YouVersion Logo
Search Icon

Lk. 13

13
Anthu osatembenuka mtima adzafa
1Anthu ena amene anali pomwepo adadza kwa Yesu, nayamba kumsimbira za Agalileya amene Pilato#13.1: Pilato: Ameneyu anali bwanamkubwa ku Yudeya. Agalileya adaabwera ku Yerusalemu m'dera la Yudeya kudzapembedza ku Nyumba ya Mulungu. Koma iwo ankautsa nkhondo ndi Aroma kaŵirikaŵiri. Tsono Pilato adaphetsa ena mwa iwo pamene ankapereka nsembe zao. Sitiŵerenganso pena paliponse za kupha kumeneku. adaalamula kuti aphedwe, pamene iwo ankapereka nsembe zao kwa Mulungu. 2Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi mukuyesa kuti Agalileyawo anali ochimwa koposa Agalileya ena onse, popeza kuti adaphedwa motere? 3Iyai, koma mukapanda kutembenuka mtima, inunso mudzaonongedwa ngati iwo aja. 4Nanga anthu aja 18 amene nyumba yosanja idaŵagwera ku Siloamu#13.4: Siloamu: Sitiŵerenganso pena paliponse za mbiri imeneyi ai. Onani mau ofotokozera Yoh. 9.7. nkuŵapha? Kodi mukuyesa kuti iwowo anali ophwanya malamulo koposa anthu ena onse okhala m'Yerusalemu? 5Iyai, koma mukapanda kutembenuka mtima, inunso mudzaonongedwa ngati iwo aja.”
Fanizo la mkuyu wosabala
6Yesu adaŵaphera fanizo, adati, “Munthu wina anali ndi mkuyu wobzalidwa m'munda wake wamphesa. Adakafunamo zipatso, koma osazipeza. 7Tsono adauza wosamala mundawo kuti, ‘Papita zaka zitatu tsopano ndikufuna zipatso mu mkuyu uwu, koma osazipeza. Udule tsono. Ukugugitsiranji nthaka?’ 8Koma iye adati, ‘Ambuye, baulekani chaka chino chokha. Ndiukumbira pa tsinde nkuuthira manyowa. 9Ukadzabala zipatso chaka chamaŵa, zidzakhala bwino. Koma ukakapanda kubala, apo mudzaudule.’ ”
Yesu achiritsa mai wokhota msana pa Sabata
10Tsiku lina la Sabata Yesu ankaphunzitsa m'nyumba ina yamapemphero. 11M'menemo munali mai wina amene anali ndi mzimu woipa umene udamudwalitsa zaka 18. Anali ndi msana wokhota, mwakuti sankatha konse kuŵeramuka. 12Pamene Yesu adamuwona, adamuitana namuuza kuti, “Mai inu, mwamasuka ku matenda anu.” 13Adamsanjika manja, ndipo pompo maiyo adaongoka, nayamba kutamanda Mulungu.
14 # Eks. 20.9, 10; Deut. 5.13, 14 Koma mkulu wa nyumba yamapemphero ija adakwiya, poona kuti Yesu wachiritsa munthu pa tsiku la Sabata. Tsono mkuluyo adauza anthu onse kuti, “Pali masiku asanu ndi limodzi antchito. Muzibwera masiku ameneŵa kudzachiritsidwa, osati pa tsiku la Sabata ai” 15Koma Ambuye adati, “Anthu achiphamaso inu, kodi suja nonsenu mumamasula ng'ombe zanu kapena abulu anu pa tsiku la Sabata kukaŵamwetsa madzi? 16Nanga maiyu, amene ali mwana wa Abrahamu, ndipo Satana adaamumanga zaka 18, kodi sikunayenera kuti amasulidwe ku nsinga imeneyi pa tsiku la Sabata?” 17Yesu atanena zimenezi, adani ake onse adachita manyazi. Koma anthu ena onse adakondwera chifukwa cha ntchito zodabwitsa zimene Iye ankachita.
Fanizo la njere yampiru ndi la chofufumitsira buledi
(Mt. 13.31-33; Mk. 4.30-32)
18Yesu adati, “Kodi Ufumu wa Mulungu uli ngati chiyani, ndipo ndingauyerekeze ndi chiyani? 19Uli ngati njere ya mbeu ya mpiru imene munthu adakaifesa m'munda mwake. Idamera nisanduka mtengo, mbalame zamumlengalenga nkumabwera kudzamanga zisa pa nthambi zake.”
20Yesu adatinso, “Ndingayerekezenso ndi chiyani Ufumu wa Mulungu? 21Ulinso ngati chofufumitsira buledi, chimene mai wina adachisanganiza ndi ufa wokwanira miyeso itatu, mpaka mtanda wonse udafufuma.”
Za khomo lophaphatiza
(Mt. 7.13-14, 21-23)
22Pa ulendo wake wopita ku Yerusalemu, Yesu ankayendera mizinda ndi midzi akuphunzitsa. 23Munthu wina adamufunsa kuti, “Ambuye, kodi adzapulumuka ndi anthu oŵerengeka okha?” Yesu adayankha kuti, 24“Yesetsani kuloŵera pa khomo lophaphatiza, pakuti kunena zoona anthu ambiri adzafuna kuloŵa, koma adzalephera.
25“Mwini nyumba adzanyamuka nkutseka pa khomo. Pamenepo, okhala panjanu mudzayamba kugogoda nkumanena kuti, ‘Ambuye, titsekulireni.’ Koma Iye adzakuyankhani kuti, ‘Sindikudziŵa kumene mukuchokera.’ 26Apo inuyo mudzayamba kunena kuti, ‘Pajatu tinkadya ndi kumamwa nanu pamodzi, ndipo Inuyo munkaphunzitsa m'miseu ya m'mizinda mwathu.’ 27#Mas. 6.8Koma Iye adzakuuzani kuti, ‘Pepani, sindikudziŵa kumene mukuchokera. Chokani apa nonsenu, anthu ochita zoipa.’ 28#Mt. 22.13; 25.30#Mt. 8.11, 12Apo mudzayamba kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzaona Abrahamu ndi Isaki ndi Yakobe ndi aneneri onse mu Ufumu wa Mulungu, inuyo mukuponyedwa kunja. 29Anthu adzachokera kuvuma ndi kuzambwe, kumpoto ndi kumwera, nadzakhala podyera mu Ufumu wa Mulungu. 30#Mt. 19.30; 20.16; Mk. 10.31Pamenepo amene ali otsirizira adzakhala oyambirira, ndipo amene ali oyambirira adzakhala otsirizira.”
Yesu alira chifukwa cha Yerusalemu
(Mt. 23.37-39)
31Nthaŵi yomweyo Afarisi ena adadzauza Yesu kuti, “Muchokeko kuno, chifukwa Herode akufuna kukuphani.” 32Yesu adati, “Pitani kaiwuzeni nkhandweyo kuti ndikutulutsa mizimu yoipa ndiponso ndikuchiritsa anthu lero ndi maŵa, ndipo mkucha mpamene nditsirize ntchito yanga. 33Komabe ndiyenera kupitirira ndi ulendo wanga lero ndi maŵa ndi mkucha, pakuti mneneri sangafere kwina koma ku Yerusalemu.
34 # 2Es. 1.30 “Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri nkuŵaponya miyala anthu amene Mulungu amakutumizira. Nkangati ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa anthu ako, monga momwe nkhuku imasonkhanitsira anapiye ake pansi pa mapiko ake, iwe nkumakana. 35#Mas. 118.26Ndithu nyumba yanu yaikuluyi idzasanduka bwinja. Ndipo ndikunenetsa kuti simudzandiwonanso konse mpaka mudzati, ‘Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye.’ ”

Currently Selected:

Lk. 13: BLY-DC

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in