1
GENESIS 3:6
Buku Lopatulika
Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso, mtengo wolakalakika wopatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene anali naye, nadya iyenso.
比較
GENESIS 3:6で検索
2
GENESIS 3:1
Ndipo njoka inali yochenjera yoposa zamoyo zonse za m'thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu. Ndipo inati kwa mkaziyo, Eya! Kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m'mundamu?
GENESIS 3:1で検索
3
GENESIS 3:15
ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.
GENESIS 3:15で検索
4
GENESIS 3:16
Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.
GENESIS 3:16で検索
5
GENESIS 3:19
m'thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m'menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.
GENESIS 3:19で検索
6
GENESIS 3:17
Kwa Adamu ndipo anati, Chifukwa kuti wamvera mau a mkazi wako, nudya za mtengo umene ndinakuuza iwe kuti, Usadyeko; nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; m'kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako
GENESIS 3:17で検索
7
GENESIS 3:11
Ndipo anati, Ndani anakuuza iwe kuti uli wamaliseche? Kodi wadya za mtengo uja, umene ndinakuuza iwe kuti usadye?
GENESIS 3:11で検索
8
GENESIS 3:24
Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika akerubi cha kum'mawa kwake kwa munda wa Edeni, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.
GENESIS 3:24で検索
9
GENESIS 3:20
Ndipo mwamuna anamutcha dzina la mkazi wake, Heva; chifukwa ndiye amake wa amoyo onse.
GENESIS 3:20で検索
ホーム
聖書
読書プラン
ビデオ