1
GENESIS 9:12-13
Buku Lopatulika
Ndipo anati Mulungu, Ichi ndi chizindikiro cha pangano limene ndipangana ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, ku mibadwomibadwo; ndiika utawaleza wanga m'mtambomo, ndipo udzakhala chizindikiro cha pangano lopangana ndi Ine ndi dziko lapansi.
比較
GENESIS 9:12-13で検索
2
GENESIS 9:16
Ndipo utawo udzakhala m'mtambo; ndipo ndidzauyang'anira kuti ndikumbukire pangano lachikhalire lili ndi Mulungu ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo padziko lapansi.
GENESIS 9:16で検索
3
GENESIS 9:6
Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m'chifanizo cha Mulungu Iye anampanga munthu.
GENESIS 9:6で検索
4
GENESIS 9:1
Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.
GENESIS 9:1で検索
5
GENESIS 9:3
Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo.
GENESIS 9:3で検索
6
GENESIS 9:2
Kuopsa kwanu, ndi kuchititsa mantha kwanu kudzakhala pa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi pa zouluka zonse za m'mlengalenga, ndi pa zonse zokwawa pansi, ndi pansomba zonse za m'nyanja, zapatsidwa m'dzanja lanu.
GENESIS 9:2で検索
7
GENESIS 9:7
Ndi inu, mubalane, muchuluke; muswane padziko lapansi, nimuchuluke m'menemo.
GENESIS 9:7で検索
ホーム
聖書
読書プラン
ビデオ