Gen. 7
7
Za chigumula
1Chauta adauza Nowa kuti, “Loŵa m'chombo iwe pamodzi ndi banja lako. Iwe wekha ndakupeza kuti ndiwe wochita zondikondweretsa mu mbadwo uno. 2Tsono tenga magulu asanu ndi aŵiri a nyama, ziŵiriziŵiri, yaimuna ndi yaikazi, zimene amaperekera nsembe, ndipo utengenso nyama ziŵiriziŵiri, yaimuna ndi yaikazi, zosaperekera nsembe. 3Utengekonso mbalame ziŵiriziŵiri za mtundu uliwonse, magulu asanu ndi aŵiri. Uchite zimenezi pofuna kuti nyama ndi mbalame za mitundu yonse zisungidwe ndi moyo, ndipo kuti zidzaswanenso pa dziko lapansi. 4Pakangopita masiku asanu ndi aŵiri, ndidzagwetsa mvula pa dziko lapansi masiku makumi anai, usana ndi usiku, kuti zife zamoyo zonse zimene ndidazipanga.” 5Ndipo Nowa adachita zonse zimene Mulungu adamlamula.
6Nowa anali wa zaka 600 pamene chigumulacho chidafika pa dziko lapansi. 7#Mt. 24.38, 39; Lk. 17.27 Iyeyo ndi mkazi wake ndi ana ake aamuna ndi akazi ao adaloŵa m'chombo, kuthaŵa chigumulacho. 8Nyama zazimuna ndi zazikazi zimene anthu amaperekera nsembe, mbalame pamodzi ndi nyama zokwaŵa zomwe, 9Nowa adaloŵa nazo m'chombo, monga Mulungu adaalamulira. 10Patangopita masiku asanu ndi aŵiri, chigumula chidafika pa dziko lonse lapansi.
11 #
2Pet. 3.6
Pa 17, mwezi wachiŵiri, Nowa ali wa zaka 600, akasupe onse a madzi ambiri okhala pansi pa dziko adatumphuka, ndipo kuthambo kudatsekukanso, kuti madzi akhuthuke. 12Choncho mvula idagwa pa dziko lapansi masiku makumi anai, usana ndi usiku. 13Pa tsiku lomwelo, Nowa ndi mkazi wake, pamodzi ndi ana ake aamuna, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi akazi ao, adaloŵa m'chombomo. 14Iwowo adaloŵa m'chombo pamodzi ndi mtundu uliwonse wa nyama zakuthengo, zoŵeta, nyama zokwaŵa ndi mbalame za mtundu uliwonse. 15Nowa adaloŵa m'chombomo pamodzi ndi zamoyo zonse zazimuna ndi zazikazi, 16monga Mulungu adaalamulira. Pomwepo Chauta adatseka pa khomo.
17Chigumula chidagundika masiku makumi anai pa dziko lapansi. Madzi adayamba kukwera pa dziko lapansi, ndipo chombo chidayamba kuyandama. 18Madziwo adanka nakwererakwerera, ndipo chombocho chidayandama pa madzi. 19Kukwera kwa madzi kudapitirira ndithu mpaka kumiza ndi mapiri aatali omwe. 20Tsono adakwererakwerera ndithu mpaka kubzola nsonga za mapiriwo mamita asanu ndi aŵiri. 21Zamoyo zonse zokhala pa dziko lapansi zidafa, monga mbalame, zoŵeta, nyama zakuthengo, mtindiri wa tizilombo tosiyanasiyana, ndi anthu onse. 22Zamoyo zonse za pa dziko lapansi zidafa. 23Chauta adaononga zamoyo zonse za pa dziko: anthu, nyama, zokwaŵa ndi mbalame. Nowa yekha adapulumuka pamodzi ndi onse amene anali naye m'chombomo. 24Madziwo adakhala osaphwa konse pa dziko lapansi masiku 150.
Currently Selected:
Gen. 7: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi

: