Yoh. 11
11
Za imfa ya Lazaro
1 #
Lk. 10.38, 39 Panali munthu wina, dzina lake Lazaro, amene ankadwala. Anali wa ku mudzi wa Betaniya, kwao kwa Maria ndi mbale wake Marita. 2#Yoh. 12.3 Mariayo ndi yemwe uja amene adaadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira, nkupukuta mapazi ao ndi tsitsi lake. Lazaro ankadwalayo anali mlongo wake. 3Tsono alongo ake aja adatumiza thenga kwa Yesu kukamuuza kuti, “Ambuye, bwenzi lanu uja akudwala.” 4Pamene Yesu adamva zimenezi adati, “Kudwalako safa nako ai, koma zatero kuti Mulungu alemekezedwe, ndipo kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe chifukwa cha matendawo.”
5Ndiye kuti Yesu ankakonda Marita ndi mng'ono wake Maria ndiponso Lazaro. 6Komabe pamene adamva za matendawo, Yesu adaswera masiku aŵiri pamalo pomwe adaaliripo. 7Pambuyo pake adauza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tipitenso ku Yudeya.” 8Ophunzira akewo adati, “Aphunzitsi, tsopano apa Ayuda ankafuna kukuponyani miyala, ndiye mukuti mupitenso komweko?” 9Yesu adati, “Kodi suja usana uli ndi maora khumi ndi aŵiri? Munthu akayenda masana, sakhumudwa, chifukwa amaona kuŵala kwa dzikoku. 10Koma akayenda usiku, amakhumudwa chifukwa kuŵalako alibe.”
11Atatero adaŵauza kuti, “Lazaro, bwenzi lathu, wagona tulo, koma ndipita kuti ndikamdzutse ku tulo taketo.” 12Apo ophunzira ake adati, “Ambuye, ngati wagona tulo, achira.” 13Iwo ankayesa kuti akunena za tulo teniteni, koma Yesu ankanena za imfa yake ya Lazaro. 14Tsono Yesu adaŵauza mosabisa kuti, “Lazaro wamwalira, 15komabe chifukwa cha inu ndikukondwera kuti Ine kunalibe kumeneko, kuti choncho mukakhulupirire. Tiyeni tipiteko.” 16Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, adauza ophunzira anzake kuti, “Tiyeni ifenso tipite nao kuti tikafe naye pamodzi.”
Yesu ndiye woukitsa anthu ndi woŵapatsa moyo
17Pamene Yesu adafika ku Betaniya, adapeza Lazaro atagona m'manda masiku anai. 18Ku Betaniya kunali kufupi ndi ku Yerusalemu, mtunda wokwanira pafupi makilomita atatu. 19Panali anthu ambiri amene adaabwera kwa Marita ndi Maria kudzaŵapepesa chifukwa cha imfa ya mlongo wao.
20Pamene Marita adamva kuti Yesu akubwera, adapita kukamchingamira. Koma Maria adaatsalira m'nyumba. 21Tsono Marita adauza Yesu kuti, “Ambuye, mukadakhala kuno, sibwenzi mlongo wanga atamwalira. 22Koma ngakhale tsopano, ndikudziŵa kuti Mulungu adzakupatsani zilizonse mungampemphe.” 23Yesu adamuuza kuti, “Mlongo wako adzauka.” 24#2Am. 7.22, 23; 12.44Marita adati, “Ndikudziŵa kuti adzauka podzauka anthu kwa akufa pa tsiku lomaliza.” 25Yesu adamuuza kuti, “Woukitsa anthu kwa akufa ndiponso woŵapatsa moyo ndine. Munthu wokhulupirira Ine, ngakhale afe adzakhala ndi moyo. 26Ndipo aliyense amene ali ndi moyo nakhulupirira Ine, sadzafa konse. Kodi ukukhulupirira zimenezi?” 27Iye adati, “Inde Ambuye, ndikukhulupirira kuti Inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu, amene adayenera kubwera pansi pano.”
Yesu alira
28Marita atanena zimenezi, adaitanira paseri Maria mng'ono wake namuuza kuti, “Afika Aphunzitsi, akukuitana.” 29Maria atamva zimenezi, adanyamuka msangamsanga, nadza kwa Yesu. 30Pamenepo nkuti Yesu asanafike kumudziko, koma anali chikhalire pamalo pomwe Marita adaakumana naye. 31Anthu amene anali m'nyumba akupepesa Mariayo, ataona kuti wanyamuka msangamsanga ndi kutuluka, adamtsatira. Ankayesa kuti akupita kumanda kukalira kumeneko.
32Maria atafika pamene panali Yesu, namuwona, adadzigwetsa kumapazi kwake nati, “Ambuye, mukadakhala kuno, sibwenzi mlongo wanga atamwalira.” 33Yesu ataona Maria akulira, ndiponso anthu amene adaadza naye iwonso akulira, zidamkhudza kwambiri ndipo adavutika mu mtima. 34Tsono adaŵafunsa kuti, “Mudamuika kuti?” Iwo adati, “Ambuye, tiyeni mukaone.” 35Yesu adayamba kulira. 36Pamenepo anthu aja adati, “Onani, ankamukonda zedi.” 37Koma ena mwa iwo adati, “Munthu uyu suja adapenyetsa munthu wosapenya uja? Monga sakadatha kuchitapo kanthu kuti Lazaroyu asafe?”
Yesu aukitsa Lazaro
38Yesu adavutikanso mu mtima, nakafika ku manda amene anali phanga. Pakhomo pake panali chimwala. 39Tsono adati, “Tachotsani chimwalacho.” Marita, mlongo wa womwalirayo, adamuuza kuti, “Pepani Ambuye, wayamba kale kununkha, pakuti wagonamo masiku anai.” 40Yesu adamufunsa kuti, “Kodi sindidakuuze kuti ukakhulupirira uwona ulemerero wa Mulungu?” 41Tsono anthu adachotsa chimwala chija. Yesu adayang'ana kumwamba nati, “Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimvera. 42Ndikudziŵa kuti mumandimvera nthaŵi zonse. Koma ndanena zimenezi chifukwa cha khamu la anthu amene ali panoŵa, kuti akhulupirire kuti ndinu mudandituma.” 43Atatero adaitana mokweza mau kuti, “Lazaro, tuluka!” 44Pomwepo munthu amene adaamwalirayo adatuluka, miyendo yake ndi manja ake zili zomangidwa ndi nsalu zamaliro. Nkhope yake inali yokutidwa ndi nsalu. Yesu adaŵauza kuti, “Mmasuleni, ndipo mlekeni azipita.”
Upo wopangana za kupha Yesu
(Mt. 26.1-5; Mk. 14.1-2; Lk. 22.1-2)
45Ambiri mwa anthu amene adaabwera kwa Maria, adaona zimene Yesu adaachita, ndipo adamkhulupirira. 46Koma ena adapita kwa Afarisi, nakaŵasimbira zimene Yesu adaachita. 47Apo akulu a ansembe ndi Afarisi adaitanitsa Bungwe Lalikulu la Ayuda, nafunsana kuti, “Titani pamenepa, popeza kuti munthuyu akuchita zozizwitsa zambiri? 48Tikamlekerera chomwechi, anthu onse adzamkhulupirira, ndipo Aroma adzabwera nkudzatiwonongera malo athu oyeraŵa ndiponso mtundu wathuwu.”
49Koma mmodzi mwa iwo, dzina lake Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe onse chaka chimenecho, adaŵauza kuti, “Inu simudziŵa kanthu konse ai. 50Monga inu simukuwona kuti nkwabwino koposa kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu onse, m'malo moti mtundu wathu wonse uwonongeke?” 51(Kwenikwenitu sadanene zimenezi ndi nzeru za iye yekha ai. Koma popeza kuti anali mkulu wa ansembe onse chaka chimenecho, ankalosa kuti Yesu adzafera mtundu wa Ayuda. 52Tsono osati kungofera fuko chabe, komanso kusonkhanitsa pamodzi ana a Mulungu amene adabalalika.)
53Kuyambira tsiku limenelo akulu aja a Ayuda adayamba kupangana zoti amuphe. 54Nchifukwa chake Yesu sankayenda poyera pakati pa anthu. Koma adachokako napita ku dziko limene linali pafupi ndi chipululu, ku mudzi wina dzina lake Efuremu, ndipo adakhala kumeneko pamodzi ndi ophunzira ake.
55Chikondwerero cha Paska chija chinkayandikira. Choncho anthu ambiri ochokera ku midzi adapita ku Yerusalemu kukachita mwambo wa kudziyeretsa,#11.55: Mwambo wa kudziyeretsa: Ayuda amene ankaswa Malamulo a Mose ankaletsedwa kuchita nao miyambo ya chipembedzo mpaka atayeretsedwa mwa njira zolamulidwa m'Malamulowo (onani Num. 9.6-8; Yoh. 18.28; Ntc. 21.24.) Paska isanayambe. 56Ankamufunafuna Yesu, ndipo pamene adasonkhana m'Nyumba ya Mulungu ankafunsana kuti, “Kodi inu mukuganiza bwanji? Kodi monga Iye uja abwera kuchikondwerero kuno?” 57Koma akulu a ansembe ndi Afarisi anali atalamula kuti aliyense akadziŵa kumene kuli Yesu, aŵadziŵitse, kuti akamgwire.
Currently Selected:
Yoh. 11: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi

: