Gen. 8

8
Kutha kwa chigumula
1Tsono Mulungu adakumbukira Nowa pamodzi ndi nyama zonse zakuthengo ndi zoŵeta zimene zinali naye m'chombomo. Adalamula mphepo kuti iwombe pa dziko lapansi, pomwepo madzi adayamba kutsika. 2Akasupe a madzi ambiri okhala pansi pa dziko pamodzi ndi zipata zakuthambo, adazitseka. Mvula adailetsa, 3ndipo madzi adayamba kutsika pang'onopang'ono. Masiku 150 atapita, madziwo anali atatsika ndithu, 4ndipo pa tsiku la 17, mwezi wachisanu ndi chiŵiri, chombocho chidakaima pamwamba pa phiri la Ararati. 5Madziwo adanka natsikabe, ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wakhumi, nsonga za mapiri zidayamba kuwoneka.
6Patapita masiku makumi anai, Nowa adatsekula zenera, 7natulutsa khwangwala. Khwangwalayo ankangouluka mu mlengalenga kudikira kuti madzi aphwe pa dziko lapansi. 8Tsono Nowa adatulutsa nkhunda kuti ikaone ngati madzi aphwa. 9Koma popeza kuti madzi anali akadalipobe pa dziko lonse, nkhundayo idabwerera, chifukwa idaasoŵa potera. Nowa adatambalitsa dzanja kunja, nailoŵetsanso m'chombo muja. 10Atadikira masiku asanu ndi aŵiri ena, adaitulutsanso nkhunda ija m'chombo. 11Madzulo idabwerako, ndipo Nowa adaona kuti kukamwa kwake kuli tsamba laliŵisi la mtengo wa olivi. Apo Nowa adadziŵa kuti madzi ayamba kuphwa. 12Pambuyo pake Nowa atadikiranso masiku ena asanu ndi aŵiri, adaitulutsanso nkhunda ija, koma nkhundayo sidabwererenso.
13Nowa ali wa zaka 601, pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, madzi adaphweratu pa dziko lapansi. Nowa adatsekula zenera la chombo chija nayang'ana kunja, nkuwona kuti pansi pauma, 14Pa tsiku la 27 mwezi wachiŵiri, dziko lonse lapansi linali litauma kotheratu.
Nowa atuluka m'chombo
15Mulungu adauza Nowa kuti, 16“Iwe ndi mkazi wako, ana ako pamodzi ndi akazi ao, tulukani m'chombomo. 17Tulutsa zamoyo zonse zili ndi iwezo, mbalame, nyama ndi zokwaŵa, kuti ziswane ndi kubalalika pa dziko lonse lapansi.” 18Motero Nowa adatuluka m'chombo, iye ndi mkazi wake ndiponso ana ake ndi akazi ao. 19Nyama zonse, zokwaŵa zonse, mbalame zonse, ndi zina zonse zoyenda pansi pano zidatuluka m'chombomo m'magulumagulu potsata mitundu yake.
Nowa apereka nsembe
20Pamenepo Nowa adamanga guwa kumangira Chauta. Adatengako mtundu uliwonse wa nyama ndi mbalame zimene anthu amaperekera nsembe, ndipo adazipha, napereka nsembe zopsereza paguwapo. 21Chauta atamva fungo lokomalo, adati, “Sindidzatembereranso dziko chifukwa cha zochita za anthu, chifukwa ndikudziŵa maganizo a munthu kuti ndi oipa kuyambira ali mwana. Sindidzaononganso zamoyo zonse monga ndachitiramu.
22“Nthaŵi zonse m'mene dziko lapansi lidzakhalire,
padzakhala nyengo yobzala ndi nyengo yokolola.
Padzakhala nyengo yachisanu ndi nyengo yotentha,
nyengo yachilimwe ndi nyengo yadzinja,
ndipo usana ndi usiku zidzakhalapo kosalekeza.”

Šiuo metu pasirinkta:

Gen. 8: BLY-DC

Paryškinti

Dalintis

Kopijuoti

None

Norite, kad paryškinimai būtų įrašyti visuose jūsų įrenginiuose? Prisijunkite arba registruokitės