9
Pangano la Mulungu ndi Nowa
1Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake aamuna nati kwa iwo, “Berekanani ndipo muchulukane ndi kudzaza dziko lapansi. 2Nyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za mlengalenga, ndi chamoyo chilichonse chokwawa, ndiponso nsomba zonse za ku nyanja; zidzakuopani ndipo ndazipereka kuti muzilamulire. 3Tsopano chamoyo chilichonse chidzakhala chakudya chanu. Monga momwe ndinakupatsirani ndiwo zamasamba, tsopano ndikupatsaninso nyama iliyonse.
4“Koma musamadye nyama imene ikanali ndi magazi oyenda. 5Aliyense wopha munthu adzaphedwa, nyama iliyonse yopha munthu idzaphedwa, munthu aliyense wopha munthu mnzake, adzaphedwa.
6“Aliyense wopha munthu,
adzaphedwanso ndi munthu;
pakuti Mulungu analenga munthu
mʼchifanizo chake.
7Inu muberekane ndi kuchulukana kuti mudzaze dziko lonse lapansi ndi kuligonjetsa.”
8Mulungu anawuza Nowa ndi ana ake kuti, 9“Tsopano Ine ndapangana ndi iwe ndi zidzukulu zako zamʼtsogolomo, 10pamodzi ndi zamoyo zonse, mbalame, ziweto ndi nyama zonse za kuthengo, ndi zonse zimene zinatuluka mʼchombo pamodzi ndi iwe. 11Pangano langa ndi ili: Ine ndilonjeza kuti sindidzawononganso zamoyo ndi madzi a chigumula. Chigumula sichidzawononganso dziko lapansi.”
12Ndipo Mulungu anati, “Ine ndikupereka chizindikiro ichi cha pangano langa la pakati pa Ine ndi iwe, ana ako, zamoyo zonse, pamodzi ndi mibado ya mʼtsogolo. 13Ndayika utawaleza wanga mʼmitambo, ndipo chidzakhala chizindikiro cha pangano langa ndi dziko lapansi. 14Nthawi zonse pakakhala mitambo mu mlengalenga ndipo utawaleza uwoneka, 15ndizikumbukira pangano langa pakati pa Ine ndi inu ndi zolengedwa zonse. Madzi sadzakhalanso chigumula chowononga dziko lapansi. 16Utawaleza ukamadzaoneka mʼmitambo, ndidzawuona ndi kukumbukira pangano losatha pakati pa Mulungu ndi zamoyo zonse pa dziko lapansi.”
17Choncho Mulungu anati kwa Nowa, “Ichi ndiye chizindikiro cha pangano limene ndalichita pakati pa Ine ndi zamoyo zonse pa dziko lapansi.”
Ana Aamuna a Nowa
18Ana aamuna a Nowa amene anatuluka mʼchombo muja anali Semu, Hamu ndi Yafeti. Hamu anali abambo ake a Kanaani. 19Ana aamuna a Nowa amenewa ndiwo anali makolo a anthu onse pa dziko lapansi.
20Nowa anali munthu woyamba kulima munda wamphesa. 21Tsiku lina pamene Nowa anamwako vinyo wa zipatso za mʼmundawo analedzera ndipo anavula zovala zake zonse ndi kugona mu tenti yake ali maliseche. 22Hamu, abambo ake a Kanaani ataona kuti abambo ake ali maliseche anakawuza abale ake awiri aja omwe anali panja. 23Koma Semu ndi Yafeti anatenga chofunda nachiyika pa mapewa awo; ndipo anayenda chamʼmbuyo naphimba umaliseche wa abambo awo. Anafulatira kuti asaone umaliseche wa abambo awo.
24Nowa atadzuka, kuledzera kutatha, ndikudziwa zimene mwana wake wamngʼono wamwamuna uja anamuchitira, 25anati,
“Atembereredwe Kanaani!
Adzakhala kapolo
wa pansi kwenikweni kwa abale ake.”
26Anatinso,
“Atamandike Yehova, Mulungu wa Semu!
Kanaani akhale kapolo wa Semu.
27Mulungu akulitse dziko la Yafeti;
Yafeti alandire madalitso pamodzi ndi Semu,
ndipo Kanaani akhale kapolo wawo.”
28Chitatha chigumula, Nowa anakhala ndi moyo zaka 350. 29Anamwalira ali ndi zaka 950.