Lk. 8
8
Azimai ena aperekeza Yesu
1Pambuyo pake Yesu adanka nayendera mizinda ndi midzi akulalika ndi kuuza anthu Uthenga Wabwino wonena za ufumu wa Mulungu. Ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja anali naye. 2#Mt. 27.55, 56; Mk. 15.40, 41; Lk. 23.49Panalinso azimai ena amene Yesu adaaŵatulutsa mizimu yoipa ndi kuŵachiza nthenda zina. Azimaiwo ndi aŵa: Maria, wotchedwa Magadalena, (amene mwa iye mudaatuluka mizimu yoipa isanu ndi iŵiri); 3Yohana, mkazi wa Kuza, kapitao wa Herode; Suzana, ndiponso azimai ena ambiri amene ndi ndalama zao ankathandiza Yesu ndi ophunzira ake.
Fanizo la wofesa mbeu
(Mt. 13.1-9; Mk. 4.1-9)
4Anthu ambirimbiri ochokera ku midzi yonse adasonkhana kumene kunali Yesu. Tsono Iye adaŵaphera fanizo. Adati, 5“Munthu wina adaapita kukafesa mbeu. Akufesa choncho, mbeu zina zidagwera m'njira. Zidapondedwa, ndipo mbalame zidazitolatola. 6Mbeu zina zidagwera pa nthaka yapathanthwe. Zidamera, koma nkufota, chifukwa zidaasoŵa chinyontho. 7Mbeu zina zidagwera pa zitsamba zaminga. Zitsambazo pokula zidalanda chakudya cha mbeu zija. 8Koma mbeu zina zidagwera pa nthaka yabwino. Zidakula nkubereka. Ngala iliyonse inali ndi njere makumi khumi.” Tsono Yesu adalankhula mokweza mau kuti, “Amene ali ndi makutu akumva, amve!”
Za cholinga cha mafanizo
(Mt. 13.10-17; Mk. 4.10-12)
9Ophunzira a Yesu adamufunsa za tanthauzo la fanizoli. 10#Yes. 6.9Tsono Iye adati, “Inuyo Mulungu adakuululirani zobisika zokhudza Ufumu wake. Koma enaŵa amazimvera m'mafanizo chabe, kuti choncho ayang'ane, koma asapenye, ndipo amve, koma asamvetse.”
Tanthauzo la fanizo la wofesa mbeu
(Mt. 13.18-23; Mk. 4.13-20)
11“Tanthauzo la fanizoli ndi ili: Mbeu zija ndi mau a Mulungu. 12Mbeu zogwera m'njira zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu. Koma Satana amabwera, nkuchotsa mau aja m'mitima mwao, kuwopa kuti angakhulupirire ndi kupulumuka. 13Mbeu zogwera pa nthaka yapathanthwe zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, nkuŵalandira ndi chimwemwe. Tsono popeza kuti alibe mizu yozama, amangokhulupirira kanthaŵi pang'ono chabe, mwakuti pa nthaŵi ya kuyesedwa, amabwerera m'mbuyo. 14Mbeu zogwera pa zitsamba zaminga zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, koma pambuyo pake nkhaŵa, kukondetsa chuma, ndiponso khumbo la zokondweretsa za moyo uno zimaŵalepheretsa, ndipo zipatso zao sizikhwima. 15Koma mbeu zogwera pa nthaka yabwino zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, naŵasunga mu mtima woona ndi wabwino, ndipo amalimbikira mpaka kubereka zipatso.”
Za nyale yovundikira ndi mbiya
(Mk. 4.21-25)
16 #
Mt. 5.15; Lk. 11.33 “Palibe munthu amene amayatsa nyale nkuivundikira ndi mbiya, kapena kuibisa kunsi kwa bedi. Koma amaiika pa malo oonekera, kuti anthu oloŵa m'nyumba aone kuŵala kwake. 17#Mt. 10.26; Lk. 12.2Pajatu chinthu chilichonse chobisika chidzaululuka, ndipo chilichonse chachinsinsi chidzadziŵika nkuwonekera poyera.
18 #
Mt. 25.29; Lk. 19.26 “Nchifukwa chake muzisamala m'mene mumamvera mau. Pajatu amene ali nako kanthu, adzamuwonjezera zina. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene akuyesa kuti ali nakoko adzamlandabe.”
Amai ake ndi abale ake a Yesu
(Mt. 12.46-50; Mk. 3.31-35)
19Amai ake ndi abale ake a Yesu adabwera kunyumbako, koma chifukwa cha kuchuluka kwa anthu, adaalephera kufika pamene panali Iyepo. 20Tsono munthu wina adauza Yesu kuti, “Amai anu ndi abale anu ali panjapa, akufuna kukuwonani.” 21Koma Yesu adati, “Inetu amai anga ndi abale anga ndi anthu amene amamva mau a Mulungu, nkumachitadi zimene mauwo akunena.”
Yesu athetsa namondwe
(Mt. 8.23-27; Mk. 4.35-41)
22Tsiku lina Yesu adaloŵa m'chombo pamodzi ndi ophunzira ake. Adaŵauza kuti, “Tiyeni tiwoloke, tipite ku tsidya ilo la nyanja.” Ndipo adanyamukadi. 23Pamene ankaoloka Yesu adagona tulo. Tsono padauka namondwe panyanjapo, mpaka chombo chija chidayamba kudzaza ndi madzi ndipo iwo anali pafupi kumira. 24Pamenepo ophunzira aja adadza kwa Yesu namudzutsa, adati, “Ambuye, Ambuye, tikumiratu!” Iye adadzuka, naletsa mphepoyo ndi mafunde amphamvuwo. Zidalekadi ndipo padagwa bata. 25Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi chikhulupiriro chanu chili kuti?” Koma iwo adaagwidwa ndi mantha nathedwa nzeru, nkumafunsana kuti, “Kodi ameneyu ndi munthu wotani? Angolamula mphepo ndi madzi omwe, izo nkumumveradi.”
Yesu achiritsa munthu wogwidwa ndi mizimu yoipa
(Mt. 8.28-34; Mk. 5.1-20)
26Iwo adafika ku dziko la Ageregesa,#8.26: Ageregesa: Ameneŵa ndi anthu okhala ku Geresa, kadziko kamene kali kuvuma kwa nyanja ya Galileya. Kadzikoka kamadziŵikanso ndi maina aŵa: “Gadara”: Mt. 8.28; ndi Geregesa. limene lidapenyana ndi Galileya. 27Pamene Yesu adafika pa mtunda, munthu wina wochokera ku mudzi wakomweko, adadzakumana naye. Munthuyo adaali ndi mizimu yoipa, ndipo kuyambira kale sankavalanso zovala. Sankakhala m'nyumba, koma ku manda. 28Pamene iye adaona Yesu, adafuula nadzigwetsa ku mapazi ake, ndipo adanena mokweza mau kuti, “Kodi ndakuputani chiyani Inu Yesu, Mwana wa Mulungu Wopambanazonse? Ndakupembani, musandizunze.” 29Adaatero chifukwa Yesu anali atalamula mzimu woipawo kuti utuluke mwa munthuyo. (Ndiye kuti kaŵirikaŵiri ukamugwira, anthu ankamumanga manja ndi maunyolo, nkumumanganso miyendo ndi zitsulo kuti amugwiritse bwino. Koma iyeyo ankazingomwetsula zomangirazo, ndipo mzimuwo unkamupirikitsira ku thengo.) 30Tsono Yesu adamufunsa munthuyo kuti, “Dzina lako ndani?” Iye adayankha kuti, “Dzina langa ndine Chigulu#8.30: Chigulu: Pa Chigriki mau ake amati “Legion”, pa Chilatini “Legio”, ndiye kuti gulu la asilikali zikwi zisanu ndi chimodzi. Wamisala uja adaadzitcha dzina limeneli kutanthauza kuti mizimu yoipa imene idaali mwa iye inali yochuluka ngati gulu lalikulu la asilikali.,” chifukwa mizimu yoipa yochuluka inali itamuloŵa. 31Kenaka mizimuyo idapempha Yesu kuti asailamule kuti ikaloŵe ku chiphompho chao.
32Pafupi pomwepo, pachitunda poteropo, pankadya gulu lalikulu la nkhumba. Tsono mizimu yoipa ija idapempha Yesu kuti ailole ikaloŵe m'nkhumbazo. Yesu adailoladi. 33Iyo idatuluka, nkukaloŵadi m'nkhumbazo. Pomwepo gulu lonselo lidaguduka kutsika chitunda chija mwaliŵiro, nkukadziponya m'nyanja, mpaka kufera m'madzimo.
34Oŵeta nkhumbazo ataona zimenezi, adathaŵa, nakauza anthu ku mzinda ndi ku midzi. 35Anthuwo adatuluka kuti akaone zimene zidaachitikazo. Atafika kumene kunali Yesuko, adapeza munthu amene adaamtulutsa mizimu yoipa uja, atakhala pansi ku mapazi a Yesu, atavala, misala ija itatha. Anthuwo adagwidwa ndi mantha. 36Anzao amene adaaonerera zonse zikuchitika, adaŵasimbira m'mene munthu wamizimuyo adaamchiritsira. 37Apo anthu onse a ku malo ozungulira Geregesa adapempha Yesu kuti achoke kumeneko, chifukwa iwo anali ndi mantha aakulu. Choncho Yesu adaloŵa m'chombo, nkumabwerera ku tsidya.
38Munthu amene adaamtulutsa mizimu yoipa uja adapempha Yesu kuti apite nao. Koma Yesu adamubweza namuuza kuti, 39“Iyai, iwe bwerera kwanu, ukafotokoze zazikulu zimene Mulungu wakuchitira.” Munthuyo adapitadi kwao nkumakalengeza mumzinda monse zazikulu zimene Yesu adaamchitira.
Yesu achiza mwana wa Yairo ndi mai wina
(Mt. 9.18-26; Mk. 5.21-43)
40Pamene Yesu adafikanso ku tsidya, chinamtindi cha anthu chidamchingamira, popeza kuti onse ankamudikira. 41Tsono kudafika munthu wina, dzina lake Yairo, amene anali mmodzi mwa akulu a nyumba yamapemphero. Iye adadzigwetsa ku mapazi a Yesu, nayamba kumdandaulira kuti apite kunyumba kwake, 42chifukwa mwana wake wamkazi anali pafupi kufa. Anali wa zaka khumi ndi ziŵiri, ndipo mwana anali yekhayo.
Pamene Yesu ankapita kumeneko, anthu aja ankamupanikiza. 43Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziŵiri. Adaamwaza chuma chake chonse kulipira asing'anga, koma panalibe ndi mmodzi yemwe wotha kumchiza. 44Iyeyu adafika cha kumbuyo kwa Yesu, nakhudza mphonje ya chovala chake, ndipodi nthaŵi yomweyo matenda a msambowo adaleka. 45Pompo Yesu adafunsa kuti, “Ndani wandikhudza?” Poti onse ankangoti, “Kaya,” Petro adati, “Aphunzitsi, anthu onseŵa akuzungulirani ndipo akukupanikizani.” 46Koma Yesu adati, “Iyai, wina wandikhudza ndithu. Ndazindikira kuti mphamvu zina zatuluka mwa Ine.” 47Pamene mai uja adaona kuti sangathenso kudzibisa, adadza monjenjemera nadzigwetsa ku mapazi a Yesu. Adafotokoza pamaso pa anthu onse aja chifukwa chimene adaakhudzira Yesu, ndiponso m'mene adachirira nthaŵi yomweyo. 48Apo Yesu adamuuza kuti, “Inu mwana wanga, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani. Pitani ndi mtendere.”
49Yesu akulankhulabe, kudafika munthu wina kuchokera kunyumba kwa mkulu wa nyumba yamapemphero uja. Adamuuza mkuluyo kuti, “Mwana uja watsirizika. Musaŵavutenso Aphunzitsiŵa.” 50Yesu atamva mauwo adauza Yairo kuti, “Musaope ai, inu mungokhulupira, ndipo mwanayo akhalanso bwino.” 51Pamene Yesu adafika kunyumba kuja, sadalole kuti wina aliyense aloŵe naye, koma Petro, Yohane ndi Yakobe, ndiponso bambo wake wa mwanayo ndi mai wake. 52Anthu onse ankalira ndi kubuma. Koma Yesu adati, “Musalire, mwanayutu sadamwalire ai, ali m'tulo chabe.” 53Pamenepo anthuwo adayamba kumseka monyodola, chifukwa ankadziŵa kuti mwanayo wamwalira basi. 54Yesu adagwira mwanayo pa dzanja nanena mokweza mau kuti, “Mwana iwe, dzuka!” 55Pomwepo moyo wake udabwereramo, iyeyo nkudzukadi nthaŵi yomweyo. Kenaka Yesu adaŵauza kuti ampatse chakudya mtsikanayo. 56Makolo ake aja adazizwa kwambiri, koma Yesu adaŵalamula kuti asauze wina aliyense zimene zidaachitikazo.
Currently Selected:
Lk. 8: BLY-DC
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi

: