Lk. 20:46-47
Lk. 20:46-47 BLY-DC
“Chenjera nawoni aphunzitsi a Malamulo. Amakonda kuyenda atavala mikanjo yaitali, ndi kuti anthu aziŵalonjera mwaulemu pa misika. Amakonda mipando yaulemu kwambiri m'nyumba zamapemphero ndiponso malo olemekezeka pa maphwando. Koma amaŵadyera chuma chao azimai amasiye, nkumapemphera mapemphero ataliatali monyengezera. Anthu ameneŵa adzalangidwa koposa.”