1
YOHANE 10:10
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga. Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wochuluka.
Lee anya n'etiti ihe abụọ
Nyochaa YOHANE 10:10
2
YOHANE 10:11
Ine ndine Mbusa Wabwino; mbusa wabwino ataya moyo wake chifukwa cha nkhosa.
Nyochaa YOHANE 10:11
3
YOHANE 10:27
Nkhosa zanga zimva mau anga, ndipo Ine ndizizindikira, ndipo zinditsata Ine.
Nyochaa YOHANE 10:27
4
YOHANE 10:28
Ndipo Ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzaonongeka kunthawi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m'dzanja langa.
Nyochaa YOHANE 10:28
5
YOHANE 10:9
Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulumutsidwa, nadzalowa, nadzatuluka, nadzapeza busa.
Nyochaa YOHANE 10:9
6
YOHANE 10:14
Ine ndiye Mbusa Wabwino; ndipo ndizindikira zanga, ndi zanga zindizindikira Ine
Nyochaa YOHANE 10:14
7
YOHANE 10:29-30
Atate wanga, amene anandipatsa izo, ali wamkulu ndi onse; ndipo palibe wina ngathe kuzikwatula m'dzanja la Atate. Ine ndi Atate ndife amodzi.
Nyochaa YOHANE 10:29-30
8
YOHANE 10:15
monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosa.
Nyochaa YOHANE 10:15
9
YOHANE 10:18
Palibe wina andichotsera uwu, koma ndiutaya Ine ndekha. Ndili nayo mphamvu yakuutaya, ndi mphamvu ndili nayo yakuutenganso; lamulo ili ndinalandira kwa Atate wanga.
Nyochaa YOHANE 10:18
10
YOHANE 10:7
Chifukwa chake Yesu ananenanso nao, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ine ndine khomo la nkhosa.
Nyochaa YOHANE 10:7
11
YOHANE 10:12
Wolipidwa amene sakhala mbusa, amene nkhosa sizili zake za yekha, aona mmbulu ulinkudza, nasiya nkhosazo, nathawa; ndipo mmbulu uzikwatula, nuzibalalitsa
Nyochaa YOHANE 10:12
12
YOHANE 10:1
Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wosalowa m'khola la nkhosa pakhomo, koma akwerera kwina, iyeyu ndiye wakuba ndi wolanda.
Nyochaa YOHANE 10:1
Ebe Mmepe Nke Mbụ Nke Ngwá
Akwụkwọ Nsọ
Atụmatụ Ihe Ogụgụ Gasị
Vidiyo Gasị