Yoh. 4
4
Yesu acheza ndi mai wa ku Samariya
1Afarisi adamva kuti Yesu akukopa ndi kubatiza ophunzira ambiri koposa Yohane. 2(Komabe amene ankabatiza si Yesuyo, koma ophunzira ake). 3Pamene Yesu adadziŵa kuti Afarisi azimva zimenezi, adachokako ku Yudeya napitanso ku Galileya. 4Pa ulendowo ankayenera kudzera m'dziko la Samariya. 5#Gen. 33.19; Yos. 24.32 Tsono adafika ku mudzi wina wa ku Samariya, dzina lake Sikari, pafupi ndi kadziko kamene Yakobe adaapatsa Yosefe, mwana wake. 6Kumeneko kunali chitsime cha Yakobe. Yesu adakhala pansi pambali pa chitsimecho, chifukwa anali atatopa ndi ulendo. Nthaŵi inali ngati 12 koloko masana.
7Tsono padafika mai wina wachisamariya kudzatunga madzi. Yesu nkunena mopempha kuti, “Zikomo mundipatseko madzi akumwa.” 8Nthaŵiyo nkuti ophunzira ake aja atakagula chakudya mu mzinda. 9#Eza. 4.1-5; Neh. 4.1, 2Mai wachisamariya uja adayankha nati, “Inu amene muli Myuda, bwanji mukupempha madzi kwa ine, mai wachisamariya?” (Pakutitu Ayuda sayenderana ndi Asamariya.) 10Yesu adati, “Mukadadziŵa mphatso ya Mulungu, mukadadziŵanso amene akupempha madzi akumwayu, bwenzi mutampempha ndi inuyo mai, Iye nakupatsani madzi opatsa moyo.” 11Maiyo adati, “Bambo, mulibe nchotungira chomwe, ndipo chitsimechi nchozama. Nanga madzi opatsa moyowo muŵatenga kuti? 12Yakobe, kholo lathu ndiye adatipatsa chitsimechi, chimene mwiniwakeyo ankamwapo pamodzi ndi ana ake, ndiponso zoŵeta zake. Kodi Inu mungapambane iyeyo?” 13Yesu adati, “Munthu aliyense womwako madzi aŵa, adzamvanso ludzu. 14Koma aliyense wodzamwa madzi amene Ine ndidzampatse, sadzamvanso ludzu konse mpaka muyaya. Madzi amene ndidzampatsewo azidzatumphukira mwa iye ngati kasupe wa madzi opatsa moyo, nkumupatsa moyo wosatha.” 15Maiyo adati, “Bambo, patsaniko ineyo madzi amenewo kuti ndisamamvenso ludzu kapena kumadzatunganso madzi kuno.”
16Yesu adati, “Pitani mukaitane amuna anu, nkukabweranso kuno.” 17Maiyo adati, “Ndilibe mwamuna.” Yesu adati, “Mwanenetsa kuti mulibe mwamuna. 18Paja mwakwatiwapo kale ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene muli naye tsopano si wanunso. Mwanenazi nzoona.” 19Maiyo adati, “Bambo, ndadziŵa tsopano kuti ndinu mneneri. 20Makolo athu ankapembedza Mulungu pa phiri ili,#4.20: Phiri ili: Limeneli ndi phiri la Gerizimu pafupi ndi Samariya. Kale Asamariya adaamangapo nyumba yopembedzeramo. Nyumbayo itasakazidwa, Asamariya ankapembedzerabe pa phiri lomwelo. koma inu Ayuda mumati ndi ku Yerusalemu kumene anthu ayenera kumakapembedzerako.” 21Yesu adamuuza kuti, “Mai, ndithu ikudza nthaŵi pamene mudzapembedza Atate, osati pa phiri ili kapenanso ku Yerusalemu ai. 22Asamariyanu mumapembedza chimene simuchidziŵa. Ayudafe timapembedza chimene timachidziŵa, pakuti chipulumutso nchochokera mwa Ayuda. 23Koma ikudza nthaŵi, ndipo yafika kale, pamene anthu opembedza kwenikweni adzapembedza Atate mwauzimu ndi moona. Atate amafuna anthu otere kuti ndiwo azimpembedza. 24Mulungu ndi mzimu, ndipo ompembedza Iye ayenera kumpembedza mwauzimu ndi moona.” 25Maiyo adati, “Ndikudziŵa kuti akudza Mpulumutsi wolonjezedwa uja. Iyeyo akadzafika, adzatifotokozera zonse.” 26Yesu adamuuza kuti, “Ndine amene, Ineyo amene ndikulankhula nanu, mai.”
