire palibe munthu amene adaona Mulungu, koma Mwana mmodzi yekha uja, amene ali wapamtima wa Atate, ndiye adaulula za Mulunguyo.
Umboni wa Yohane Mbatizi
(Mt. 3.1-12; Mk. 1.7, 8; Lk. 3.15-17)
19Nthaŵi ina akuluakulu a Ayuda a ku Yerusalemu adaatuma ansembe ndi Alevi ena kukafunsa Yohane kuti, “Kodi iwe ndiwe yani?” 20Iye adayankha mosabisa konse, adanenetsa ndithu kuti, “Inetu sindine Mpulumutsi wolonjezedwa uja ai.” 21#Mal. 4.5; Deut. 18.15, 18; Mphu. 48.10, 11Adamufunsanso kuti, “Nanga ndiwe yani? Ndiwe Eliya kodi?” Iye adati, “Iyai, sindine Eliya.” Iwo adati, “Kodi ndiwe Mneneri#1.21: Kodi ndiwe Mneneri: Mulungu adaalonjeza kuti adzatumiza mneneri wina wonga Mose (Deut. 18.15), ndipo Ayuda ankayembekeza kufika kwake (Yoh. 6.14; 7.40). Mneneriyo ndi Yesu amene (Ntc. 3.22-24). tikumuyembekeza uja?” Koma Yohane adayankha kuti, “Ainso.” 22Tsono adamuuza kuti, “Tanena zenizenitu, kuti tikaŵafotokozere bwino amene atituma. Mwiniwakewe umati ndiwe yani?” 23#Yes. 40.3Yohane adaŵayankha kuti, “Monga adaanenera mneneri Yesaya:
“Ine ndine liwu la munthu wofuula m'chipululu;
akunena kuti,
‘Ongolani mseu wodzadzeramo Ambuye.’ ”
24Anthu aja adaaŵatuma ndi Afarisi. 25Tsono adafunsa Yohane kuti, “Ngati sindiwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, kapena Eliya, kapenanso Mneneri tikumuyembekeza uja, nanga bwanji umabatiza?” 26Yohane adaŵayankha kuti, “Ine ndimabatiza ndi madzi, koma pakati panupa pali wina amene inu simukumdziŵa. 27Iyeyu ngwobwera pambuyo panga, komabe sindili woyenera ngakhale kumasula zingwe za nsapato zake.”
28Zimenezi zidachitikira ku Betaniya, kutsidya kwa mtsinje wa Yordani, kumene Yohane ankabatiza.
Yesu ndiye Mwanawankhosa wa Mulungu
29M'maŵa mwake Yohane adaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo adati, “Suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu uja, wochotsa machimo a anthu a pa dziko lonse lapansi. 30Iyeyu ndi amene ndinkanena uja kuti, ‘Pambuyo panga pakubwera munthu wopambana ine, pakuti ine ndisanabadwe, Iye alipo.’ 31Inenso sindinkamudziŵa, koma ndidabwera kudzabatiza ndi madzi kuti Aisraele amdziŵe.”
32Yohane adachitanso umboni, adati, “Ndidaona Mzimu Woyera akutsika kumwamba ngati nkhunda, nakhazikika pa Iye. 33Ine sindinkamudziŵa, koma Mulungu amene adandituma kudzabatiza ndi madzi, ndiye adaandiwuza kuti, ‘Amene udzaone Mzimu Woyera akutsika ndi kukhazikika pa Iye, ndi Iyeyo wobatiza mwa Mzimu Woyera.’ 34Ineyo ndidaziwonadi, ndipo ndikuchita umboni kuti ameneyu ndi Mwanadi wa Mulungu.”
Ophunzira oyamba a Yesu
35M'maŵa mwakenso Yohane anali pamalo pomwepo pamodzi ndi ophunzira ake ena aŵiri. 36Pamene adaona Yesu akuyenda, iye adati, “Suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu.” 37Ophunzira aŵiri aja atamva mauwo, adatsatira Yesu. 38Yesu adacheuka naona kuti akumtsatira, tsono adaŵafunsa kuti, “Kodi ulendowu?” Iwo adati, “Timati tidziŵe, kodi mumakhala kuti, Rabi?” (Tanthauzo la Rabi ndiye kuti, Mphunzitsi.) 39Yesu adati, “Tiyeni mukakuwone.” Iwo adapita naye. Pamenepo nthaŵi inali ngati 4 koloko madzulo. Adakaonako kumene Iye ankakhala, ndipo adakhala naye tsiku limenelo.
40Mmodzi mwa aŵiri aja amene adaamva mau a Yohane natsatira Yesu, anali Andrea, mbale wake wa Simoni Petro. 41Iye adayamba kukapeza mbale wakeyo Simoni, namuuza kuti, “Tampeza Mesiya.” (Ndiye kuti, Mpulumutsi wolonjezedwa uja.) 42Motero adamtenga kupita naye kwa Yesu. Pamene Yesu adamuwona adati, “Ndiwe Simoni, mwana wa Yohane. Dzina lako lidzakhala Kefa.” (Tanthauzo la Kefa ndi Petro, ndiye kuti Thanthwe.)
Yesu aitana Filipo ndi Natanaele
43M'maŵa mwake Yesu adaganiza zopita ku Galileya. Adapeza Filipo, namuuza kuti, “Unditsate.” 44Filipo anali wa ku mudzi wa Betsaida, kwaonso kwa Andrea ndi Petro. 45Filipo adakapeza Natanaele namuuza kuti, “Tampeza Ujayu amene Mose adalemba za Iye m'buku la Malamulo, uja anenerinso adalemba za Iye. Ndi Yesu Mwana wa Yosefe, wa ku Nazarete.” 46Koma Natanaele adamufunsa kuti, “Kodi ku Nazarete nkuchokera kanthu kabwino?” Filipo adati, “Tiye ukadziwonere wekha.”
47Pamene Yesu adaona Natanaele akubwera potero, adati, “Mwamuwonatu Mwisraele weniweni wopanda chinyengo.” 48Natanaele adamufunsa kuti, “Mwandidziŵa bwanji?” Yesu adati, “Muja unakhala patsinde pa mkuyu paja, Filipo asanakuitane, Ine ndinakuwona.” 49Natanaele adati, “Aphunzitsi, ndinudi Mwana wa Mulungu, ndinu Mfumu ya Israele.” 50Yesu adamuyankha kuti, “Kodi wakhulupirira chifukwa ndakuuza kuti ndinakuwona patsinde pa mkuyu paja? Udzaona zoposa pamenepa.” 51#Gen. 28.12Adatinso, “Ndithu ndikunenetsa kuti mudzaona Kumwamba kutatsekuka, angelo a Mulungu akukwera ndi kutsika pa Mwana wa Munthu.”
Currently Selected:
Yoh. 1: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi

: