Yoh. 10

10
Fanizo la khola la nkhosa
1“Kunena zoona, munthu woloŵa m'khola la nkhosa osadzera pa khomo, koma kuchita kukwerera pena, ameneyo ndi wakuba ndi wolanda. 2Koma munthu woloŵera pa khomo ndiye mbusa wa nkhosazo. 3Iyeyo mlonda amamtsekulira. Nkhosa zimamva mau ake, ndipo amaziitana maina nkhosa zakezo, nazitulutsa. 4Akazitulutsa nkhosa zake zonse, amazitsogolera, izo nkumamtsatira, chifukwa zimadziŵa mau ake. 5Mlendo sizidzamtsatira ai, zidzamthaŵa, chifukwa sizidziŵa mau a alendo.”
6Yesu adaŵaphera fanizoli, koma iwo sadamvetse zimene ankaŵauzazo.
Yesu ndiye mbusa wabwino
7Tsono Yesu adatinso, “Ndithu ndikunenetsa kuti Ine ndine khomo la nkhosa. 8Ena onse amene adabwera Ine ndisanafike, ngakuba ndi olanda, koma nkhosa sizinaŵamvere. 9Khomo ndine. Munthu akaloŵera pa Ine, adzapulumuka. Azidzaloŵa ndi kutuluka, ndipo adzapeza chakudya. 10Wakuba amangodzera kuba, kupha ndi kuwononga. Koma Ine ndidabwera kuti nkhosazo zikhale ndi moyo, moyo wake wochuluka.
11 # Mphu. 18.13 “Ine ndine mbusa wabwino. Mbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake. 12Koma wolembedwa ntchito chabe akaona mmbulu ulikudza, amazisiya nkhosazo iye nkuthaŵa. Amatero popeza kuti si mbusa weniweni, ndipo nkhosa si zake ai. Tsono mmbulu uja umagwirapo zina, zina nkumwazikana. 13Wolembedwa ntchito uja amathaŵa, chifukwa amangotsata malipiro chabe, ndipo salabadirako za nkhosazo. 14#Mt. 11.27; Lk. 10.22Mbusa wabwino ndine. Nkhosa zanga ndimazidziŵa, ndipo izozo Ineyo zimandidziŵa, 15monga momwe Atate amadziŵira Ine, nanenso nkuŵadziŵa Atatewo. Ndimatayirapo moyo wanga pa nkhosazo. 16Ndili nazo nkhosa zina zimene sizili za m'khola lino. Zimenezonso ndiyenera kuzikusa. Zidzamva mau anga, ndipo padzakhala gulu limodzi mbusa wakenso mmodzi.
17“Nchifukwa chake Atate amandikonda, popeza kuti ndikupereka moyo wanga kuti ndikautengenso. 18Palibe munthu wondilanda moyo wangawu, koma ndikuupereka ndekha. Ndili nazo mphamvu zoutaya moyo wanga, ndili nazonso mphamvu zoutenganso. Udindo umenewu ndidaulandira kwa Atate anga.”
19Anthu adaayambanso kutsutsana okhaokha chifukwa cha mau ameneŵa. 20Ambiri mwa iwo ankati, “Ali ndi mizimu yoipa, ndipo wapenga. Bwanji mukumumveranso Iyeyu?” 21Koma ena ankati, “Mau ameneŵa si a munthu wogwidwa ndi mizimu yoipa. Kodi mizimu yoipa nkupenyetsa anthu akhungu?”
Ayuda akana Yesu
22 # 1Am. 4.36, 52-59; 2Am. 1.18; 10.5 Ku Yerusalemu kunali chikondwerero chokumbukira kuperekedwanso kwa Nyumba ya Mulungu. Inali nyengo yozizira. 23Yesu ankangodziyendera m'Nyumba ya Mulungu, m'khonde lotchedwa Khonde la Solomoni. 24Anthu adamzinga namufunsa kuti, “Kodi udzaleka liti kutikayikitsa? Ngati ndiwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, tiwuze momveka.” 25Yesu adati, “Ndidakuuzani kale, komabe simukhulupirira. Ntchito zimene ndimachita m'dzina la Atate anga, ndizo zimandichitira umboni. 26Koma inu simukhulupirira konse, chifukwa simuli a m'gulu la nkhosa zanga. 27Nkhosa zanga zimamva mau anga. Ine ndimazidziŵa, ndipo zimanditsatira. 28Ndimazipatsa moyo wosatha, ndipo sizidzatayika konse. Palibe munthu wodzazilanda m'manja mwanga. 29#Lun. 3.1Atate anga amene adandipatsa nkhosazo amapambana onse, ndipo palibe amene angathe kuzilanda m'manja mwao. 30Ine ndi Atate ndife amodzi.”
31Anthuwo adatolanso miyala kuti amlase. 32Yesu adaŵafunsa kuti, “Ndakuwonetsani ntchito zabwino zambiri zimene Atate adandichititsa. Nanga mwa zimenezi ntchito imene mukuti mundiponyere miyala ndi iti?” 33#Lev. 24.16Anthu aja adamuyankha kuti, “Sitikufuna kukuponya miyala chifukwa cha ntchito yabwino ai, koma chifukwa ukunyoza Mulungu. Iwe, amene uli munthu chabe, ukudziyesa Mulungu.” 34#Mas. 82.6 Yesu adati, “Kodi m'Malamulo mwanu suja mudalembedwa kuti ‘Mulungu adati, Ndinu milungu?’ 35Paja mau a m'Malembo ngoona mpaka muyaya, ndipo Mwiniwakeyo adaŵatcha milungu anthu aja Iye ankalankhula nawoŵa. 36Inetu Atate adandipatula nandituma pansi pano. Tsono inuyo munganene bwanji kuti ndikunyoza Mulungu, chifukwa ndati ndine Mwana wa Mulungu? 37Ngati sindichita ntchito zimene Atate anga adandipatsa, musandikhulupirire. 38Koma ngati ndimazichitadi, khulupirirani ntchitozo, ngakhale simukhulupirira Ine. Apo mudzadziŵa mosapeneka konse kuti Atate amakhala mwa Ine, ndipo Ine ndimakhala mwa Atate.”
39Pamenepo anthu aja adafunanso kumgwira, koma Iye adazemba.
40 # Yoh. 1.28 Yesu adabwereranso kutsidya kwa mtsinje wa Yordani, kumene Yohane ankabatizira anthu poyamba paja, ndipo adakhala komweko. 41Anthu ambiri adadza kwa Iye, nkumanena kuti, “Yohane sadachite chizindikiro chozizwitsa ai, koma zonse zimene ankanena za Munthuyu zinali zoonadi.” 42Motero anthu ambiri adakhulupirira Yesu kumeneko.

S'ha seleccionat:

Yoh. 10: BLY-DC

Subratllat

Comparteix

Copia

None

Vols que els teus subratllats es desin a tots els teus dispositius? Registra't o inicia sessió