27Nthaŵi yomweyo ophunzira ake a Yesu adafika, ndipo ankadabwa kuti Iye akucheza ndi mkazi. Komabe panalibe amene adamufunsa kuti, “Zakhala bwanji?” Kapena kuti, “Bwanji mukulankhula naye?” 28Maiyo adasiya mtsuko wake napita ku mudzi nkukauza anthu kuti, 29“Tiyeni, mukaone munthu amene wandiwuza zonse zimene ine ndidachita. Kodi ameneyu sangakhale Mpulumutsi wolonjezedwa uja kapena?” 30Apo anthuwo adatuluka m'mudzimo kubwera kwa Yesu,
31Nthaŵi imeneyo ophunzira ake a Yesu ankamupempha kuti, “Aphunzitsi, idyani.” 32Koma Iye adati, “Ine ndili nacho chakudya chimene inu simukuchidziŵa.” 33Pamenepo ophunzirawo adayamba kufunsana kuti, “Kodi kapena wina wadzaŵapatsa kale chakudya?” 34Koma Yesu adati, “Chakudya changa nkuchita zimene afuna Atate amene adandituma, kuti nditsirize ntchito imene Iwo adandipatsa. 35Paja anthu amati, ‘Ikapita miyezi inai, ndiye kuti yafika nyengo yokolola.’ Koma ndithu, taonani m'mindamu, kodi simukuwona kuti mbeu zacha kale kudikira kholola? 36Okolola ayamba kale kulandira malipiro, ndipo akututira mbeu ku moyo wosatha, kuti obzala ndi okolola akondwere pamodzi. 37Paja amanenadi zoona aja amati, ‘Wobzala ndi wina, wokolola ndi winanso.’ 38Ine ndidakutumani kukakolola mbeu zimene simudagwirirepo ntchito. Anthu ena ndiwo adagwira ntchito, inu mwangolandirapo phindu la ntchito yaoyo.”
39Asamariya ambiri a m'mudzi muja adakhulupirira Yesu chifukwa cha umboni wa mai uja, wakuti, “Iye wandiwuza zonse zimene ndidachita.” 40Tsono pamene Asamariyawo adafika kwa Yesu, adampempha kuti akhale nao kwaoko. Ndipo adakhaladi komweko masiku aŵiri. 41Pamenepo anthu enanso ambiri adakhulupirira chifukwa cha mau a Yesu. 42Mwakuti adauza mai uja kuti, “Takhulupirira tsopano, osati chifukwa cha mau ako, koma chifukwa tadzimvera tokha. Tadziŵa kuti ameneyu ndi Mpulumutsidi wa anthu a pa dziko lonse lapansi.”
Yesu achiritsa mwana wa nduna ya mfumu
(Mt. 8.5-13; Lk. 7.1-10)
43Atapita masiku aŵiriwo, Yesu adachoka napita ku Galileya. 44#Mt. 13.57; Mk. 6.4; Lk. 4.24Mwiniwakeyo anali atanena kuti, “Mneneri, anthu akwao samchitira ulemu.” 45#Yoh. 2.23Komabe pamene adafika ku Galileya, Agalileya adamlandira popeza kuti eniakewo nawonso adaapita ku Yerusalemu ku chikondwerero cha Paska, ndipo adaaona zonse zimene Yesu adaachita pachikondwereropo.
46 #
Yoh. 2.1-11
Yesu adapitanso ku mudzi wa Kana ku Galileya, kumene Iye adaasandutsa madzi vinyo kuja. Panali Nduna ina ya mfumu imene mwana wake ankadwala ku Kapernao. 47Pamene adamva kuti Yesu wafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya, adadza kwa Iye nampempha kuti apite naye ku Kapernao, kuti akachiritse mwana wake amene anali pafupi kufa. 48Yesu adamuuza kuti, “Mukapanda kuwona zizindikiro ndi zozizwitsa, simukhulupirira ai.” 49Ndunayo idati, “Ndapota nanu Ambuye, tiyeni mwana wanga asanafe.” 50Yesu adamuuza kuti, “Pitani! Mwana wanu wachira.” Munthuyo adakhulupiriradi mau a Yesuwo, ndipo adapita kwao. 51Pa njira adakumana ndi antchito ake, ndipo iwo adamuuza kuti, “Mwana wanu wachira.” 52Adaŵafunsa za nthaŵi imene adachira mwanayo, iwo nkunena kuti, “Malungo ake adamleka dzulo nthaŵi ya 1 koloko masana.” 53Bamboyo adazindikira kuti inali nthaŵi yomwe Yesu adaamuuza kuti, “Mwana wanu wachira.” Tsono iye adakhulupirira pamodzi ndi onse a m'banja mwake.
54Ichi chinali chizindikiro chachiŵiri chimene Yesu adaonetsa atafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya.
Currently Selected:
Yoh. 4: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi

: